bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
/
2 Samuel 14
2 Samuel 14
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
← Chapter 13
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 15 →
1
Ndipo Yowabu mwana wa Zeruya anazindikira kuti mtima wa mfumu unalunjika kwa Abisalomu.
2
Ndipo Yowabu anatumiza ku Tekowa, natenga kumeneko mkazi wanzeru, nanena naye, Ukokomezeke monga mfedwa, nuvale zovala za pamaliro, osadzola mafuta, koma ukhale ngati munthu wamkazi wakulira akufa nthawi yaikulu.
3
Nulowe kwa mfumu, nulankhule nayo monga momwemo. Chomwecho Yowabu anampangira mau.
4
Ndipo pamene mkazi wa ku Tekowayo anati alankhule ndi mfumuyo, anagwa nkhope yake pansi, namlambira, nati, Ndithandizeni mfumu.
5
Ndipo mfumuyo inanena naye, Usowanji? Iye nayankha, Zoonadi ine ndine mkazi wamasiye, mwamuna wanga anamwalira.
6
Ndipo mdzakazi wanu ndinali nao ana amuna awiri, ndipo awiriwo analimbana kumunda, panalibe wina wakuwaletsa, koma wina anakantha mnzake namupha.
7
Ndipo onani, chibale chonse chinaukira mdzakazi wanu, ndi kuti, Upereke iye amene anakantha mbale wake, kuti timuphe chifukwa cha moyo wa mbale wake amene anamupha; koma pakutero adzaononga wolowa yemwe; chomwecho adzazima khala langa lotsala, ndipo sadzasiyira mwamuna wanga dzina kapena mbeu kunja kuno.
8
Ndipo mfumu inanena ndi mkaziyo, Pita kunyumba yako, ndipo ndidzalamulira za iwe.
9
Ndipo mkazi wa ku Tekowayo ananena ndi mfumu, Mbuye wanga mfumu, mphulupulu ikhale pa ine ndi pa nyumba ya atate wanga; ndipo mfumu ndi mpando wachifumu wao zikhale zopanda chifukwa.
10
Ndipo mfumu inati, Ubwere naye kwa ine aliyense wakunena kanthu ndi iwe, ndipo iyeyo sadzakukhudzanso.
11
Nati iye, Mfumu mukumbukire Yehova Mulungu wanu kuti wolipsa mwazi asaonjeze kuononga, kuti angaononge mwana wanga. Niti iyo, Pali Yehova, palibe tsitsi limodzi la mwana wako lidzagwa pansi.
12
Pamenepo mkaziyo anati, Mulole mdzakazi wanu alankhule mau kwa mbuye wanga mfumu. Niti iyo Nena.
13
Ndipo mkaziyo anati, Chifukwa ninjinso munalingalira chinthu chotere pa anthu a Mulungu? Pakuti pakulankhula mau awa mfumu ikunga wopalamula, popeza mfumu siitumiza okamtenganso woingidwa wake.
14
Pakuti kufa tidzafa, ndipo tili ngati madzi otayika pansi amene sakhoza kuwaolanso; ngakhale Mulungu sachotsa moyo, koma alingalira njira yakuti wotayikayo asakhale womtayikira Iye.
15
Chifukwa chake tsono chakuti ndadzanena mau awa ndi mbuye wanga mfumu, ndicho kuti anthu anandiopsa ine; ndipo mdzakazi wanu ndinati, Ndilankhuletu ndi mfumu; kapena mfumu idzachita chopempha mdzakazi wake.
16
Pakuti mfumu idzamvera ndi kupulumutsa mdzakazi wake m'dzanja la munthu wakufuna kundiononga ine pamodzi ndi mwana wanga, kutichotsa ku cholowa cha Mulungu.
17
Ndipo mdzakazi wanu ndinati, Mau a mbuye wanga mfumu akhale opumulitsa; mbuye wanga mfumu ali ngati mthenga wa Mulungu, kuzindikira zabwino ndi zoipa; ndipo Yehova Mulungu wanu akhale nanu.
18
Pamenepo mfumu inayankha, ninena naye mkaziyo, Usandibisire kanthu ka zimene ndidzakufunsa iwe. Mkaziyo nati, Mbuye wanga mfumu anene.
19
Ndipo mfumuyo inati, Kodi Yowabu adziwana ndi iwe mwa izi zonse? Mkaziyo nayankha nati, Pali moyo wanu mbuye wanga mfumu, palibe kulewa ku dzanja lamanja, kapena kulamanzere kwa zonse mudazinena mbuye wanga mfumu; pakuti mnyamata wanu Yowabu ndiye anandiuza, naika mau onse awa m'kamwa mwa mdzakazi wanu.
20
Mnyamata wanu Yowabu anachita chinthu ichi kuti asandulize mamvekedwe a mlanduwo. Ndipo mbuye wanga ali wanzeru, monga ndi nzeru ya mthenga wa Mulungu, kudziwa zonse zili m'dziko lapansi.
21
Ndipo mfumuyo inanena ndi Yowabu, Taonanitu, ndachita chinthu ichi; chifukwa chake, pita nubwere nayenso mnyamatayo Abisalomu.
22
Ndipo Yowabu anagwa nkhope yake pansi, namlambira, nadalitsa mfumuyo; nati Yowabu, Lero mnyamata wanu ndadziwa kuti munandikomera mtima, mbuye wanga mfumu, popeza mfumu yachita chopempha mnyamata wake.
23
Chomwecho Yowabu ananyamuka namka ku Gesuri, nabwera naye Abisalomu ku Yerusalemu.
24
Ndipo mfumu inati, Apatukire kunyumba ya iye yekha, koma asaone nkhope yanga. Chomwecho Abisalomu anapatukira kunyumba ya iye yekha, wosaona nkhope ya mfumu.
25
Ndipo m'Israele monse munalibe wina anthu anamtama kwambiri chifukwa cha kukongola kwake monga Abisalomu; kuyambira ku mapazi kufikira pakati pa mutu wake mwa iye munalibe chilema.
26
Ndipo pometa tsitsi lake amameta potsiriza chaka, chifukwa tsitsi linamlemerera, chifukwa chake atalimeta anayesa tsitsi la pa mutu wake, napeza masekeli mazana awiri, monga mwa muyeso wa mfumu.
27
Ndipo kwa Abisalomu kunabadwa ana amuna atatu ndi mwana wamkazi mmodzi, dzina lake ndiye Tamara, iye ndiye mkazi wokongola nkhope.
28
Ndipo Abisalomu anakhala ku Yerusalemu zaka ziwiri zathunthu, osaona nkhope ya mfumu.
29
Pamenepo Abisalomu anaitana Yowabu kuti akamtumize iye kwa mfumu; koma anakana kubwera kwa iye; ndipo anamuitananso nthawi yachiwiri, koma anakana kubwera.
30
Chifukwa chake iye anati kwa anyamata ake, Onani munda wa Yowabu uli pafupi ndi wanga, ndipo iye ali ndi barele pamenepo, mukani mukamtenthere. Ndipo anyamata a Abisalomu anatentha za m'mundawo.
31
Pamenepo Yowabu ananyamuka nafika kwa Abisalomu kunyumba yake, nanena naye, Chifukwa ninji anyamata anu anatentha za m'munda mwanga;
32
Abisalomu nayankha Yowabu, Ona, ndinatumiza kwa iwe kuti, Bwera kuno kuti ndikutume kwa mfumu kukanena, Ine ndinabwereranji kuchokera ku Gesuri? Mwenzi nditakhala komweko; chifukwa chake tsono mundilole kuona nkhope ya mfumu; ndipo ngati mulinso mphulupulu mwa ine andiphe ndithu.
33
Chomwecho Yowabu anadza kwa mfumu namuuza; ndipo pamene iye adaitana Abisalomu, iye anadza kwa mfumu naweramira nkhope yake pansi pamaso pa mfumu; ndipo mfumu inampsompsona Abisalomu.
← Chapter 13
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 15 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24