bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
/
2 Kings 21
2 Kings 21
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
← Chapter 20
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 22 →
1
Manase anali wa zaka khumi ndi ziwiri polowa iye ufumu wace, nakhala mfumu zaka makumi asanu ndi zisanu m'Yerusalemu; ndi dzina la mace ndiye Hefisiba.
2
Ndipo anacita coipa pamaso pa Yehova, monga mwa zonyansa za amitundu amene Yehova anawaingitsa pamaso pa ana a Israyeli.
3
Pakuti anamanganso misanje, imene Hezekiya atate wace adaiononga; nautsira Baala maguwa a nsembe, nasema cifanizo, monga anacita Ahabu mfumu ya Israyeli, nagwadira khamu lonse la kuthambo, nalitumikira.
4
Namanga iye maguwa a nsembe m'nyumba ya Yehova imene Yehova adainenera kuti, M'Yerusalemu ndidzaika dzina langa.
5
Nalimangira khamu lonse la kuthambo maguwa a nsembe m'mabwalo awiri a nyumba ya Yehova.
6
Napititsa mwana wace pamoto, naombeza maula, nacita zanyanga, naika obwebweta ndi openda; anacita zoipa zambiri pamaso pa Yehova kuutsa mkwiyo wace.
7
Ndipo anaika cifanizo cosema cimene adacipanga m'nyumba ija Yehova adainenera kwa Davide ndi kwa Solomo mwana wace kuti, M'nyumba muno ndi m'Yerusalemu umene ndausankha mwa mafuko onse a Israyeli ndidzaikamo dzina langa kosatha.
8
Ndipo sindidzacotsanso mapazi a Israyeli m'dziko ndidalipereka kwa makolo ao; cokhaci asamalire kucita monga mwa zonse ndawalamulira ndi monga mwa cilamulo conse anawalamulira Mose mtumiki wanga.
9
Koma sanamvera, nawalakwitsa Manase, nawacititsa coipa, kuposa amitundu amene Yehova adawaononga pamaso pa ana a Israyeli.
10
Pamenepo Yehova ananena mwa atumiki ace aneneri, ndi kuti,
11
Popeza Manase mfumu ya Yuda anacita zonyansa izi, pakuti zoipa zace zinaposa zonse adazicita Aamori, amene analipo asanabadwe iye, nalakwitsanso Yuda ndi mafano ace;
12
cifukwa cace atero Yehova Mulungu wa Israyeli, Taonani, nditengera Yerusalemu ndi Yuda coipa, cakuti yense acimvera cidzamliritsa mwini khutu.
13
Ndipo ndidzayesa pa Yerusalemu cingwe coongolera ca Samariya, ndi cingwe colungamitsira ciriri ca nyumba ya Ahabu; ndidzapukuta Yerusalemu monga umo apukutira mbale, kuipukuta ndi kuibvundikira.
14
Ndipo ndidzataya cotsala ca colowa canga, ndi kuwapereka m'dzanja la adani ao, nadzakhala iwo cakudya ndi cofunkha ca adani ao onse;
15
popeza anacita coipa pamaso panga, nautsa mkwiyo wanga citurukire makolo ao m'Aigupto, mpaka lero lino.
16
Ndiponso Manase anakhetsa mwazi wambiri wosacimwa mpaka anadzaza m'Yerusalemu monsemo, osawerenga kulakwa kwace analakwitsa nako Yuda, ndi kucita coipa pamaso pa Yehova.
17
Macitidwe ena tsono a Manase, ndi zonse anazicita, sizilembedwa kodi m'buku la macitidwe a mafumu a Yuda?
18
Nagona Manase ndi makolo ace, naikidwa m'munda wa nyumba yace, m'munda wa Uza, nakhala mfumu m'malo mwace Amoni mwana wace.
19
Amoni anali wa zaka makumi awiri mphambu ziwiri polowa iye ufumu wace, nakhala mfumu zaka ziwiri m'Yerusalemu; ndi dzina la mace ndiye Mesulemeti mwana wa Haruzi wa ku Yotiba.
20
Nacita iye coipa pamaso pa Yehova, monga umo amacitira Manase atate wace.
21
Nayenda iye m'njira monse anayendamo atate wace, natumikira mafano anawatumikira atate wace, nawagwadira;
22
nasiya Yehova Mulungu wa makolo ace, sanayenda m'njira ya Yehova.
23
Ndipo anyamata ace a Amoni anamcitira ciwembu, napha mfumuyo m'nyumba yace yace.
24
Koma anthu a m'dzikomo anapha onse akumcitira ciwembu mfumu Amoni; ndipo anthu a m'dzikomo anamlonga ufumu Yosiya mwana wace m'malo mwace.
25
Macitidwe ena tsono a Amoni adawacita, salembedwa kodi m'buku la macitidwe a mafumu a Yuda?
26
Naikidwa iye m'manda mwace m'munda wa Uza; nakhalamfumum'malo mwace Yosiya mwana wace.
← Chapter 20
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 22 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25