bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
/
Jonah 3
Jonah 3
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
← Chapter 2
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 4 →
1
Ndipo mau a Yehova anadza kwa Yona nthawi yachiwiri, ndi kuti,
2
Nyamuka, pita ku Ninive mudzi waukulu uja, nuulalikire uthenga umene ndikuuza.
3
Ndipo Yona ananyamuka, napita ku Ninive, monga mwa mau a Yehova. Koma Ninive ndiwo mudzi waukulu pamaso pa Yehova, wa ulendo wa masiku atatu.
4
Ndipo Yona anayamba kulowa mudziwo ulendo wa tsiku limodzi, nalalikira, nati, Atsala masiku makumi anai ndipo Ninive adzapasuka.
5
Ndipo anthu a Ninive anakhulupirira Mulungu, nalalikira chosala, navala chiguduli, kuyambira wamkulu kufikira wamng'ono wa iwowa.
6
Pakuti mau awa anafikira mfumu ya Ninive, ndipo inanyamuka kumpando wake wachifumu, nivula chofunda chake, nifunda chiguduli, nikhala m'maphulusa.
7
Ndipo analalikira, nanena m'Ninive mwa lamulo la mfumu ndi nduna zake, ndi kuti, Ngakhale munthu kapena nyama, ngakhale ng'ombe kapena nkhosa, zisalawe kanthu, zisadye, zisamwe madzi;
8
koma zifundidwe ndi chiguduli munthu ndi nyama, nizifuulire kolimba kwa Mulungu; ndipo abwere yense kuleka njira yake yoipa, ndi chiwawa chili m'manja mwake.
9
Kaya, akatembenuka Mulungu, ndi kuleka kubwera ku mkwiyo wake waukali, kuti tisatayike.
10
Ndipo Mulungu anaona ntchito zao, kuti anabwera kuleka njira yao yoipa; ndipo Mulungu analeka choipa adanenachi kuti adzawachitira, osachichita.
← Chapter 2
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 4 →
All chapters:
1
2
3
4