bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
/
Jonah 3
Jonah 3
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
← Chapter 2
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 4 →
1
Ndipo mau a Yehova anadza kwa Yona nthawi yaciwiri, ndi kuti,
2
Nyamuka, pita ku Nineve mudzi waukuru uja, nuulalikire uthenga umene ndikuuza.
3
Ndipo Yona ananyamuka, napita ku Nineve, monga mwa mau a Yehova. Koma Nineve ndiwo mudzi waukuru pamaso pa Yehova, wa ulendo wa masiku atatu.
4
Ndipo Yona anayamba kulowa mudziwo ulendo wa tsiku limodzi, nalalikira, nati, Atsala masiku makumi anai ndipo Nineve adzapasuka.
5
Ndipo anthu a Nineve anakhulupirira Mulungu, nalalikira cosala, nabvala ciguduli, kuyambira wamkuru kufikira wamng'ono wa iwowa.
6
Pakuti mau awa anafikira mfumu ya Nineve, ndipo Inanyamuka ku mpando wace wacifumu, nibvula copfunda cace, nipfunda ciguduli, nikhala m'mapulusa.
7
Ndipo analalikira, nanena m'Nineve mwa lamulo la mfumu ndi nduna zace, ndi kuti, Ngakhale munthu kapena nyama, ngakhale ng'ombe kapena nkhosa, zisalawe kanthu, zisadye, zisamwe madzi;
8
koma zipfundidwe ndi ciguduli munthu ndi nyama, nizipfuulire kolimba kwa Mulungu; ndipo abwere yense kuleka njira yace yoipa, ndi ciwawa ciri m'manja mwace.
9
Kaya, akatembenuka Mulungu, ndi kuleka kubwera ku mkwiyo wace waukali, kuti tisatayike,
10
Ndipo Mulungu anaona nchito zao, kuti anabwera kuleka njira yao yoipa; ndipo Mulungu analeka coipa adanenaci kuti adzawacitira, osacicita.
← Chapter 2
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 4 →
All chapters:
1
2
3
4