bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
/
Ezra 10
Ezra 10
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
← Chapter 9
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
1
Pakupemphera Ezara tsono, ndi kuwulula ndi kulira misozi, ndi kudzigwetsa pansi pakhomo pa nyumba ya Mulungu, udamsonkhanira mwa Israele msonkhano waukulu ndithu wa amuna, ndi akazi, ndi ana; popeza anthu analira kulira kwakukulu.
2
Pamenepo Sekaniya mwana wa Yehiyele, mwana wina wa Elamu, anambwezera Ezara mau, nati, Talakwira Mulungu wathu, tadzitengera akazi achilendo a mitundu ya dzikoli; koma tsopano chimtsalira Israele chiyembekezo kunena za chinthu ichi.
3
Ndipo tsono tipangane ndi Mulungu wathu kuchotsa akazi onse, ndi obadwa mwa iwo, monga mwa uphungu wa mbuye wanga, ndi wa iwo akunjenjemera pa lamulo la Mulungu wathu; ndipo chichitike monga mwa chilamulo.
4
Nyamukani, mlandu ndi wanu; ndipo ife tili nanu; limbikani, chitani.
5
Nanyamuka Ezara, nalumbiritsa akulu a ansembe, ndi Alevi, ndi Aisraele onse, kuti adzachita monga mwa mau awa. Nalumbira iwo.
6
Pamenepo Ezara ananyamuka pakhomo pa nyumba ya Mulungu, nalowa m'chipinda cha Yehohanani mwana wa Eliyasibu, ndipo atafikako sanadye mkate, sanamwe madzi; pakuti anachita maliro chifukwa cha kulakwa kwa iwo otengedwa ndende.
7
Nabukitsa iwo mau mwa Yuda ndi Yerusalemu kwa ana onse otengedwa ndende, kuti azisonkhana ku Yerusalemu;
8
ndi kuti aliyense wosafikako atapita masiku atatu, monga mwa uphungu wa akalonga ndi akulu, chuma chake chonse chidzaonongeka konse, ndipo iye adzachotsedwa kumsonkhano wa iwo otengedwa ndende.
9
Ndipo anasonkhana ku Yerusalemu amuna onse a Yuda ndi Benjamini asanapite masiku atatu, ndiwo mwezi wachisanu ndi chinai, tsiku la makumi awiri a mwezi; nakhala pansi anthu onse m'khwalala pakhomo pa nyumba ya Mulungu, alikunjenjemera chifukwa cha mlandu uwu, ndi chifukwa cha mvulayi.
10
Pamenepo Ezara wansembe ananyamuka, nanena nao, Mwalakwa, mwadzitengera akazi achilendo, kuonjezera kupalamula kwa Israele.
11
Chifukwa chake tsono, wululani kwa Yehova Mulungu wa makolo anu, nimuchite chomkondweretsa; mudzilekanitse ndi mitundu ya anthu a m'dzikomo, ndi kwa akazi achilendo.
12
Ndipo unayankha msonkhano wonse, ndi kunena ndi mau akulu, Monga mwa mau anu tiyenera kuchita.
13
Koma anthu ndiwo ambiri, ndi nyengo yino nja mvula, tilibenso mphamvu yakuima pabwalo, ndi ntchitoyi sindiyo ya tsiku limodzi kapena awiri; pakuti tachulukitsa kulakwa kwathu pa chinthu ichi.
14
Ayang'anire ichi tsono akalonga athu a msonkhano wonse, ndi onse a m'midzi mwathu amene anadzitengera akazi achilendo abwere pa nthawi zoikika, ndi pamodzi nao akulu a mudzi wao uliwonse, ndi oweruza ake, mpaka udzatichokera mkwiyo waukali wa Mulungu wathu chifukwa cha mlandu uwu.
15
Yonatani mwana wa Asahele ndi Yazeya mwana wa Tikiva okha anatsutsana nacho, ndi Mesulamu ndi Sabetai Mlevi anawathandiza.
16
Pamenepo anthu otengedwa ndende anachita chotero. Ndi Ezara wansembe, ndi anthu akulu a nyumba za makolo, monga mwa nyumba za makolo ao, iwo onse otchulidwa maina ao, anasankhidwa, nakhala pansi tsiku loyamba la mwezi wakhumi kufunsa za mlanduwu.
17
Natsiriza nao amuna onse adadzitengera akazi achilendo tsiku loyamba la mwezi woyamba.
18
Ndipo anapeza mwa ana a ansembe odzitengera akazi achilendo, ndiwo a ana a Yesuwa mwana wa Yozadaki, ndi abale ake Maaseiya, ndi Eliyezere, ndi Yaribu, ndi Gedaliya.
19
Ndipo anaimika dzanja lao kuti adzachotsa akazi ao; ndipo popeza adapalamuladi, anapereka nsembe nkhosa yamphongo ya zoweta pa kupalamula kwao.
20
Ndi a ana a Imeri: Hanani ndi Zebadiya.
21
Ndi a ana a Harimu: Maaseiya, ndi Eliya, ndi Semaya, ndi Yehiyele, ndi Uziya.
22
Ndi a ana a Pasuri: Eliyoenai, Maaseiya, Ismaele, Netanele, Yozabadi, ndi Elasa.
23
Ndi a Alevi: Yozabadi, ndi Simei, ndi Kelaya (ndiye Kelita), Petahiya, Yuda, ndi Eliyezere.
24
Ndi a oimbira: Eliyasibu; ndi a odikira: Salumu, ndi Telemu, ndi Uri.
25
Ndi Aisraele a ana a Parosi: Ramiya, ndi Iziya, ndi Matikiya, ndi Miyamini, ndi Eleazara, ndi Malikiya, ndi Benaya.
26
Ndi a ana a Elamu: Mataniya, Zekariya, ndi Yehiyele, ndi Abidi, ndi Yeremoti, ndi Eliya.
27
Ndi a ana a Zatu: Eliyoenai, Eliyasibu, Mataniya, ndi Yeremoti, ndi Zabadi, ndi Aziza.
28
Ndi a ana a Bebai: Yehohanani, Hananiya, Zabai, Atilai.
29
Ndi a ana a Bani: Mesulamu, Maluki, ndi Adaya, Yasubu, ndi Seyala, Yeremoti.
30
Ndi a ana a Pahatimowabu: Adina, ndi Kelali, Benaya, Maaseiya, Mataniya, Bezalele, ndi Binuyi, ndi Manase.
31
Ndi a ana a Harimu: Eliyezere, Isiya, Malikiya, Semaya, Simeoni,
32
Benjamini, Maluki, Semariya.
33
A ana a Hasumu: Matenai, Matata. Zabadi, Elifeleti, Yeremai, Manase, Simei.
34
A ana a Bani: Maadai, Amuramu, ndi Uwele,
35
Benaya, Bedeiya, Keluhu,
36
Vaniya, Meremoti, Eliyasibu,
37
Mataniya, Matenai, ndi Yasu,
38
ndi Bani, ndi Binuyi, Simei,
39
ndi Selemiya, ndi Natani, ndi Adaya,
40
Makinadebai, Sasai, Sarai,
41
Azarele, ndi Selemiya, Semariya,
42
Salumu, Amariya, Yosefe.
43
A ana a Nebo: Yeiyele, Matitiya, Zabadi, Zebina, Yadai, ndi Yowele, Benaya.
44
Awa onse adatenga akazi achilendo, ndi ena a iwowa anali ndi akazi amene adawabalira ana.
← Chapter 9
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10