bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
/
1 Kings 9
1 Kings 9
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
← Chapter 8
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 10 →
1
Ndipo kunali, atasiriza Solomoni kumanga nyumba ya Yehova, ndi nyumba ya mfumu, ndi chifuniro chonse cha Solomoni anachikhumbacho,
2
Yehova anaonekera kwa Solomoni nthawi yachiwiri, monga momwe adamuonekera ku Gibiyoni.
3
Ndipo Yehova anati kwa iye, Ndamva pemphero lako ndi pembedzero lako wandipembedza nalo; ndapatula nyumba imene waimangayi kuikamo dzina langa nthawi zosatha, ndipo maso anga ndi mtima wanga zidzakhala kumeneko masiku onse.
4
Ndipo iwe ukadzayenda pamaso panga, monga momwe Davide atate wako anayendera ndi mtima woona ndi wolungama, kuzichita zonse ndakulamulirazo, ndi kusunga malemba anga ndi maweruzo anga,
5
pamenepo Ine ndidzakhazikitsa chimpando cha ufumu wako pa Israele nthawi yosatha, monga ndinalonjezana ndi Davide atate wako, ndi kuti, Sadzakusowa munthu wamwamuna pa mpando wachifumu wa Israele.
6
Koma mukadzabwerera pang'ono pokha osanditsata, kapena inu, kapena ana anu, osasunga malamulo anga ndi malemba anga amene ndawaika pamaso panu; mukadzatumikira milungu ina ndi kuilambira;
7
pamenepo Ine ndidzalikha Aisraele kuwachotsera m'dziko ndidawapatsali; ndipo nyumba yino ndapatulira dzina langayi ndidzaitaya kosapenyeka; ndipo Israele adzakhala ngati mwambi ndi nkhani pakati pa anthu onse.
8
Ndipo munthu yense wopitirira pa nyumba yaitali yino adzadabwa nayo, nadzainyoza, nadzati, Yehova watero chifukwa ninji ndi dziko lino ndi nyumba yino?
9
Ndipo anthu adzayankha, Popeza anasiya Yehova Mulungu wao amene adatulutsa makolo ao m'dziko la Ejipito, natsata milungu ina, nailambira, naitumikira; chifukwa chake Yehova anawagwetsera choipa chonsechi.
10
Ndipo kunali, zitatha zaka makumi awiri m'mene Solomoni adatsiriza nyumba ziwirizo, ndizo nyumba ya Yehova ndi nyumba ya mfumu;
11
popeza Hiramu mfumu ya Tiro adamthandiza Solomoni ndi mitengo yamkungudza ndi yamlombwa ndi golide yemwe, monga momwe iye anafuniramo, chifukwa chake mfumu Solomoni anampatsa Hiramu midzi makumi awiri m'dziko la Galileya.
12
Ndipo Hiramu anatuluka ku Tiro kukaona midzi adampatsa Solomoniyo, koma siinamkomera.
13
Nati, Midzi yino mwandipatsayi njotani, mbale wanga? Naitcha dzina lao, Dziko lachikole, kufikira lero lino.
14
Ndipo Hiramu adatumiza kwa mfumu matalente a golide zana limodzi mphambu makumi awiri.
15
Ndipo chifukwa chake cha msonkho uja anausonkhetsa mfumu Solomoni ndi chimenechi; kuti amange nyumba ya Yehova, ndi nyumba ya iye yekha, ndi Milo, ndi linga la Yerusalemu, ndi Hazori, ndi Megido, ndi Gezere.
16
Pakuti Farao mfumu ya Aejipito adakwera nalanda Gezere, nautentha ndi moto, nawapha Akanani akukhala m'mudzimo, naupereka kwaulere kwa mwana wake mkazi wa Solomoni.
17
Ndipo Solomoni anamanganso Gezere, ndi Betehoroni wakunsi,
18
ndi Baalati, ndi Tamara wa m'chipululu m'dziko muja,
19
ndi midzi yonse yosungamo zinthu zake za Solomoni, ndi midzi yosungamo magaleta ake, ndi midzi yokhalamo apakavalo ake, ndi zina zilizonse zidakomera Solomoni kuzimanga m'Yerusalemu, ndi ku Lebanoni, ndi m'dziko lonse la ufumu wake.
20
Ndipo Aamori, ndi Ahiti, ndi Aperizi, ndi Ahivi, ndi Ayebusi otsala, amene sanali a ana a Israele,
21
ana ao amene adatsala m'dziko, amene ana a Israele sanakhoze kuononga konse, Solomoni anawasenzetsa msonkho wa ntchito kufikira lero.
22
Koma Solomoni sanawayese ana a Israele akapolo, koma iwowo anali anthu a nkhondo, ndi anyamata ake, ndi akalonga ake, ndi akazembe ake, ndi oyang'anira magaleta ake ndi apakavalo ake.
23
Ameneyo anali akulu a kapitao oyang'anira ntchito ya Solomoni, mazana asanu mphambu makumi asanu akulamulira anthu ogwira ntchito aja.
24
Koma mwana wamkazi wa Farao anatuluka m'mudzi wa Davide kukwera kunyumba yake adammangira Solomoni, pamenepo iye anamanganso Milo.
25
Ndipo chaka chimodzi Solomoni anapereka katatu nsembe zopsereza ndi zamtendere, pa guwa la nsembe limene anammangira Yehova, nafukiza zonunkhira pa guwa la nsembe pamaso pa Yehova, atatsiriza nyumbayo.
26
Ndipo mfumu Solomoni anamanga zombo zambiri ku Eziyoni-Gebere uli pafupi ndi Eloti, m'mphepete mwa Nyanja Yofiira, ku dziko la Edomu.
27
Ndipo, Hiramu anatuma anyamata ake m'zombozo amalinyero ozolowera m'nyanja, pamodzi ndi anyamata a Solomoni.
28
Ndipo iwo anafika ku Ofiri, natengako golide matalente mazana anai mphambu makumi awiri, nafika naye kwa mfumu Solomoni.
← Chapter 8
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 10 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22