bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
/
Jonah 4
Jonah 4
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
← Chapter 3
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
1
Koma sikudakomera Yona konse, ndipo anapsa mtima.
2
Ndipo anapemphera kwa Yehova, nati, Ha, Yehova! Si ndiwo mau anga ndikali m'dziko langa? Chifukwa chake ndinafulumira kuthawira ku Tarisisi, pakuti ndinadziwa kuti Inu ndinu Mulungu wachisomo ndi wodzala chifundo, wolekerera ndi wokoma mtima mochuluka, ndi woleka choipacho.
3
Ndipo tsopano, Yehova, mundichotseretu moyo wanga, kundikomera ine kufa, osakhala ndi moyo ai.
4
Ndipo Yehova anati, Uyenera kupsa mtima kodi?
5
Pamenepo Yona anatuluka m'mudzi, nakhala pansi kum'mawa kwa mudzi, nadzimangira komweko thandala, nakhala pansi pake mumthunzi mpaka adzaona chochitikira mudzi.
6
Ndipo Yehova Mulungu anaikiratu msatsi, naumeretsera Yona, uchite mthunzi pamutu pake, kumlanditsa m'nsautso yake. Ndipo Yona anakondwera kwambiri chifukwa cha msatsiwo.
7
Koma Mulungu anauikira mphanzi pakucha m'mawa mwake, ndiyo inadya msatsi, nufota.
8
Ndipo kunali, potuluka dzuwa Mulungu anaika mphepo ya kum'mawa yotentha, ndipo dzuwa linatentha mutu wake wa Yona, nalefuka iye, nadzipempherera kuti afe; nati, Kundikomera ine kufa, kukhala ndi moyo ai.
9
Ndipo Mulungu anati kwa Yona, Uyenera kodi kupsa mtima chifukwa cha msatsiwo? Nati iye, Ee, kundiyenera ine kupsa mtima mpaka imfa.
10
Ndipo Yehova anati, Unachitira chifundo msatsiwo umene sunagwirapo ntchito, kapena kuumeretsa, umene unamera usiku, nutha usiku;
11
ndipo sindiyenera Ine kodi kuchitira chifundo Ninive mudzi waukulu uwu; m'mene muli anthu oposa zikwi zana limodzi mphambu zikwi makumi awiri osadziwa kusiyanitsa pakati pa dzanja lao lamanja ndi lamanzere, ndi zoweta zambiri zomwe?
← Chapter 3
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
All chapters:
1
2
3
4