bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
/
2 Corinthians 1
2 Corinthians 1
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 2 →
1
Paulo, mtumwi wa Khristu Yesu, mwa chifuniro cha Mulungu, ndi Timoteo mbaleyo, kwa Mpingo wa Mulungu umene uli ku Korinto, pamodzi ndi oyera mtima onse amene ali m'Akaya monse:
2
Chisomo kwa inu ndi mtendere zochokera kwa Mulungu Atate wathu, ndi Ambuye Yesu Khristu.
3
Wolemekezeka Mulungu ndi Atate wa Ambuye wathu Yesu Khristu, Atate wa zifundo ndi Mulungu wa chitonthozo chonse,
4
wotitonthoza ife m'nsautso yathu yonse, kuti tidzathe ife kutonthoza iwo okhala m'nsautso iliyonse, mwa chitonthozo chimene titonthozedwa nacho tokha ndi Mulungu.
5
Pakuti monga masautso a Khristu atichulukira ife, choteronso chitonthozo chathu chichuluka mwa Khristu.
6
Koma ngati tisautsidwa, kuli chifukwa cha chitonthozo ndi chipulumutso chanu; ngati titonthozedwa, kuli kwa chitonthozo chanu chimene chichititsa mwa kupirira kwa masautso omwewo amene ifenso timva.
7
Ndipo chiyembekezo chathu cha kwa inu nchokhazikika; podziwa kuti monga muli oyanjana ndi masautsowo, koteronso ndi chitonthozo.
8
Pakuti sitifuna abale, kuti mukhale osadziwa za chisautso chathu tinakomana nacho m'Asiya, kuti tinathodwa kwakukulu, koposa mphamvu yathu, kotero kuti tinada nkhawa ngakhale za moyo wathu;
9
koma tokha tinakhala nacho chitsutso cha imfa mwa ife tokha, kuti tisalimbike pa ife tokha, koma pa Mulungu wakuukitsa akufa;
10
amene anatilanditsa mu imfa yaikulu yotere, nadzalanditsa; amene timyembekezera kuti adzalanditsanso;
11
pothandizana inunso ndi pemphero lanu la kwa ife; kuti pa mphatso ya kwa ife yodzera kwa anthu ambiri, payamikike ndi anthu ambiri chifukwa cha ife.
12
Pakuti kudzitamandira kwathu ndiko umboni wa chikumbu mtima chathu, kuti m'chiyero ndi kuona mtima kwa Mulungu, si m'nzeru ya thupi, koma m'chisomo cha Mulungu tinadzisunga m'dziko lapansi, koma koposa kwa inu.
13
Pakuti sitilemba kwa inu zina, koma zimene muwerenga, kapenanso muvomereza; ndipo ndiyembekeza kuti mudzavomereza kufikira chimaliziro;
14
monganso munativomerezera ife pena, kuti ife ndife kudzitamandira kwanu, monga momwe inunso muli kudzitamandira kwathu m'tsiku la Ambuye wathu Yesu.
15
Ndipo m'kulimbika kumene ndinafuna kudza kwa inu kale, kuti mukakhale nacho chisomo chachiwiri;
16
ndipo popyola kwanu kupita ku Masedoniya, ndi kudzanso kwa inu pobwera kufuma ku Masedoniya; ndi kuperekezedwa ndi inu ku Yudeya.
17
Pamenepo, pakufuna chimene, kodi ndinachitapo kosinthasintha? Kapena zimene nditsimikiza mtima kodi ndizitsimikiza mtima monga mwa thupi? Kuti pa ine pakhale eya, eya, ndi iai, iai?
18
Koma Mulungu ali wokhulupirika, kuti mau athu a kwa inu sanakhala eya ndi iai.
19
Pakuti Mwana wa Mulungu, Yesu Khristu, amene analalikidwa mwa inu ndi ife, (ine ndi Silivano ndi Timoteo) sanakhala eya ndi iai, koma anakhala eya mwa Iye.
20
Pakuti monga mawerengedwe a malonjezano a Mulungu ali mwa Iye eya; chifukwa chakenso ali mwa Iye Amen, kwa ulemerero wa Mulungu mwa ife.
21
Koma Iye wakutikhazika pamodzi ndi inu kwa Khristu, natidzoza ife, ndiye Mulungu;
22
amenenso anatisindikiza chizindikiro, natipatsa chikole cha Mzimu mu mitima yathu.
23
Koma ine ndiitana Mulungu akhale mboni pa moyo wanga, kuti kulekera inu ndinaleka kudza ku Korinto.
24
Si kuti tichita ufumu pa chikhulupiriro chanu, koma tikhala othandizana nacho chimwemwe chanu; pakuti ndi chikhulupiriro muimadi.
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 2 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13