bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
/
Ecclesiastes 1
Ecclesiastes 1
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 2 →
1
Mau a Mlaliki, mwana wa Davide, mfumu ya m'Yerusalemu.
2
Zachabechabe, ati Mlaliki; zachabechabe zonse ndi chabe.
3
Kodi ntchito zake zonse munthu asauka nazo zimpindulira chiyani?
4
Mbadwo wina upita, mbadwo wina nufika; koma dziko lingokhalabe masiku onse.
5
Inde dzuwa lituluka, nililowa, nilifulumira komwe linatulukako.
6
Kulowa kumwera ndi kuzungulira kumpoto zungulirezungulire imaomba mphepo; ibweranso monga mwa mazunguliridwe ake.
7
Mitsinje yonse ithira m'nyanja, koma nyanja yosadzala; komwe imukira mitsinjeyo, komweko ibweranso.
8
Zinthu zonse zilemetsa; munthu sakhoza kuzifotokoza; maso sakhuta m'kuona, ndi makutu sakhuta m'kumva.
9
Chomwe chinaoneka chidzaonekanso; ndi chomwe chinachitidwa chidzachitidwanso; ndipo palibe kanthu katsopano pansi pano.
10
Kodi pali kanthu unganene kuti, Taona katsopano aka? Kanalipo kale, kale lomwe tisanabadwe ife.
11
Zoyamba zija sizikumbukiridwa; ngakhale zomwe zilinkudzazo, omwe adzakhalabe m'tsogolomo, sadzazikumbukirai.
12
Ine Mlaliki ndinali mfumu ya Israele m'Yerusalemu.
13
Ndipo ndinapereka mtima kufunafuna ndi nzeru, ndi kulondetsa zonse zimachitidwa pansi pa thambo; ntchito yovuta imeneyi Mulungu apatsa ana a anthu akasauke nayo.
14
Ndaona ntchito zonse zipangidwa kunja kuno; ndipo zonsezo ndi chabe ndi kungosautsa mtima.
15
Chokhotakhota sichingaongokenso; ndipo choperewera sichingawerengedwe.
16
Ndinalankhula ndi mtima wanga, ndi kuti, Taona, ndakuza ndi kudzienjezera nzeru koposa onse anakhala m'Yerusalemu ndisanabadwe ine; inde mtima wanga wapenyera kwambiri nzeru ndi chidziwitso.
17
Ndipo ndinapereka mtima kudziwa nzeru ndi kudziwa misala ndi utsiru; ndinazindikira kuti ichinso chingosautsa mtima.
18
Pakuti m'nzeru yambiri muli chisoni chambiri; ndi yemwe aenjezera chidziwitso aenjezera zowawa.
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 2 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12