bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
/
Leviticus 3
Leviticus 3
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
← Chapter 2
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 4 →
1
Ndipo copereka cace cikakhala nsembe yoyamika; akabwera nayo ng'ombe, kapena yaimuna kapena yaikazi, azibwera nayo yopanda cirema pamaso pa Yehova.
2
Ndipo aike dzanja lace pa mutu wa copereka cace, ndi kuipha pa cipata ca cihema cokomanako; ndipo ana a Aroni, ansembewo, awaze mwazi wace pa guwa la nsembe pozungulira.
3
Pamenepo abwere nayo nsembe yamoto ya kwa Yehova, yotengako ku nsembe yoyamika; acotse mafuta akukuta matumbo, ndi mafuta onse akukhala pamatumbo,
4
ndi imso ziwiri, ndi mafuta ali pomwepo okhala m'cuuno, ndi cokuta ca mphafa cofikira kuimso.
5
Ndipo ana a Aroni azitenthe pa guwa la nsembe, pa nsembe yopsereza, iri pa nkhuni zimene ziri pamoto; ndiyo nsembe yamoto, ya pfungo lokoma la kwa Yehova.
6
Ndipo copereka cace cikakhala nkhosa kapena mbuzi, kuti ikhale nsembe yoyamika ya kwa Yehova; ingakhale yaimuna kapena yaikazi, azibwera nayo yopanda cirema;
7
akabwera nayo nkhosa kuti ikhale copereka cace, abwere nayo pamaso pa Yehova;
8
naike dzanja lace pamutu pa copereka cace, naiphe patsogolo pa cihema cokomanako; ndipo ana a Aroni awaze mwazi wace pa guwa la nsembe pozungulira.
9
Pamenepo abwere nayo nsembe yamoto ya kwa Yehova; yotengako ku nsembe yoyamika; mafuta ace, mcira wamafuta wonse, ataucotsa kufupi ku pfupa lao msana; naicotse mafuta akukuta matumbo, ndi mafuta onse akukhala pamatumbo,
10
ndi imso ziwiri, ndi mafuta ali pomwepo, okhala m'cuuno, ndi cokuta ca mphafa cofikira kuimso.
11
Ndipo wansembe azitenthe pa guwa la nsembe; ndico cakudya ca nsembe yamoto ya kwa Mulungu.
12
Ndipo copereka cace cikakhala mbuzi, azibwera nayo pamaso pa Yehova;
13
naike dzanja lace pamutu pace, naiphe pa khomo la cihema cokomanako; ndipo ana a Aroni awaze mwazi wace pa guwa la nsembe pozungulira.
14
Ndipo abwere naco copereka cace cotengako, ndico nsembe yamoto ya kwa Yehova; acotse mafuta akukuta matumbo, ndi mafuta onse akukhala pamatumbo,
15
ndi imso ziwiri, ndi mafuta ali pomwepo, okhala m'cuuno, ndi cokuta ca mphafa cofikira kuimso.
16
Ndipo wansembe atenthe izi pa guwa la nsembe; ndizo cakudya ca nsembe yamoto icite pfungo lokoma; mafuta onse nga Yehova.
17
Likhale lemba losatha m'mibadwo yanu m'nyumba zanu zonse, musamadya kapena mafuta kapena mwazi.
← Chapter 2
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 4 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27