bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
/
James 2
James 2
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
← Chapter 1
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 3 →
1
Abale anga, pakuti muli nacho chikhulupiriro cha Ambuye wathu Yesu Khristu, Ambuye wa ulemerero, musakhale okondera ndi kusamala maonekedwe.
2
Pakuti akalowa m'sunagoge mwanu munthu wovala mphete yagolide, ndi chovala chokometsetsa, ndipo akalowanso munthu wosauka ndi chovala chodetsa;
3
ndipo mukapenyerera iye wovala chokometsetsa, nimukati naye, Inu mukhale apa pabwino; ndipo mukati kwa wosaukayo, Iwe, imauko, kapena, khala pansi pa mpando wa mapazi anga;
4
kodi simunasiyanitsa mwa inu nokha, ndi kukhala oweruza oganizira zoipa?
5
Mverani, abale anga okondedwa; kodi Mulungu sanasankha osauka a dziko lapansi akhale olemera ndi chikhulupiriro, ndi olowa nyumba a ufumu umene adaulonjeza kwa iwo akumkonda Iye?
6
Koma inu mumanyoza munthu wosauka. Kodi sakusautsani inu achuma, nakukokerani iwowa kumabwalo a milandu?
7
Kodi sachitira mwano iwowa dzina lokomali muitanidwa nalo?
8
Koma ngati muchita chikwanirire lamulolo lachifumu, monga mwa malembo, Uzikonda mnzako monga udzikonda wekha, muchita bwino:
9
koma ngati musamala maonekedwe, muchita uchimo, ndipo mutsutsidwa ndi chilamulo monga olakwa.
10
Pakuti amene aliyense angasunge malamulo onse, koma akakhumudwa pa limodzi, iyeyu wachimwira onse.
11
Pakuti Iye wakuti, Usachite chigololo, anatinso, Usaphe. Ndipo ukapanda kuchita chigololo, koma ukapha, wakhala wolakwira lamulo.
12
Lankhulani motero, ndipo chitani motero, monga anthu amene adzaweruzidwa ndi lamulo la ufulu.
13
Pakuti chiweruziro chilibe chifundo kwa iye amene sanachita chifundo; chifundo chidzitamandira kutsutsana nacho chiweruziro.
14
Chipindulo chake nchiyani, abale anga, munthu akanena, Ndili nacho chikhulupiriro, koma alibe ntchito? Kodi chikhulupirirocho chikhoza kumpulumutsa?
15
Mbale kapena mlongo akakhala wausiwa, nichikamsowa chakudya cha tsiku lake,
16
ndipo wina wa inu akanena nao, Mukani ndi mtendere, mukafunde ndi kukhuta; osawapatsa iwo zosowa za pathupi; kupindula kwake nchiyani?
17
Momwemonso chikhulupiriro, chikapanda kukhala nacho ntchito, chikhala chakufa m'kati mwakemo.
18
Koma wina akati, Iwe uli nacho chikhulupiriro, ndipo ine ndili nazo ntchito; undionetse ine chikhulupiriro chako chopanda ntchito zako, ndipo ine ndidzakuonetsa iwe chikhulupiriro changa chotuluka m'ntchito zanga.
19
Ukhulupirira iwe kuti Mulungu ali mmodzi; uchita bwino; ziwanda zikhulupiriranso, ndipo zinthunthumira.
20
Koma ufuna kuzindikira kodi, munthu wopanda pake iwe, kuti chikhulupiriro chopanda ntchito chili chabe?
21
Abrahamu kholo lathu, sanayesedwa wolungama ndi ntchito kodi, paja adapereka mwana wake Isaki nsembe pa guwa la nsembe?
22
Upenya kuti chikhulupiriro chidachita pamodzi ndi ntchito zake, ndipo motuluka mwa ntchito chikhulupiriro chidayesedwa changwiro;
23
ndipo anakwaniridwa malembo onenawa, Ndipo Abrahamu anakhulupirira Mulungu, ndipo kudawerengedwa kwa iye chilungamo; ndipo anatchedwa bwenzi la Mulungu.
24
Mupenya kuti munthu ayesedwa wolungama ndi ntchito yake, osati ndi chikhulupiriro chokha.
25
Ndipo momwemonso sanayesedwa wolungama Rahabu mkazi wa damayo ndi ntchito kodi, popeza adalandira amithenga, nawatulutsa adzere njira ina?
26
Pakuti monga thupi lopanda mzimu lili lakufa, koteronso chikhulupiriro chopanda ntchito chili chakufa.
← Chapter 1
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 3 →
All chapters:
1
2
3
4
5