bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
/
2 Corinthians 10
2 Corinthians 10
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
← Chapter 9
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 11 →
1
Koma ine ndekha Paulo, ndidandaulira inu mwa kufatsa ndi ulere wa Khristu, ine amene pamaso panu ndikhala wodzichepetsa pakati pa inu, koma pokhala kwina ine ndilimbika mtima kwa inu;
2
koma ndipempha kuti pokhala ndili pomwepo, ndisalimbike mtima ndi kulimbika kumene ndiyesa kulimbika nako pa ena, amene atiyesera ife monga ngati tilikuyendayenda monga mwa thupi.
3
Pakuti pakuyendayenda m'thupi, sitichita nkhondo monga mwa thupi,
4
(pakuti zida za nkhondo yathu sizili za thupi, koma zamphamvu mwa Mulungu zakupasula malinga);
5
ndi kugwetsa matsutsano, ndi chokwezeka chonse chimene chidzikweza pokana chidziwitso cha Mulungu, ndi kugonjetsa ganizo lonse kukumvera kwa Khristu;
6
ndi kukhala okonzeka kubwezera chilango kusamvera konse, pamene kumvera kwanu kudzakwaniridwa.
7
Kodi mupenyera zopenyeka pamaso? Ngati wina alimbika mwa yekha kuti ali wa Khristu, ayesere ichinso mwa iye yekha, kuti monga iye ali wa Khristu, koteronso ife.
8
Pakuti ndingakhale ndikadzitamandira kanthu kochulukira za ulamuliro (umene anatipatsa Ambuye kukumangirira, ndipo si kukugwetsera kwanu), sindidzanyazitsidwa;
9
kuti ndisaoneke monga ngati kukuopsani mwa akalatawo.
10
Pakuti, akalatatu, ati, ndiwo olemera, ndi amphamvu; koma maonekedwe a thupi lake ngofooka, ndi mau ake ngachabe.
11
Woteroyo ayese ichi kuti monga tili ife ndi mau mwa akalata, pokhala palibe ife, tili oterenso m'machitidwe pokhala tili pomwepo.
12
Pakuti sitilimba mtima kudziwerenga, kapena kudzilinganiza tokha ndi ena a iwo amene adzivomeretsa okha; koma iwowa, podziyesera okha ndi iwo okha, ndi kudzilinganiza okha ndi iwo okha, alibe nzeru.
13
Koma ife sitidzadzitamandira popitirira muyeso, koma monga mwa muyeso wa chilekezero chimene Mulungu anatigawira muyeso, kufikira ngakhale kwa inunso.
14
Pakuti sitinyanyampiradi tokha, monga ngati sitinafikira kwa inu; pakuti tinadza kufikira inunso, mu Uthenga Wabwino wa Khristu:
15
osadzitamandira popitirira muyeso mwa machititso a ena; koma tili nacho chiyembekezo kuti pakukula chikhulupiriro chanu, tidzakulitsidwa mwa inu monga mwa chilekezero chathu kwa kuchulukira,
16
kukalalikira Uthenga Wabwino m'tsogolo mwake mwa inu, sikudzitamandira mwa chilekezero cha wina, ndi zinthu zokonzeka kale.
17
Koma iye wodzitamandira adzitamandire mwa Ambuye;
18
pakuti si iye amene adzitama yekha, koma iye amene Ambuye amtama ali wovomerezeka.
← Chapter 9
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 11 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13