bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
/
Esther 7
Esther 7
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
← Chapter 6
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 8 →
1
Motero inadza mfumu ndi Hamani kumwa naye mkazi wamkulu Estere.
2
Nitinso mfumu kwa Estere tsiku lachiwirili pa madyerero a vinyo, Pempho lanu nchiyani, mkazi wamkulu Estere? Lidzapatsidwa kwa inu; mufunanji? Chidzachitika, kufikira limodzi la magawo awiri a ufumu wanga.
3
Nayankha mkazi wamkulu Estere, nati, Ngati mwandikomera mtima, mfumu, ndipo chikakomera mfumu, andilekere moyo wanga pa kupempha kwanga, ndi wa anthu a mtundu wanga pa pempho langa;
4
pakuti tagulitsidwa; ine ndi anthu a mtundu wanga, kuti ationonge, atiphe, natipulule. Koma tikadagulitsidwa tikhale akapolo ndi adzakazi, ndikadakhala chete; chinkana wosautsa sakadakhoza kubwezera kusowa kwa mfumu.
5
Pamenepo mfumu Ahasuwero inalankhula, niti kwa mkazi wamkulu Estere, Ndani uyu, ali kuti iyeyu wadzazidwa mtima wake kuti azitero?
6
Nati Estere, Munthu wosautsa ndi mdani ndiye Hamani woipa uyu. Pamenepo Hamani anagwidwa mantha pamaso pa mfumu ndi mkazi wamkulu.
7
Ninyamuka mfumu mu mkwiyo wake ku madyerero a vinyo, nimka kumunda wa maluwa wa kuchinyumba; koma Hamani anatsalira kudzipempherera moyo kwa mkazi wamkulu Estere; popeza anapenya kuti mfumu inatsimikiza mtima kumchitira choipa.
8
Nibwera mfumu kumunda wa maluwa wa kuchinyumba kulowanso m'nyumba munali madyerero a vinyo, napeza Hamani atagwa pa kama wokhalapo Estere. Niti mfumu, Kodi aumiriza mkazi wamkulu pamaso panga m'nyumba? Potuluka mau pakamwa pa mfumu anamphimba Hamani nkhope.
9
Nati Haribona wina wa adindo okhala pamaso pa mfumu, Taonaninso, mtengowo msinkhu wake mikono makumi asanu, umene Hamani anaupangira Mordekai wonenera mfumu zokoma, uimiritsidwa m'nyumba ya Hamani. Niti mfumu, Mpachike pomwepo.
10
Nampachika Hamani pa mtengo adaukonzera Mordekai. Pamenepo mkwiyo wa mfumu unatsika.
← Chapter 6
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 8 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
Recommended Reading
Commentary
Esther Commentaries
→
Devotional
Esther Devotional Guide
→
Get This Bible
Chewa (Buku Lopatulika) Study Bible
→