bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
/
Galatians 4
Galatians 4
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
← Chapter 3
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 5 →
1
Koma ndinena kuti, pokhala wolowa nyumba ali wakhanda, sasiyana ndi kapolo, angakhale ali mwini zonse;
2
komatu ali wakumvera omsungira ndi adindo, kufikira nthawi yoikika kale ndi atate wake.
3
Koteronso ife, pamene tinali akhanda, tinali akapolo akumvera miyambo ya dziko lapansi;
4
koma pokwaniridwa nthawi, Mulungu anatuma Mwana wake, wobadwa ndi mkazi, wobadwa wakumvera lamulo,
5
kuti akaombole iwo akumvera lamulo, kuti ife tikalandire umwana.
6
Ndipo popeza muli ana, Mulungu anatumiza Mzimu wa Mwana wake alowe m'mitima yathu, wofuula Abba! Atate!
7
Kotero kuti sulinso kapolo, koma mwana; koma ngati mwana, wolowa nyumbanso mwa Mulungu.
8
Komatu pajapo, posadziwa Mulungu inu, munachitira ukapolo iyo yosakhala milungu m'chibadwidwe chao;
9
koma tsopano, podziwa Mulungu inu, koma makamaka podziwika ndi Mulungu, mubwereranso bwanji kutsata miyambo yofooka ndi yaumphawi, imene mufuna kubwerezanso kuichitira ukapolo?
10
Musunga masiku, ndi miyezi, ndi nyengo, ndi zaka.
11
Ndiopera inu, kuti kapena ndadzivutitsa ndi inu chabe.
12
Abale, ndikupemphani, khalani monga ine, pakuti inenso ndili monga inu. Simunandichitira choipa ine;
13
koma mudziwa kuti m'kufooka kwa thupi ndinakulalikirani Uthenga Wabwino poyamba:
14
ndipo chija cha m'thupi langa chakukuyesani inu simunachipeputsa, kapena sichinakunyansirani, komatu munandilandira ine monga mngelo wa Mulungu, monga Khristu Yesu mwini.
15
Pamenepo thamo lanu lili kuti? Pakuti ndikuchitirani inu umboni, kuti, kukadatheka, mukadakolowola maso anu ndi kundipatsa ine.
16
Kotero kodi ndasanduka mdani wanu, pakukunenerani zoona?
17
Achita changu pa inu koma si kokoma ai, komatu afuna kukutsekerezani inu kunja, kuti mukawachitire iwowa changu.
18
Koma nkwabwino kuchita changu m'zabwino nthawi zonse, si pokhapokha pokhala nanu pamodzi ine.
19
Tiana tanga, amene ndilikumvanso zowawa za kubala inu, kufikira Khristu aumbika mwa inu,
20
koma mwenzi nditakhala nanu tsopano, ndi kusintha mau anga; chifukwa ndisinkhasinkha nanu.
21
Ndiuzeni, inu akufuna kukhala omvera lamulo, kodi simukumva chilamulo?
22
Pakuti palembedwa, kuti Abrahamu anali nao ana amuna awiri, mmodzi wobadwa mwa mdzakazi, ndi mmodzi wobadwa mwa mfulu.
23
Komatu uyo wa mdzakazi anabadwa monga mwa thupi; koma iye wa mfuluyo, anabadwa monga mwa lonjezano. Izo ndizo zophiphiritsa;
24
pakuti akaziwa ali mapangano awiri, mmodzi wa kuphiri la Sinai, akubalira ukapolo, ndiye Hagara.
25
Koma Hagara ndiye phiri la Sinai, m'Arabiya, nafanana ndi Yerusalemu wa tsopano; pakuti ali muukapolo pamodzi ndi ana ake.
26
Koma Yerusalemu wa kumwamba uli waufulu, ndiwo amai wathu.
27
Pakuti kwalembedwa, Kondwera, chumba iwe wosabala; imba nthungululu, nufuule iwe wosamva kuwawa kwa kubala; pakuti ana ake a iye ali mbeta achuluka koposa ana a iye ali naye mwamuna.
28
Koma ife, abale, monga Isaki, tili ana a lonjezano.
29
Komatu monga pompaja iye wobadwa monga mwa thupi anazunza wobadwa monga mwa Mzimu, momwemonso tsopano.
30
Koma lembo linena chiyani? Taya kubwalo mdzakazi ndi mwana wake, pakuti sadzalowa nyumba mwana wa mdzakazi pamodzi ndi mwana wa mfulu.
31
Chifukwa chake, abale, sitili ana a mdzakazi, komatu a mfulu.
← Chapter 3
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 5 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6