bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
/
Daniel 12
Daniel 12
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
← Chapter 11
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
1
Ndipo nthawi yomweyi adzauka Mikaele kalonga wamkulu wakutumikira ana a anthu a mtundu wako; ndipo padzakhala nthawi ya masautso, siinakhala yotere kuyambira mtundu wa anthu kufikira nthawi yomwe ija; ndipo nthawi yomweyo anthu ako adzapulumutsidwa, yense amene ampeza wolembedwa m'buku.
2
Ndipo ambiri a iwo ogona m'fumbi lapansi adzauka, ena kunka kumoyo wosatha, ndi ena kumanyazi ndi mnyozo wosatha.
3
Ndipo aphunzitsi adzawala ngati kunyezimira kwa thambo; ndi iwo otembenuza ambiri atsate chilungamo ngati nyenyezi kunthawi za nthawi.
4
Koma iwe Daniele, tsekera mau awa, nukomere chizindikiro buku, mpaka nthawi ya chimaliziro; ambiri adzathamanga chauko ndi chauko, ndi chidziwitso chidzachuluka.
5
Pamenepo ine Daniele ndinapenya, ndipo taonani, anaimapo awiri ena, wina m'mphepete mwa mtsinje tsidya lino, ndi mnzake m'mphepete mwa mtsinje tsidya lija.
6
Ndipo wina anati kwa munthu wovala bafuta, wokhala pamwamba pa madzi a mumtsinje, Chimaliziro cha zodabwitsa izi chidzafika liti?
7
Ndipo ndinamva munthuyo wovala bafuta wokhala pamwamba pa madzi a mumtsinje, nakweza dzanja lake lamanja ndi lamanzere kumwamba, nalumbira pali Iye wokhala ndi moyo kosatha, kuti zidzachitika nthawi, ndi nthawi zina, ndi nusu; ndipo atatha kumwaza mphamvu ya anthu opatulikawo zidzatha izi zonse.
8
Ndinachimva ichi, koma osachizindikira; pamenepo ndinati Mbuye wanga, chitsiriziro cha izi nchiyani?
9
Ndipo anati, Pita Daniele; pakuti mauwo atsekedwa, nakomeredwa chizindikiro mpaka nthawi ya chitsiriziro.
10
Ambiri adzadzitsuka ndi kudziyeretsa, nadzayesedwa ndi moto; koma oipa adzachita moipa; ndipo palibe mmodzi wa oipa adzazindikira; koma aphunzitsi ndiwo adzazindikira.
11
Ndipo kuyambira nthawi yoti idzachotsedwa nsembe yachikhalire, nichidzaimika chonyansa chakupululutsa, adzakhalanso masiku chikwi chimodzi mphambu mazana awiri kudza makumi asanu ndi anai.
12
Wodala iye amene ayembekeza, nafikira kumasiku chikwi chimodzi mphambu mazana atatu kudza makumi atatu ndi asanu.
13
Koma iwe, muka mpaka chimaliziro; pakuti udzapumula, nudzaima m'gawo lako masiku otsiriza.
← Chapter 11
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12