bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
/
Daniel 4
Daniel 4
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
← Chapter 3
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 5 →
1
Mfumu Nebukadinezara, kwa anthu mitundu ya anthu, ndi a manenedwe okhala pa dziko lonse lapansi: Mtendere uchulukire inu.
2
Chandikomera kuonetsa zizindikiro ndi zozizwa, zimene anandichitira Mulungu Wam'mwambamwamba.
3
Ha! Zizindikiro zake nzazikulu, ndi zozizwa zake nza mphamvu, ufumu wake ndiwo ufumu wosatha, ndi kulamulira kwake ku mibadwomibadwo.
4
Ine Nebukadinezara ndinalimkupumula m'nyumba mwanga, ndi kukhala mwaufulu m'chinyumba changa.
5
Ndinaona loto lakundiopsa, ndi zolingirira za pakama panga, ndi masomphenya a m'mtima mwanga, zinandivuta ine.
6
Chifukwa chake ndinalamulira kuti adze kwa ine anzeru onse a ku Babiloni, kuti andidziwitse kumasulira kwake kwa lotoli.
7
Pamenepo anafika alembi, openda, Ababiloni, ndi alauli; ndipo ndinawafotokozera lotoli, koma sanandidziwitse kumasulira kwake.
8
Koma potsiriza pake analowa pamaso panga Daniele, dzina lake ndiye Belitesazara, monga mwa dzina la mulungu wanga, amenenso muli mzimu wa milungu yoyera m'mtima mwake; ndipo ndinamfotokozera lotoli pamaso pake, ndi kuti,
9
Belitesazara iwe, mkulu wa alembi, popeza ndidziwa kuti mwa iwe muli mzimu wa milungu yoyera, ndi kuti palibe chinsinsi chikusautsa, undifotokozere masomphenya a loto langa ndalotali, ndi kumasulira kwake.
10
Masomphenya a m'mtima mwanga pakama panga ndi awa: Ndinapenya ndi kuona mtengo pakati pa dziko lapansi, msinkhu wake ndi waukulu.
11
Mtengowo unakula, nulimba, ndi msinkhu wake unafikira kumwamba, nuonekera mpaka chilekezero cha dziko lonse lapansi.
12
Masamba ake anali okoma, ndi zipatso zake zinachuluka, ndi m'menemo munali zakudya zofikira onse, nyama za kuthengo zinatsata mthunzi wake, ndi mbalame za m'mlengalenga zinafatsa m'thambi zake, ndi nyama zonse zinadyako.
13
Ndinaona m'masomphenya a m'mtima mwanga pakama panga, taonani, mthenga woyera anatsika kumwamba.
14
Anafuulitsa, natero, Likhani mtengowo, sadzani nthambi zake, yoyolani masamba ake, mwazani zipatso zake, nyama za kuthengo zichoke pansi pake, ndi mbalame pa nthambi zake.
15
Koma siyani chitsa ndi mizu yake m'nthaka, chomangidwa ndi mkombero wa chitsulo ndi mkuwa, mu msipu wa kuthengo; nchokhathamira ndi mame a kumwamba, ndi gawo lake likhale pamodzi ndi nyama zili m'machire a m'dziko.
16
Mtima wake usandulike, usakhalenso mtima wa munthu, apatsidwe mtima wonga wa nyama, nizimpitire nthawi zisanu ndi ziwiri.
17
Chitsutso ichi adachilamulira amithenga oyerawo, anachifunsa, nachinena, kuti amoyo adziwe kuti Wam'mwambamwamba alamulira m'ufumu wa anthu, naupereka kwa aliyense Iye afuna, nauutsira wolubukira anthu.
18
Loto ili ndinaliona ine mfumu Nebukadinezara; ndipo iwe, Belitesazara, undifotokozere kumasulira kwake, popeza anzeru onse a m'ufumu wanga sakhoza kundidziwitsa kumasulira kwake; koma iwe ukhoza, popeza mwa iwe muli mzimu wa milungu yoyera.
19
Pamenepo Daniele, dzina lake ndiye Belitesazara anadabwa nthawi, namsautsa maganizo ake. Mfumu inayankha, niti, Belitesazara, lisakusautse lotoli, kapena kumasulira kwake. Belitesazara anayankha, nati, Mbuye wanga, lotoli likadakhala la iwo akudana nanu, ndi kumasulira kwake kwa iwo akuutsana nanu.
20
Mtengo mudauona umene unakula, nukhala wolimba, nufikira kumwamba msinkhu wake, nuonekera pa dziko lonse lapansi,
21
umene masamba ake anali okoma, ndi zipatso zake zochuluka, ndi m'menemo munali chakudya chofikira onse, umene nyama za kuthengo zinakhala pansi pake, ndi mbalame za m'mlengalenga zinapeza pokhala pao pa nthambi yake;
22
ndinu, mfumu; mwakula, mwalimba, pakuti ukulu wanu wakula, nufikira kumwamba, ndi ufumu wanu ku chilekezero cha dziko lapansi.
23
Tsono, kuti mfumu inaona mthenga woyera wotsika kumwamba, ndi kuti, Likhani mtengowo ndi kuuononga, koma siyani chitsa chake ndi mizu m'nthaka, chomangidwa ndi mkombero wa chitsulo ndi mkuwa, mu msipu wa kuthengo, nichikhale chokhathamira ndi mame a kumwamba, ndi gawo lake likhale pamodzi ndi nyama za kuthengo, mpaka zitampitira nthawi zisanu ndi ziwiri;
24
kumasulira kwake ndi uku, mfumu; ndipo chilamuliro cha Wam'mwambamwamba chadzera mbuye wanga mfumu:
25
kuti adzakuingitsani kukuchotsani kwa anthu, ndi pokhala panu padzakhala pamodzi ndi nyama za kuthengo; ndipo mudzadya udzu ngati ng'ombe, nimudzakhala wokhathamira ndi mame a kumwamba, nizidzakupitirani nthawi zisanu ndi ziwiri, mpaka mudzadziwa kuti Wam'mwambamwamba alamulira m'ufumu wa anthu, naupereka kwa aliyense Iye afuna mwini.
26
Ndipo kuti anauza asiye chitsa ndi mizu ya mtengo, ufumu wanu udzakhazikikira inu, mukakatha kudziwa kuti Kumwamba kumalamulira.
27
Chifukwa chake, mfumu, kupangira kwanga kukomere inu, dulani machimo anu ndi kuchita chilungamo, ndi mphulupulu zanu mwa kuchitira aumphawi chifundo; kuti kapena nthawi ya mtendere wanu italike.
28
Chonsechi chinagwera mfumu Nebukadinezara.
29
Itatha miyezi khumi ndi iwiri, analikuyenda m'chinyumba chachifumu cha ku Babiloni.
30
Mfumu inanena, niti, Suyu Babiloni wamkulu ndinammanga, akhale pokhala pachifumu, ndi mphamvu yanga yaikulu uoneke ulemerero wa chifumu changa?
31
Akali m'kamwa mwa mfumu mau awa, anamgwera mau ochokera kumwamba, ndi kuti, Mfumu Nebukadinezara, anena kwa iwe: ufumu wakuchokera.
32
Nadzakuinga kukuchotsa kwa anthu, ndi pokhala pako udzakhala pamodzi ndi nyama za kuthengo; adzakudyetsa udzu ngati ng'ombe; nizidzakupitira nthawi zisanu ndi ziwiri, mpaka udzadziwa kuti Wam'mwambamwamba alamulira m'ufumu wa anthu, naupereka kwa aliyense Iye afuna mwini.
33
Nthawi yomweyo anachitika mau awa kwa Nebukadinezara; anamuinga kumchotsa kwa anthu; nadya udzu ngati ng'ombe iye, ndi thupi lake linakhathamira ndi mame a kumwamba, mpaka tsitsi lake lidamera ngati nthenga za chiombankhanga ndi makadabo ake ngati makadabo a mbalame.
34
Atatha masiku awa tsono, ine Nebukadinezara ndinakweza maso anga kumwamba, ndi nzeru zanga zinandibwerera; ndipo ndinalemekeza Wam'mwambamwamba, ndi kumyamika ndi kumchitira ulemu Iye wokhala chikhalire; pakuti kulamulira kwake ndiko kulamulira kosatha, ndi ufumu wake ku mibadwomibadwo;
35
ndi okhala pa dziko lapansi onse ayesedwa achabe; ndipo Iye achita mwa chifuniro chake m'khamu la kumwamba ndi mwa okhala pa dziko lapansi; ndipo palibe woletsa dzanja lake, kapena wakunena naye, Muchitanji?
36
Nthawi yomweyi nzeru zanga zinandibwerera, ndi chifumu changa ndi kunyezimira kwanga zinandibwerera, kuti uonekenso ulemerero wa ufumu wanga; ndi mandoda anga ndi akulu anga anandifuna; ndipo ndinakhazikika m'ufumu wanga, Iye nandionjezeranso ukulu wochuluka.
37
Tsono ine Nebukadinezara ndiyamika, ndi kukuza, ndi kulemekeza Mfumu ya Kumwamba, pakuti ntchito zake zonse nzoona, ndi njira zake chiweruzo; ndi oyenda m'kudzikuza kwao, Iye akhoza kuwachepetsa.
← Chapter 3
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 5 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12