bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
/
Ecclesiastes 10
Ecclesiastes 10
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
← Chapter 9
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 11 →
1
Ntchentche zakufa zinunkhitsa moipa nizioletsa mafuta onunkhira a sing'anga; chomwecho kupusa kwapang'ono kuipitsa iye amene atchuka chifukwa cha nzeru ndi ulemu.
2
Wanzeru, mtima wake uli kudzanja lake lamanja; koma chitsiru, mtima wake kulamanzere.
3
Inde, poyendanso chitsiru panjira, nzeru yake imthera ndipo angoti kwa onse kuti, Ndine chitsiru.
4
Ngati mkulu akukwiyira, usasiye malo ako; chifukwa chifatso chipembedza utachimwa kwambiri.
5
Pali choipa ndachiona pansi pano, ngati kulakwa koyambira ndi mkulu;
6
utsiru ukhazikika pamwamba penipeni, ndipo olemera angokhala mwamanyazi.
7
Ndaona akapolo atakwera pa akavalo, ndi mafumu, alikuyenda pansi ngati akopolo.
8
Wokumba mbuna adzagwamo; ndipo woboola mpanda njoka idzamluma.
9
Wosendeza miyala adzaphwetekedwa nayo; wowaza nkhuni nadzitema.
10
Chitsulo chikakhala chosathwa, ndipo ukaleka kunola, uzipambana kulimbikira; koma nzeru ipindulira pochenjeza.
11
Njoka ikaluma isanalodzedwe, watsenga saona mphotho.
12
Mau a m'kamwa mwa munthu wanzeru nga chisomo; koma milomo ya chitsiru idzachimeza.
13
Chiyambi cha mau a m'kamwa mwake ndi utsiru; ndipo chimaliziro cha m'kamwa mwake ndi misala yoipa.
14
Chitsiru chichulukitsanso mau; koma munthu sadziwa chimene chidzaoneka; ndipo ndani angamuuze chomwe chidzakhala m'tsogolo mwake?
15
Ntchito ya zitsiru izitopetsa zonsezo, pakuti sichidziwa kunka kumudzi.
16
Tsoka kwa dzikowe, pamene mfumu yako ndiye mwana, ndipo akalonga ako adyera mamawa!
17
Mwai kwa dzikowe, pamene mfumu yako ndiye mwana wa aufulu, ndipo akalonga ako adya pa nthawi yoyenera akalimbe osati akaledzere ai.
18
Tsindwi litewa ndi mphwai za eni ake; nyumba nidontha ndi ulesi wa manja.
19
Amaphikira zakudya kuti asekere, vinyo nakondweretsa moyo; ndipo ndalama zivomera zonse.
20
Usatemberere mfumu ngakhale poganizira; usatemberere wolemera m'chipinda chogona iwemo; pakuti mbalame ya mlengalenga idzanyamula mauwo, ndipo chouluka ndi mapiko chidzamveketsa zonenazo.
← Chapter 9
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 11 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12