bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
/
James 4
James 4
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
← Chapter 3
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 5 →
1
Zichokera kuti nkhondo, zichokera kuti zolimbana mwa inu? Kodi sizichokera kuzikhumbitso zanu zochita nkhondo m'ziwalo zanu?
2
Mulakalaka, ndipo zikusowani; mukupha, nimuchita kaduka, ndipo simukhoza kupeza; mulimbana, nimuchita nkhondo; mulibe kanthu, chifukwa simupempha.
3
Mupempha, ndipo simulandira, popeza mupempha koipa, kuti mukachimwaze pochita zikhumbitso zanu.
4
Akazi achigololo inu, kodi simudziwa kuti ubwenzi wa dziko lapansi uli udani ndi Mulungu? Potero, iye amene afuna kukhala bwenzi la dziko lapansi adziika mdani wa Mulungu.
5
Kodi muyesa kapena kuti malembo angonena chabe? Kodi Mzimuyo adamkhalitsa mwa ife akhumbitsa kuchita nsanje?
6
Koma apatsa chisomo choposa. Potero anena malembo, Mulungu akaniza odzikuza, koma apatsa chisomo odzichepetsa.
7
Potero mverani Mulungu; koma kanizani mdierekezi, ndipo adzakuthawani inu.
8
Yandikirani kwa Mulungu, ndipo adzayandikira kwa inu. Sambani m'manja, ochimwa inu; yeretsani mitima, a mitima iwiri inu.
9
Khalani osautsidwa, lirani, lirani misozi; kuseka kwanu kusanduke kulira, ndi chimwemwe chanu chisanduke chisoni.
10
Dzichepetseni pamaso pa Ambuye, ndipo adzakukwezani.
11
Musamanenerana, abale. Wonenera mbale, kapena woweruza mbale wake, anenera lamulo, naweruza lamulo: koma ngati uweruza lamulo, suli wochita lamulo, komatu woweruza.
12
Woika lamulo ndi woweruza ndiye mmodzi, ndiye amene akhoza kupulumutsa ndi kuononga; koma iwe woweruza mnzako ndiwe yani?
13
Nanga tsono, inu akunena, Lero kapena mawa tidzapita kulowa kumudzi wakutiwakuti, ndipo tidzagonerako ndi kutsatsa malonda, ndi kupindula nao;
14
inu amene simudziwa chimene chidzagwa mawa. Moyo wanu uli wotani? Pakuti muli utsi, wakuonekera kanthawi, ndi pamenepo ukanganuka.
15
Mukadanena inu, Akalola Mulungu, ndipo tikakhala ndi moyo, tidzachita kakutikakuti.
16
Koma tsopano mudzitamandira m'kudzikuza kwanu; kudzitamandira kulikonse kotero nkoipa.
17
Potero kwa iye amene adziwa kuchita bwino, ndipo sachita, kwa iye kuli tchimo.
← Chapter 3
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 5 →
All chapters:
1
2
3
4
5