bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
/
Esther 1
Esther 1
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 2 →
1
Izi zinachitika masiku a Ahasuwero, ndiye Ahasuweroyo anachita ufumu kuyambira Indiya kufikira Kusi, pa maiko zana limodzi mphambu makumi awiri kudza asanu ndi awiri.
2
Masiku ajawo, pokhala Ahasuwero pa mpando wa ufumu wake uli m'chinyumba cha ku Susa,
3
chaka chachitatu cha ufumu wake, anakonzera madyerero akalonga ake onse, ndi omtumikira; amphamvu a Persiya ndi Mediya, omveka ndi akalonga a maikowo anakhala pamaso pake,
4
pamene anaonetsa zolemera za ufumu wake waulemu, ndi ulemerero wa ukulu wake woposa, masiku ambiri, ndiwo masiku zana limodzi mphambu makumi asanu ndi atatu.
5
Atatha masikuwa, mfumu inakonzera madyerero anthu onse okhala m'chinyumba cha ku Susa, akulu ndi ang'ono, masiku asanu ndi awiri, ku bwalo la munda wa maluwa wa ku chinyumba cha mfumu;
6
panali nsalu zolenjeka zoyera, zabiriwiri, ndi zamadzi, zomangika ndi zingwe za thonje labafuta, ndi lofiirira, pa zigwinjiri zasiliva, ndi nsanamira zansangalabwi; makama anali a golide ndi siliva pa mayalidwe a miyala yofiira, ndi yoyera, ndi yoyezuka, ndi yakuda.
7
Nawapatsa chakumwa m'zomwera zagolide, zomwerazo nzosiyanasiyana, ndi vinyo wachifumu anachuluka, monga mwa ufulu wa mfumu.
8
Ndi mamwedwewo anali monga mwa lamulo; panalibe kukakamiza; pakuti mfumu idaikira akulu onse a nyumba yake motero, kuti achite monga momwe akhumba aliyense.
9
Vasiti yemwe, mkazi wamkulu, anakonzera akazi madyerero m'nyumba yachifumu ya mfumu Ahasuwero.
10
Tsiku lachisanu ndi chiwiri, pokondwera mtima wa mfumu ndi vinyo, iye anauza Mehumani, Bizita, Haribona, Bigita, ndi Abagita, Zetara, ndi Karikasi, adindo asanu ndi awiriwo akutumikira pamaso pa mfumu Ahasuwero,
11
abwere naye Vasiti mkazi wamkulu pamaso pa mfumu ndi korona wachifumu, kuonetsa anthu ndi akulu kukoma kwake; popeza anali wokongola maonekedwe ake.
12
Koma Vasiti mkazi wamkuluyo anakana kudza pa mau a mfumu adamuuza adindowo; potero mfumu idapsa mtima ndithu, ndi mkwiyo wake unatentha m'kati mwake.
13
Pamenepo mfumu inanena kwa eni nzeru, akudziwa za m'tsogolo, mfumu idafotero nao onse akudziwa malamulo ndi maweruzo,
14
a pafupi naye ndiwo Karisena, Setara, Adimata, Tarisisi, Meresi, Marisena, ndi Memukana, akalonga asanu ndi awiri a Persiya ndi Mediya, openya nkhope ya mfumu ndi kukhala oyamba m'ufumu.
15
Anati, Tidzachitanji naye mkazi wamkulu Vasiti monga mwa malamulo, popeza sanachite chomuuza mfumu Ahasuwero mwa adindo?
16
Ndi Memukana anati, pamaso pa mfumu ndi akalonga, Vasiti mkazi wamkulu sanalakwire mfumu yekha, komanso akalonga onse, ndi mitundu yonse ya anthu okhala m'maiko onse a mfumu Ahasuwero.
17
Pakuti machitidwe awa a mkazi wamkuluyo adzabuka kufikira akazi onse, kupeputsa amuna ao pamaso pao; anthu akati, Mfumu Ahasuwero anati abwere naye Vasiti mkazi wamkulu pamaso pake, koma sanadze iye.
18
Inde tsiku lomwelo akazi akulu a Persiya ndi Mediya, atamva machitidwe a mkazi wamkuluyo, adzatero nao momwemo kwa akalonga onse a mfumu. Ndi chipeputso ndi mkwiyo zidzachuluka.
19
Chikakomera mfumu, atuluke mau achifumu pakamwa pake, nalembedwe m'malamulo a Apersiya ndi Amediya, angasinthike, kuti Vasiti asalowenso pamaso pa mfumu Ahasuwero; ndi mfumu aninkhe chifumu chake kwa mnzake womposa iye.
20
Ndipo mau amene adzaika mfumu akamveka m'ufumu wake wonse, (pakuti ndiwo waukulu), akazi onse adzachitira amuna ao ulemu, akulu ndi ang'ono.
21
Ndipo mauwo anakonda mfumu ndi akalonga; ndi mfumu inachita monga mwa mau a Memukana,
22
natumiza akalata kumaiko onse a mfumu, kudziko lililonse monga mwa chilembedwe chao, ndi kumtundu uliwonse monga mwa chinenedwe chao, kuti mwamuna aliyense akhale wamkulu m'nyumba yakeyake, nawabukitse monga mwa chinenedwe cha anthu a mtundu wake.
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 2 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10