bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
/
Micah 5
Micah 5
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
← Chapter 4
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 6 →
1
Uzisonkhana tsopano magulu magulu, mwana wamkazi wa magulu iwe; watimangira misasa, adzapanda woweruza wa Israyeli ndi ndodo patsaya.
2
Koma iwe, Betelehemu Efrata, ndiwe wamng'ono kuti ukhale mwa zikwi za Yuda, mwa iwe mudzanditurukira wina wakudzakhala woweruza m'Israyeli; maturukiro ace ndiwo a kale lomwe, kuyambira nthawi yosayamba.
3
Cifukwa cace Iye adzawapereka kufikira nthawi yoti wobalayo wabala; pamenepo otsala a abale ace adzabwera pamodzi ndi ana a Israyeli,
4
Ndipo adzaimirira, nadzadyetsa nkhosa zace mu mphamvu ya Yehova, m'ukulu wa dzina la Yehova Mulungu wace; ndipo iwo adzakhalabe; pakuti pamenepo Iye adzakhala wamkuru kufikira malekezero a dziko lapansi.
5
Ndipo ameneyo adzakhala Mtendere; pamene a ku Asuri adzalowa m'dziko lathu, ndi pamene adzaponda m'zinyumba zathu, tidzawaukitsira abusa asanu ndi awiri, ndi akalonga asanu ndi atatu.
6
Ndipo iwo adzatha dziko la Asuri ndi lupanga, ndi dziko la Nimrodi, ndilo polowera pace; ndipo adzatilanditsa kwa a ku Asuri pamene alowa m'dziko lathu, pamene aponda m'kati mwa malire athu.
7
Ndipo otsala a Yakobo adzakhala pakati pa mitundu yambiri ya anthu, ngati mame ocokera kwa Yehova, ngati mvula paudzu, yosacedwera munthu, yosalindira ana a anthu.
8
Ndipo, otsala a Yakobo adzakhala mwa amitundu, pakati pa mitundu yambiri ya anthu, ngati mkango mwa nyama za kuthengo, ngati msona wa mkango mwa magulu a nkhosa; umenewo ukapitako, upondereza, numwetula, ndipo palibe wakupulumutsa.
9
Dzanja lako likwezeke pamwamba pa iwo akuyambana nawe, ndi adani ako onse aonongeke.
10
Ndipo kudzacitika tsiku ilo, ati Yehova, ndidzaononga akavalo ako m'kati mwako, ndi kutha magareta ako;
11
ndipo ndidzaononga midzi ya m'dziko lako, ndi kupasula malinga ako onse;
12
ndipo ndidzaononga zanyanga za m'dzanja lako; ndipo sudzakhalanso nao alosi;
13
ndidzaononganso mafano ako osema, ndi zoimiritsa zako pakati pako; ndipo sudzalambiranso nchito za manja ako.
14
Ndipo ndidzazula zifanizo zako m'kati mwako, ndi kutha midzi yako.
15
Ndipo ndidzabwezera amitundu osamvera cilango mu mkwiyo waukali.
← Chapter 4
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 6 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7