bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
/
1 Kings 17
1 Kings 17
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
← Chapter 16
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 18 →
1
Ndipo Eliya wa ku Tisibe wokhala ku Giliyadi ananena ndi Ahabu, nati, Pali Yehova Mulungu wa Israele, amene ndimakhala pamaso pake, ngati adzagwa mame kapena mvula zaka izi, koma ntanena ine ndipo.
2
Ndipo mau a Yehova anadza kwa iye, nati,
3
Choka kuno, nutembenukire kum'mawa, ukabisale kumtsinje Keriti uli ku Yordani.
4
Ndipo kudzakhala kuti uzikamwa mumtsinje, ndipo ndalamulira makungubwi kukudyetsa kumeneko.
5
Momwemo iye anamuka, nachita monga mwa mau a Yehova, nakakhala kumtsinje Keriti uli ku Yordani.
6
Ndipo makungubwi anamtengera mkate ndi nyama m'mawa, ndi mkate ndi nyama madzulo; namamwa iye mumtsinje.
7
Ndipo kunachitika, atapita masiku ena mtsinje udaphwa, popeza munalibe mvula m'dziko.
8
Ndipo mau a Yehova anadza kwa iye, nati,
9
Nyamuka, pita ku Zarefati wa ku Sidoni, nukhale kumeneko; taona, ndamlamulira mkazi wamasiye wa kumeneko akudyetse.
10
Tsono iye ananyamuka namka ku Zarefati, nafika ku chipata cha mudzi; ndipo taona mkazi wamasiye anali kutola nkhuni; ndipo iye anamuitana, nati, Unditengere madzi pang'ono m'chikho, ndimwe.
11
Ndipo m'mene analikumuka kukatenga iye anamuitananso, nati, Unditengerenso kanthongo ka mkate m'dzanja lako.
12
Nati iye, Pali Yehova Mulungu wako, ndilibe mkate, koma kaufa dzanja limodzi kali m'mbiya, ndi mafuta pang'ono m'nsupa; ndipo taona, ndilikutola nkhuni ziwiri kuti ndikadziphikire ndekha ndi mwana wanga, tidye, tife.
13
Ndipo Eliya anati kwa iye, Usachita mantha, kachite monga umo wanenamo, koma thanga wandiocherako kamkate, nubwere nako kwa ine; ndipo utatero udziphikire wekha ndi mwana wako.
14
Popeza atero Yehova Mulungu wa Israele, Mbiya ya ufa siidzatha, ndipo nsupa ya mafuta siidzachepa, kufikira tsiku lakugwetsa mvula Yehova pa dziko lapansi.
15
Ndipo iye anakachita monga mwa mau a Eliya, nadya iye mwini, ndi iyeyo, ndi a m'nyumba ake, masiku ambiri.
16
Mbiya ya ufa siidatha, ndi nsupa ya mafuta siinachepa, monga mwa mau a Yehova amene ananenetsa Eliya.
17
Ndipo kunali, zitatha izi, mwana wa mkazi mwini nyumbayo anadwala; ndipo pokula nthenda yake, analeka kupuma.
18
Ndipo mkaziyo ananena ndi Eliya, Ndili nawe chiyani munthu iwe wa Mulungu? Kodi wadza kwa ine kundikumbutsa tchimo langa, ndi kundiphera mwana wanga?
19
Ndipo ananena naye, Ndipatse mwana wako. Namtenga m'mfukato mwake napita naye ku chipinda chosanja chogonamo iyeyo, namgoneka pa kama wa iye mwini.
20
Nafuulira kwa Yehova, nati, Yehova Mulungu wanga, kodi mwamgwetsera choipa mkazi wamasiye amene ndikhala naye, kumphera mwanake?
21
Nafungatira katatu pa mwanayo, nafuulira kwa Yehova, nati, Yehova Mulungu wanga, ndikupemphani, ubwere moyo wake wa mwanayu m'chifuwa mwake.
22
Ndipo Yehova anamva mau a Eliya, ndipo moyo wa mwanayo unalowanso mwa iye, nakhalanso moyo.
23
Ndipo Eliya ananyamula mwanayo, natsika naye ku chipinda chosanja, nalowa naye m'nyumba, nampereka kwa amake; nati, Eliya, Taona, mwana wako ali moyo.
24
Ndipo mkazi anati kwa Eliya, Ndizindikira tsopano kuti ndinu munthu wa Mulungu, ndi kuti mau a Yehova ali m'kamwa mwanuwo ngoona.
← Chapter 16
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 18 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22