bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
/
Galatians 1
Galatians 1
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 2 →
1
Paulo, mtumwi (wosachokera kwa anthu, kapena mwa munthu, koma mwa Yesu Khristu, ndi Mulungu Atate, amene anamuukitsa Iye kwa akufa),
2
ndi abale onse amene ali pamodzi ndi ine, kwa Mipingo ya ku Galatiya:
3
Chisomo kwa inu, ndi mtendere wa kwa Mulungu Atate, ndi Ambuye wathu Yesu Khristu,
4
amene anadzipereka yekha chifukwa cha machimo athu, kuti akatilanditse ife m'nyengo ya pansi pano yino yoipa, monga mwa chifuniro cha Mulungu ndi Atate wathu;
5
yemweyo akhale nao ulemerero kunthawi za nthawi. Amen.
6
Ndizizwa kuti msanga motere mulikupatuka kwa iye amene anakuitanani m'chisomo cha Khristu, kutsata Uthenga Wabwino wina;
7
umene suli wina; koma pali ena akuvuta inu, nafuna kuipsa Uthenga Wabwino wa Khristu.
8
Koma ngakhale ife, kapena mngelo wochokera Kumwamba, ngati akakulalikireni Uthenga Wabwino wosati umene tidakulalikirani ife, akhale wotembereredwa.
9
Monga tinanena kale, ndipo ndinenanso tsopano apa, ngati wina akulalikirani Uthenga Wabwino wosati umene mudaulandira, akhale wotembereredwa.
10
Pakuti kodi ndikopa anthu tsopano, kapena Mulungu? Kapena kodi ndifuna kukondweretsa anthu? Ndikadakhala wokondweretsabe anthu, sindikadakhala kapolo wa Khristu.
11
Pakuti ndikudziwitsani inu, abale, za Uthenga Wabwinowo wolalikidwa ndi ine, kuti suli monga mwa anthu.
12
Pakutitu sindinaulandira kwa munthu, kapena sindinauphunzira, komatu unadza mwa vumbulutso la Yesu Khristu.
13
Pakuti mudamva za makhalidwe anga kale mwa Chiyuda, kuti ndinalondalonda Mpingo wa Mulungu koposa, ndi kuupasula,
14
ndipo ndinawaposa ndi kutsogola mwa Chiyuda ambiri a msinkhu wanga mwa mtundu wanga, ndipo ndinakhala wachangu koposa pa miyambo ya makolo anga.
15
Koma pamene padakondweretsa Mulungu, amene anandipatula, ndisanabadwe, nandiitana ine mwa chisomo chake,
16
kuti avumbulutse Mwana wake mwa ine, kuti ndimlalikire Iye mwa amitundu; pomwepo sindinafunsana ndi thupi ndi mwazi:
17
kapena kukwera kunka ku Yerusalemu sindinankako kwa iwo amene anakhala atumwi ndisanakhale mtumwi ine, komatu ndinamuka ku Arabiya, ndipo ndinabweranso ku Damasiko.
18
Pamenepo patapita zaka zitatu, ndinakwera kunka ku Yerusalemu kukazindikirana naye Kefa, ndipo ndinakhala kwa iye masiku khumi ndi asanu.
19
Koma wina wa atumwi sindinamuona, koma Yakobo mbale wa Ambuye.
20
Ndipo izi ndikulemberani inu, taonani, pamaso pa Mulungu sindinama ine.
21
Pamene ndinadza kumbali za Siriya ndi Silisiya.
22
Koma ndinali wosadziwika nkhope yanga kwa Mipingo ya ku Yudeya ya mwa Khristu;
23
koma analinkumva kokha, kuti, Iye wakutilondalonda ife kale, tsopano alalikira chikhulupirirocho adachipasula kale;
24
ndipo analemekeza Mulungu mwa ine.
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 2 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6