bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
/
Psalms 119
Psalms 119
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
← Chapter 118
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 51
Chapter 52
Chapter 53
Chapter 54
Chapter 55
Chapter 56
Chapter 57
Chapter 58
Chapter 59
Chapter 60
Chapter 61
Chapter 62
Chapter 63
Chapter 64
Chapter 65
Chapter 66
Chapter 67
Chapter 68
Chapter 69
Chapter 70
Chapter 71
Chapter 72
Chapter 73
Chapter 74
Chapter 75
Chapter 76
Chapter 77
Chapter 78
Chapter 79
Chapter 80
Chapter 81
Chapter 82
Chapter 83
Chapter 84
Chapter 85
Chapter 86
Chapter 87
Chapter 88
Chapter 89
Chapter 90
Chapter 91
Chapter 92
Chapter 93
Chapter 94
Chapter 95
Chapter 96
Chapter 97
Chapter 98
Chapter 99
Chapter 100
Chapter 101
Chapter 102
Chapter 103
Chapter 104
Chapter 105
Chapter 106
Chapter 107
Chapter 108
Chapter 109
Chapter 110
Chapter 111
Chapter 112
Chapter 113
Chapter 114
Chapter 115
Chapter 116
Chapter 117
Chapter 118
Chapter 119
Chapter 120
Chapter 121
Chapter 122
Chapter 123
Chapter 124
Chapter 125
Chapter 126
Chapter 127
Chapter 128
Chapter 129
Chapter 130
Chapter 131
Chapter 132
Chapter 133
Chapter 134
Chapter 135
Chapter 136
Chapter 137
Chapter 138
Chapter 139
Chapter 140
Chapter 141
Chapter 142
Chapter 143
Chapter 144
Chapter 145
Chapter 146
Chapter 147
Chapter 148
Chapter 149
Chapter 150
Chapter 120 →
1
Odala angwiro m'mayendedwe ao, Akuyenda m'cilamulo ca Yehova.
2
Odala iwo akusunga mboni zace, Akumfuna ndi mtima wonse;
3
Inde, sacita cosalungama; Ayenda m'njira zace.
4
Inu munatilamulira. Tisamalire malangizo anu ndi cangu,
5
Ha! mwenzi zitakhazikika njira zanga Kuti ndisamalire malemba anu.
6
Pamenepo sindidzacita manyazi, Pakupenyerera malamulo anu onse.
7
Ndidzakuyanrikani ndi mtima woongoka, Pakuphunzira maweruzo anu olungama.
8
Ndidzasamalira malemba anu: Musandisiye ndithu.
9
Mnyamata adzayeretsa mayendedwe ace bwanji? Akawasamalira monga mwa mau anu.
10
Ndinakufunani ndi mtima wanga wonse; Ndisasokere kusiyana nao malamulo anu.
11
Ndinawabisa mau anu mumtima mwanga, Kuti ndisalakwire Inu.
12
Inu ndinu wodala Yehova; Ndiphunzitseni malemba anu.
13
Ndinafotokozera ndi milomo yanga Maweruzo onse a pakamwa panu,
14
Ndinakondwera m'njira ya mboni zanu, Koposa ndi cuma conse,
15
Ndidzalingirira pa malangizo anu, Ndi kupenyerera mayendedwe anu.
16
Ndidzadzikondweretsa nao malemba anu; Sindidzaiwala mau anu,
17
Mucitire cokoma mtumiki wanu kuti ndikhale ndi moyo; Ndipo ndidzasamalira mau anu.
18
Munditsegulire maso, kuti ndipenye Zodabwiza za m'cilamulo canu.
19
Ine ndine mlendo pa dziko lapansi; Musandibisire malamulo anu.
20
Mtima wanga wasweka ndi kukhumba Maweruzo anu nyengo zonse.
21
Munadzudzula odzikuza otembereredwa, Iwo akusokera kusiyana nao malamulo anu.
22
Mundicotsere cotonza, ndi cimpepulo; Pakuti ndinasunga mboni zanu.
23
Nduna zomwe zinakhala zondineneza; Koma mtumiki wanu analingirira malemba anu.
24
Mboni zanu zomwe ndizo zondikondwetsa, Ndizo zondipangira nzeru.
25
Moyo wanga umamatika ndi pfumbi; Mundipatse moyo monga mwa mau anu.
26
Ndinafotokozera njira zanga, ndipo munandiyankha: Mundiphunzitse malemba anu.
27
Mundizindikiritse njira ya malangizo anu; Kuti ndilingalire zodabwiza zanu.
28
Moyo wanga wasungunuka ndi cisoni: Mundilimbitse monga mwa mau anu.
29
Mundicotsere njira ya cinyengo; Nimundipatse mwacifundo cilamulo canu.
30
Ndinasankha njira yokhulupirika; Ndinaika maweruzo anu pamaso, panga,
31
Ndimamatika nazo mboni zanu; Musandicititse manyazi, Yehova.
32
Ndidzathamangira njira ya malamulo anu, Mutakulitsa mtima wanga.
33
Mundiphunzitse, Yehova, njira ya malemba anu; Ndidzaisunga kufikira kutha kwace.
34
Mundizindikiritse, ndipo ndidzasunga malamulo anu; Ndidzawasamalira ndi mtima wanga wonse.
35
Mundiyendetse mopita malamulo anu; Pakuti ndikondwera m'menemo.
36
Lingitsani mtima wanga ku mboni zanu, Si ku cisiriro ai.
37
Mucititse mlubza maso anga ndisapenye zacabe, Mundipatse moyo mu njira yanu.
38
Limbitsirani mtumiki wanu mau anu, Ndiye wodzipereka kukuopani.
39
Mundipatutsire cotonza canga ndiciopaco; Popeza maweruzo anu ndi okoma.
40
Taonani, ndinalira malangizo anu; Mundipatse moyo mwa cilungamo canu.
41
Ndipo cifundo canu cindidzere, Yehova, Ndi cipulumutso canu, monga mwa mau anu.
42
Kuti ndikhale nao mau akuyankha wonditonza; Popeza ndikhulupirira mau anu.
43
Ndipo musandicotsere ndithu mau a coonadi pakamwa panga; Pakuti ndinayembekeza maweruzo anu.
44
Potero ndidzasamalira malamulo anu cisamalire Ku nthawi za nthawi.
45
Ndipo ndidzayenda mwaufulu; Popeza ndinafuna malangizo anu.
46
Ndidzalankhulanso za umboni wanu pamaso pa mafumu, Osacitapo manyazi.
47
Ndipo ndidzadzikondweretsa nao malamulo anu, Amene ndiwakonda.
48
Ndidzakwezanso manja anga ku malamulo anu, amene ndiwakonda; Ndipo ndidzalingalira pa malemba anu.
49
Kumbukilani mau a kwa mtumiki wanu, Amene munandiyembekezetsa nao.
50
Citonthozo canga m'kuzunzika kwanga ndi ici; Pakuti mau anu anandipatsa moyo.
51
Odzikuza anandinyoza kwambiri: Koma sindinapatukanso naco cilamulo canu.
52
Ndinakumbukila maweruzo anu kuyambira kale, Yehova, Ndipo ndinadzitonthoza.
53
Ndinasumwa kwakukuru, Cifukwa ca oipa akusiya cilamulo canu.
54
Malemba anu anakhala nyimbo zanga M'nyumba ya ulendo wanga,
55
Usiku ndinakumbukila dzina lanu, Yehova, Ndipo ndinasamalira cilamulo canu.
56
Ici ndinali naco, Popeza ndinasunga malangizo anu.
57
Yehova ndiye gawo langa: Ndinati ndidzasunga mau anu.
58
Ndinapemba pankhope panu ndi mtima wanga wonse: Mundicitire cifundo monga mwa mau anu.
59
Ndinaganizira njira zanga, Ndipo ndinabweza mapazi anga atsate mboni zanu.
60
Ndinafulumira, osacedwa, Kusamalira malamulo anu.
61
Anandikulunga nazo zingwe za oipa; Koma sindinaiwala cilamulo canu.
62
Pakati pa usiku ndidzauka kukuyamikani Cifukwa ca maweruzo anu olungama.
63
Ine ndine wakuyanjana nao onse akukuopani, Ndi iwo akusamalira malangizo anu.
64
Dziko lapansi lidzala naco cifundo canu, Yehova; Mundiphunzitse malemba anu.
65
Munacitira mtumiki wanu cokoma, Yehova, Monga mwa mau anu.
66
Mundiphunzitse cisiyanitso ndi nzeru; Pakuti ndinakhulupirira malamulo anu.
67
Ndisanazunzidwe ndinasokera; Koma tsopano ndisamalira mau anu.
68
Inu ndinu wabwino, ndi wakucita zabwino; Mundiphunzitse malemba anu.
69
Odzikuza anandipangira bodza: Ndidzasunga malangizo anu ndi mtima wanga wonse.
70
Mtima wao unona ngati mafuta; Koma ine ndikondwera naco cilamulo canu.
71
Kundikomera kuti ndinazunzidwa; Kuti ndiphunzire malemba anu.
72
Cilamulo ca pakamwa panu cindikomera Koposa golidi ndi siliva zikwi zikwi.
73
Manja anu anandilenga nandiumba; Mundizindikiritse, kuti ndiphunzire malemba anu.
74
Iwo amene akuopani adzandiona ine nadzakondwera; Popeza ndayembekezera mau anu;
75
Ndidziwa kuti maweruzo anu ndiwo olungama, Yehova, Ndi kuti munandizunza ine mokhulupirika.
76
Cifundo canu cikhaletu cakunditonthoza, ndikupemphani, Monga mwa mau anu kwa mtumiki wanu.
77
Nsoni zokoma zanu zindidzere, kuti ndikhale ndi moyo; Popeza cilamulo canu cindikondweretsa.
78
Odzikuza acite manyazi, popeza anandicitira monyenga ndi bodza: Koma ine ndidzalingalira malangizo anu.
79
Iwo akuopa Inu abwere kwa ine, Ndipo adzadziwa mboni zanu.
80
Mtima wanga ukhale wangwiro m'malemba anu; Kuti ndisacite manyazi.
81
Moyo wanga unakomoka ndi kukhumba cipulumutso canu: Ndinayembekezera mau anu.
82
Maso anga anatha mphamvu ndi kukhumba mau anu, Ndikuti, Mudzanditonthoza liti?
83
Popeza ndakhala ngati thumba lofukirira; Koma sindiiwala malemba anu.
84
Masiku a mtumiki wanu ndiwo angati? Mudzaweruza liti iwo akundilondola koipa?
85
Odzikuza anandikumbira mbuna, Ndiwo osasamalira cilamulo canu.
86
Malamulo anu onse ngokhulupirika; Andilondola nalo bodza; ndithandizeni.
87
Akadandithera pa dziko lapansi; Koma ine sindinasiya malangizo anu.
88
Mundipatse moyo monga mwa cifundo canu; Ndipo ndidzasamalira mboni ya pakamwa panu,
89
Mau anu aikika kumwamba, Kosatha, Yehova.
90
Cikhulupiriko canu cifikira mibadwo mibadwo; Munakhazikitsa dziko lapansi, ndipo likhalitsa.
91
Kunena za maweruzo anu alimbikira kufikira lero; Pakuti onsewa ndiwo atumiki anu.
92
Cilamulo canu cikadapanda kukhala cikondweretso canga, Ndikadatayika m'kuzunzika kwanga.
93
Sindidzaiwala malangizo anu nthawi zonse; Popeza munandipatsa nao moyo.
94
Ine ndine wanu, ndipulumutseni Pakuti ndinafuna malangizo anu.
95
Oipa anandilalira kundiononga; Koma ndizindikira mboni zanu.
96
Ndinapenya malekezero ace a ungwiro wonse; Koma lamulo lanu ndi lotakasuka ndithu.
97
Ha! Ndikondadi cilamulo canu; Ndilingiriramo ine tsiku lonse.
98
Malamulo anu andipatsa nzeru yakuposa adani anga; Pakuti akhala nane cikhalire.
99
Ndiri nayo nzeru yakuposa aphunzitsi anga onse; Pakuti ndilingalira mboni zanu.
100
Ndizindikira koposa okalamba Popeza ndinasunga malangizo anu.
101
Ndinaletsa mapazi anga njira iri yonse yoipa, Kuti ndisamalire mau anu.
102
Sindinapatukana nao maweruzo anu; Pakuti Inu munandiphunzitsa.
103
Mau anu azunadi powalawa ine! Koposa uci m'kamwa mwanga.
104
Malangizo anu andizindikiritsa; Cifukwa cace ndidana nao mayendedwe onse acinyengo,
105
Mau anu ndiwo nyali ya ku mapazi anga, Ndi kuunika kwa panjira panga,
106
Ndinalumbira, ndipo ndinatsimikiza mtima, Kuti ndidzasamalira maweruzo anu olungama.
107
Ndazunzika kwambiri: Ndipatseni moyo, Yehova, monga mwa mau anu.
108
Landirani, Yehova, zopereka zaufulu za pakamwa panga, Ndipo ndiphunzitseni maweruzo anu.
109
Moyo wanga ukhala m'dzanja langa cikhalire; Koma sindiiwala cilamulo canu.
110
Oipa anandichera msampha; Koma sindinasokera m'malangizo anu.
111
Ndinalandira mboni zanu zikhale colandira cosatha; Pakuti ndizo zokondweretsa mtima wanga.
112
Ndinalingitsa mtima wanga ucite malemba anu, Kosatha, kufikira cimatiziro.
113
Ndidana nao a mitima iwiri; Koma ndikonda cilamulo canu.
114
Inu ndinu pobisalapo panga, ndi cikopa canga; Ndiyembekezera mau anu.
115
Mundicokere ocita zoipa inu; Kuti ndisunge malamulo a Mulungu wanga.
116
Mundicirikize monga mwa mau anu, kuti ndikhale ndi moyo; Ndipo ndisacite manyazi pa ciyembekezo canga.
117
Mundigwirizize ndipo ndidzapulumutsidwa, Ndipo ndidzasamalira malemba anu cisamalire.
118
Mupepulaonseakusokeram'malemba anu; Popeza cinyengo cao ndi bodza.
119
Mucotsa oipa onse a pa dziko lapansi ngati mphala: Cifukwa cace ndikonda mboni zanu.
120
Thupi langa linjenjemera ndi kuopa Inu; Ndipo ndicita mantha nao maweruzo anu.
121
Ndinacita ciweruzo ndi cilungamo; Musandisiyira akundisautsa.
122
Mumkhalire cikole mtumiki wanucimkomere; Odzikuza asandisautse.
123
Maso anga anatha mphamvu pafuna cipulumutso canu, Ndi mau a cilungamo canu.
124
Mucitire mtumiki wanu monga mwa cifundo canu, Ndipo ndiphunzitseni malemba anu,
125
Ine ndine mtumiki wanu, ndizindikiritseni; Kuti ndidziwe mboni zanu.
126
Yafika nyengo yakuti Yehova acite kanthu; Pakuti anaswa cilamulo canu.
127
Cifukwa cace ndikonda malamulo anu Koposa golidi, Inde golidi woyengeka,
128
Cifukwa cace ndiyesa ngolunjika malangizo anu onse akunena zonse; Koma ndidana nazo njira zonse zonyenga.
129
Mboni zanu nzodabwiza; Cifukwa cace moyo wanga uzisunga,
130
Potsegulira mau anu paunikira; Kuzindikiritsa opusa.
131
Ndinatsegula pakamwa panga, ndi kupuma wefu wefu; Popeza ndinakhumba malamulo anu.
132
Munditembenukire, ndi kundicitira cifundo, Monga mumatero nao akukonda dzina lanu.
133
Kfiazikitsanimapaziangam'mau anu; Ndipo zisandigonjetse zopanda pace ziri zonse.
134
Mundiombole ku nsautso ya munthu: Ndipo ndidzasamalira malangizo anu.
135
Muwalitse nkhope yanu pa mtumiki wanu; Ndipo mundiphunzitse malemba anu.
136
Maso anga atsitsa mitsinje ya madzi, Popeza sasamalira cilamulo canu.
137
Inu ndinu wolungama, Yehova, Ndipo maweruzo anu ndiwo olunjika.
138
Mboni zanuzo mudazilamulira Ziri zolungama ndi zokhulupirika ndithu.
139
Cangu canga cinandithera, Popeza akundisautsa anaiwala mau anu.
140
Mau anu ngoyera ndithu; Ndi mtumiki wanu awakonda.
141
Wamng'ono ine, ndi wopepulidwa; Koma sindiiwala malemba anu.
142
Cilungamo canu ndico cilungamo cosatha; Ndi cilamulo canu ndico coonadi.
143
Kusautsika ndi kupsinjika kwandigwera; Koma malamulo anu ndiwo ondikondweretsa ine.
144
Mboni zanu ndizo zolungama kosatha; Mundizindikiritse izi, ndipo ndidzakhala ndi moyo.
145
Ndinaitana ndi mtima wanga wonse; mundiyankhe, Yehova; Ndidzasunga malemba anu.
146
Ndinaitanira Inu; ndipulumutseni, Ndipo ndidzasamalira mboni zanu.
147
Ndinapfuula kusanace: Ndinayembekezera mau anu.
148
Maso anga anakumika malonda a usiku, Kuti ndilingirire mau anu.
149
Imvani liu langa monga mwa cifundo canu; Mundipatse moyo monga mwa kuweruza kwanu, Yehova.
150
Otsata zaciwembu andiyandikira; Akhala kutali ndi cilamulo canu.
151
Inu muli pafupi, Yehova; Ndipo malamulo anu onse ndiwo coonadi,
152
Kuyambira kale ndinadziwa mu mboni zanu, Kuti munazikhazika kosatha,
153
Penyani kuzunzika kwanga, nimundilanditse; Pakuti sindiiwala cilamulo canu.
154
Mundinenere mlandu wanga, nimundiombole; Mundipatse moyo monga mwa mau anu.
155
Cipulumutso citalikira oipa; Popeza safuna malemba anu.
156
Zacifundo zanu ndi zazikuru, Yehova; Mundipatse moyo monga mwa maweruzo anu.
157
Ondilondola ndi ondisautsa ndiwoambiri; Koma sindinapatukana nazo mboni zanu.
158
Ndinapenya ocita monyenga, ndipo ndinanyansidwa nao; Popeza sasamalira mau anu.
159
Penyani kuti ndikonda malangizo anu; Mundipatse moyo, Yehova, monga mwa cifundo canu.
160
Ciwerengero ca mau anu ndico coonadi; Ndi maweruzo anu olungama onse akhala kosatha.
161
Nduna zinandilondola kopanda cifukwa; Koma mtima wanga ucita mantha nao mau anu.
162
Ndikondwera nao mau anu, Ngati munthu wakupeza zofunkha zambiri.
163
Ndidana nalo bodza ndi kunyansidwa nalo; Koma ndikonda cilamulo canu.
164
Ndikulemekezani kasanu ndi kawiri, tsiku limodzi, Cifukwa ca maweruzo anu alungama.
165
Akukonda cilamulo canu ali nao mtendere wambiri; Ndipo alibe cokhumudwitsa.
166
Ndinayembekeza cipulumutso canu, Yehova, Ndipo ndinacita malamulo anu.
167
Moyo wanga unasamalira mboni zanu; Ndipo ndizikonda kwambiri.
168
Ndinasamalira malangizo anu ndi mboni zanu; Popeza njira zanga zonse ziri pamaso panu,
169
Kupfuula kwanga kuyandikire pamaso pano, Yehova; Mundizindikiritse monga mwa mau anu.
170
Kupemba kwanga kudze pamaso panu; Mundilanditse monga mwa mau anu.
171
Milomo yanga iturutse cilemekezo; Popeza mundiphunzitsa malemba anu.
172
Lilime langa liyimbire mau anu; Pakuti malamulo anu onse ndiwo olungama.
173
Dzanja lanu likhale lakundithandiza Popezandinasankha malangizo anu.
174
Ndinakhumba cipulumutso canu, Yehova; Ndipo cilamulo canu ndico condikondweretsa.
175
Mzimu wanga ukhale ndi moyo, ndipo udzakulemekezani; Ndipo maweruzo anu andithandize.
176
Ndinasocera ngati nkhosa yotayika; funani mtumiki wanu; Pakuti sindiiwala malamulo anu.
← Chapter 118
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 51
Chapter 52
Chapter 53
Chapter 54
Chapter 55
Chapter 56
Chapter 57
Chapter 58
Chapter 59
Chapter 60
Chapter 61
Chapter 62
Chapter 63
Chapter 64
Chapter 65
Chapter 66
Chapter 67
Chapter 68
Chapter 69
Chapter 70
Chapter 71
Chapter 72
Chapter 73
Chapter 74
Chapter 75
Chapter 76
Chapter 77
Chapter 78
Chapter 79
Chapter 80
Chapter 81
Chapter 82
Chapter 83
Chapter 84
Chapter 85
Chapter 86
Chapter 87
Chapter 88
Chapter 89
Chapter 90
Chapter 91
Chapter 92
Chapter 93
Chapter 94
Chapter 95
Chapter 96
Chapter 97
Chapter 98
Chapter 99
Chapter 100
Chapter 101
Chapter 102
Chapter 103
Chapter 104
Chapter 105
Chapter 106
Chapter 107
Chapter 108
Chapter 109
Chapter 110
Chapter 111
Chapter 112
Chapter 113
Chapter 114
Chapter 115
Chapter 116
Chapter 117
Chapter 118
Chapter 119
Chapter 120
Chapter 121
Chapter 122
Chapter 123
Chapter 124
Chapter 125
Chapter 126
Chapter 127
Chapter 128
Chapter 129
Chapter 130
Chapter 131
Chapter 132
Chapter 133
Chapter 134
Chapter 135
Chapter 136
Chapter 137
Chapter 138
Chapter 139
Chapter 140
Chapter 141
Chapter 142
Chapter 143
Chapter 144
Chapter 145
Chapter 146
Chapter 147
Chapter 148
Chapter 149
Chapter 150
Chapter 120 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48
49
50
51
52
53
54
55
56
57
58
59
60
61
62
63
64
65
66
67
68
69
70
71
72
73
74
75
76
77
78
79
80
81
82
83
84
85
86
87
88
89
90
91
92
93
94
95
96
97
98
99
100
101
102
103
104
105
106
107
108
109
110
111
112
113
114
115
116
117
118
119
120
121
122
123
124
125
126
127
128
129
130
131
132
133
134
135
136
137
138
139
140
141
142
143
144
145
146
147
148
149
150