bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
/
Ezra 1
Ezra 1
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 2 →
1
Chaka choyamba tsono cha Kirusi mfumu ya ku Persiya, kuti akwaniridwe mau a Yehova m'kamwa mwa Yeremiya, Yehova anautsa mzimu wa Kirusi, kuti abukitse mau m'ufumu wake wonse, nawalembenso, ndi kuti,
2
Atero Kirusi mfumu ya ku Persiya, Yehova Mulungu Wam'mwamba anandipatsa maufumu onse a pa dziko lapansi, nandilangiza ndimmangire nyumba m'Yerusalemu, ndiwo m'Yuda.
3
Aliyense mwa inu a anthu ake onse, Mulungu wake akhale naye, akwere kunka ku Yerusalemu, ndiwo m'Yuda, nakaimange nyumba ya Yehova Mulungu wa Israele; Iye ndiye Mulungu wokhala m'Yerusalemu.
4
Ndipo aliyense wotsala pamalo paliponse agonerapo iye, anthu a kumalo kwake amthandize ndi siliva, ndi golide, ndi zoweta, ndi chuma, pamodzi ndi nsembe yaufulu ya kwa nyumba ya Mulungu ili ku Yerusalemu.
5
Pamenepo ananyamuka akulu a nyumba za makolo a Yuda ndi Benjamini, ndi ansembe, ndi Alevi, ndiwo onse amene Mulungu adawautsira mzimu wao akwere kukamanga nyumba ya Yehova ili ku Yerusalemu.
6
Ndipo onse akuwazinga analimbitsa manja ao ndi zipangizo za siliva, ndi golide, ndi chuma, ndi zoweta, ndi zinthu za mtengo wake, pamodzi ndi nsembe zaufulu.
7
Kirusi mfumu anatulutsanso zipangizo za nyumba ya Yehova, zimene Nebukadinezara adazitulutsa m'Yerusalemu, ndi kuziika m'nyumba ya milungu yake;
8
zomwezi Kirusi mfumu ya ku Persiya anazitulutsa ndi dzanja la Mitiredati wosunga chumayo, naziwerengera Sezibazara kalonga wa Ayuda.
9
Kuwerenga kwake ndiko: mbale zagolide makumi atatu, mbale zasiliva chikwi chimodzi, mipeni makumi awiri mphambu isanu ndi inai;
10
zikho zagolide makumi atatu, zikho zasiliva zina mazana anai ndi khumi, zipangizo zina chikwi chimodzi.
11
Zipangizo zonse zagolide ndi zasiliva ndizo zikwi zisanu ndi mazana anai. Izi zonse Sezibazara anakwera nazo, pokwera andende aja kuchokera ku Babiloni kunka ku Yerusalemu.
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 2 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10