bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
/
Jonah 2
Jonah 2
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
← Chapter 1
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 3 →
1
Pamenepo Yona anapemphera kwa Yehova Mulungu wace ali m'mimba mwa nsombayo.
2
Ndipo anati, Ndinaitana Yehova m'nsautso yanga, Ndipo anandiyankha ine; Ndinapfuula ndiri m'mimba ya manda, Ndipo munamva mau anga.
3
Pakuti munandiponya mwakuya m'kati mwa nyanja, Ndipo madzi anandizinga; Mapfunde anu onse a nyondonyondo anandimiza.
4
Ndipo ndinati, Ndatayika ndicoke pamaso panu; Koma ndidzapenyanso Kacisi wanu wopatulika.
5
Madzi anandizinga mpaka moyo wanga, Madzi akuya anandizungulira, Kayandeyande wa m'nyanja anandikulunga mutu.
6
Ndinatsikira ku matsinde a mapiri, Mipingiridzo ya dziko inanditsekereza kosatha; Koma munandikwezera moyo wanga kuucotsa kucionongeko, Yehova Mulungu wanga.
7
Pokomoka moyo wanga m'kati mwanga ndinakumbukila Yehova; Ndi pemphero langa linafikira Inu m'Kacisi wanu wopatulika.
8
Iwo osamalira mabodza opanda pace Ataya cifundo cao cao.
9
Koma ine ndidzakupherani Inu nsembe ndi mau akuyamika, Ndidzakwaniritsacowindacanga. Cipulumutso nca Yehova.
10
Pamenepo Yehova analankhula ndi nsombayo, ndipo inamsanzira Yona kumtunda.
← Chapter 1
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 3 →
All chapters:
1
2
3
4