bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
/
Leviticus 24
Leviticus 24
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
← Chapter 23
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 25 →
1
Ndipo Yehova ananena ndi Mose, ndi kuti,
2
Uza ana a Israyeli, kuti akutengere mafuta a azitona oyera opera akuunikira, kuti aziwalitsa nyali nthawi zonse.
3
Aroni aikonze kunja kwa nsaru yocinga ya mboni, m'cihema cokomanako, kuyambira madzulo kufikira m'mawa, pamaso pa Yehova nthawi zonse; likhale lemba losatha mwa mibadwo yanu.
4
Akonze nyalizo pa coikapo nyali coona pamaso pa Yehova nthawi zonse.
5
Ndipo uzitenga ufa wosalala, ndi kuphika timitanda khumi ndi tiwiri; awiri a magawo khumi a efa afikane kamtanda kamodzi,
6
Ndipo utiike m'mizere iwiri, tisanu ndi kamodzi mzere umodzi, pa gome loyera, pamaso pa Yehova.
7
Nuike libano loona ku mzere uli wonse, kuti likhale kumkate ngati cokumbutsa, nsembe yamoto ya Yehova.
8
Nthawi zonse tsiku la Sabata aukonze pamaso pa Yehova, cifukwa ca ana a Israyeli, ndilo pangano losatha.
9
Ndipo ukhale wa Aroni ndi ana ace, audye pamalo popatulika; pakuti auyese wopatulikitsa wocokera ku nsembe zamoto za Yehova; ndilo lemba losatha.
10
Ndipo mwana wamwamuna wa mkazi M-israyeli, atate wace ndiye M-aigupto, anaturuka mwa ana a Israyeli; ndi mwana wamwamuna wa mkazi M-israyeliyo analimbana naye munthu M-israyeli kucigono;
11
ndipo mwana wamwamuna wa mkazi M-israyeli anacitira DZINA mwano, natemberera; ndipo anadza naye kwa Mose. Dzina la mai wace ndiye Selomiti, mwana wa Dibri, wa pfuko la Dani.
12
Ndipo anamsunga m'kaidi, kuti awafotokozere m'mene anenere Yehova.
13
Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,
14
Turuka naye wotembererayo kunja kwa cigono; ndipo onse adamumva aike manja ao pamutu pace, ndi khamu lonse limponye miyala afe.
15
Ndipo unene ndi ana a Israyeli, ndi kuti, Ali yense wotemberera Mulungu wace azisenza kucimwa kwace.
16
Ndi iye wakucitira mwano dzina la Yehova, amuphe ndithu; khamu lonse limponye miyala ndithu; mlendo ndi wobadwa m'dziko yemwe akacitira dzina la Yehova mwano, awaphe.
17
Munthu akakantha munthu mnzace ali yense kuti afe, amuphe ndithu.
18
Munthu akakantha nyama kuti ife, ambwezere yina; moyo kulipa moyo.
19
Munthu akacititsa mnansi wace cirema, monga umo anacitira momwemo amcitire iye;
20
kutyola kulipa kutyola, diso kulipa diso, dzino kulipa dzino; monga umo anacitira munthu cirema, momwemo amcitire iye.
21
Iye wakukantha nyama kuti ife, ambwezere yina; iye wakupha munthu, amuphe.
22
Ciweruzo canu cifanefane ndi mlendo ndi wobadwa m'dziko; pakuti Ine ndine Yehova Mulungu wanu.
23
Ndipo Mose ananena ndi ana a Israyeli, ndipo anaturutsa wotembererayo kunja kwa cigono, namponya miyala. Ndipo ana a Israyeli anacita monga Yehova adauza Mose.
← Chapter 23
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 25 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27