bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
/
Micah 2
Micah 2
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
← Chapter 1
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 3 →
1
Tsoka iwo akulingirira cinyengo, ndi kukonza coipa pakama pao! kutaca m'mawa acicita, popeza cikhozeka m'manja mwao.
2
Ndipo akhumbira minda, nailanda; ngakhale nyumba, nazicotsa; asautsa mwamuna ndi nyumba yace, inde munthu ndi colowa cace.
3
Cifukwa cace atero Yehova, Taonani, ndilingirira coipa pa banja ili, cimene simudzacotsako makosi anu, kapena kuyenda modzikuza inu; Pakuti nyengo iyi ndi yoipa.
4
Tsiku ilo adzanena fanizo lakunena inu, nadzalira maliro olemerera, ndi kuti, Tapasuka konse; iye asintha gawo la anthu anga; ha! andicotsera ili! agawira opikisana minda yathu.
5
Cifukwa cace udzasowa woponya cingwe camaere m'msonkhano wa Yehova.
6
Musamanenera, amanenera ati. Sadzanenera kwa awa; matonzo sadzacoka.
7
Kodi adzati, Nyumba ya Yakobo iwe, Mzimu wa Yehova waperewera kodi? izi ndi nchito zace kodi? Mau anga samcitira zokoma kodi, iye amene ayenda coongoka?
8
Koma ngakhale dzulo anthu anga anauka ngati mdani; mukwatula copfunda ku maraya a iwo opitirira mosatekeseka, ngati anthu osafuna nkhondo.
9
Muwataya akazi a anthu anga kunja kwa nyumba zao zokondweretsa; mucotsa ulemerero wanga kwa ana ao kosatha.
10
Nyamukani, cokani, pakuti popumula panu si pano ai; cifukwa ca udio Wakuononga ndi cionongeko cacikuru.
11
Munthu akayenda ndi mtima wacinyengo ndi kunama, ndi kuti, Ndidzanenera kwa iwe za vinyo ndi cakumwa cakuledzeretsa; iye ndiye mneneri wa anthu ace.
12
Ndidzakumemezani ndithu, Yakobo, inu nonse; ndidzasonkhanitsa ndithu otsala a Israyeli; ndidzawaika pamodzi ngati nkhosa za ku Boma; ngati zoweta pakati pa busa pao adzacita phokoso cifukwa ca kucuruka anthu.
13
Wotyola wakwera pamaso pao; iwo anatyola, napita kucipata, naturuka pomwepo; ndi mfumu yao yapita pamaso pao, ndipo Yehova awatsogolera.
← Chapter 1
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 3 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7