bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
2 Peter 1
2 Peter 1
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 2 →
1
Ndine, Simoni Petro, mtumiki ndi mtumwi wa Yesu Khristu. Ndikulemba kalatayi kwa anthu amene adalandira chikhulupiriro chomwe ifenso tidalandirako. Iwonso adachilandira chifukwa cha chilungamo cha Mulungu ndi Mpulumutsi wathu Yesu Khristu.
2
Mulungu akukomereni mtima ndi kukupatsani mtendere wochuluka, pakumdziŵa Iyeyo ndiponso Yesu Ambuye athu.
3
Mulungu mwa mphamvu zake adatipatsa zonse zotithandiza kukhala ndi moyo ndiponso opembedza, pakutidziŵitsa za Iyeyo amene adatiitana ku ulemerero ndi ubwino wake woposa.
4
Mwa ulemerero ndi ubwino wakewo adatipatsa madalitso aakulu ndi amtengowapatali amene Iye adatilonjeza. Adatero kuti mulandireko moyo wake wa Mulungu, mutapulumuka ku chivunde chimene chili pa dziko lapansi chifukwa cha zilakolako zoipa.
5
Tsono muyesetse kuchita khama kuwonjezera makhalidwe abwino pa chikhulupiriro chanu, ndi nzeru zoona pa makhalidwe anu abwinowo.
6
Muwonjezerepo kudziletsa pa nzeru zoonazo, kulimbika pa kudziletsa kwanu, ndiponso kupembedza Mulungu pa kulimbika kwanuko.
7
Pa kupembedzapo muwonjezerepo chifundo chachibale, ndipo pa chifundo chachibalecho muwonjezepo chikondi.
8
Ngati zonsezi zikhala mwa inu, nkumachuluka, simudzakhala olephera ndi opanda phindu pa nzeru zodziŵira Ambuye athu Yesu Khristu.
9
Paja munthu wopanda zimenezi ndiye kuti ngwakhungu, sangathe kuwona patali, ndipo waiŵala kuti adamtsuka machimo ake akale.
10
Nchifukwa chake abale, chitani changu koposa kale kutsimikiza kuti Mulungu adakuitanani ndipo adakusankhani. Mukatero simudzagwa konse.
11
Choncho adzakutsekulirani kwathunthu khomo loloŵera mu Ufumu wosatha wa Ambuye athu ndi Mpulumutsi wathu, Yesu Khristu.
12
Nchifukwa chake cholinga changa nchakuti ndizikukumbutsani zimenezi nthaŵi zonse, ngakhale mukuzidziŵa ndipo mumakhulupirira ndi mtima wonse choona chimene mudalandira.
13
Ndiyesa nkoyenera kuti, ndikadali mu msasa uno, nditsitsimutse mitima yanu pakukukumbutsani zimenezi.
14
Pakuti ndikudziŵa kuti nthaŵi yakutuluka mu msasa wanga uno yayandikira, monga andidziŵitsira Ambuye athu Yesu Khristu.
15
Ndipo ndidzayesetsa kukonza zoti nditachoka ine, muzidzatha kuzikumbukira zimenezi nthaŵi iliyonse.
16
Ife sitidatsate nthano zongopeka chabe, pamene tidakudziŵitsani za mphamvu zao ndi za kubweranso kwao kwa Ambuye athu Yesu Khristu. Koma tidachita kuuwona ndi maso athu ukulu wake.
17
Iye adalandira ulemu ndi ulemerero kwa Mulungu Atate, ndipo adamufikira mau ochokera kwa Atate aulemererowo akuti, “Uyu ndi Mwana wanga wokondedwa, amene ndimakondwera naye.”
18
Ndipo mau ameneŵa ifeifeyo tidaŵamva kuchokera kumwamba chifukwa tidaali naye pamodzi pa phiri loyera lija.
19
Motero tikudziŵa ndithu tsopano kuti mau aja a anereriŵa ngoona. Nkwabwino tsono kuti muŵayang'anitsitse ngati nyale yoŵala m'malo amdima, kufikira nthaŵi imene kudzayambe kucha, pamene nyenyezi yam'mamaŵa idzayambe kuŵala m'mitima mwanu.
20
Koma choyamba mumvetse kuti munthu payekha sangathe kumasulira mau a aneneri olembedwa m'Malembo.
21
Paja mau a aneneri sadadze konse ndi kufuna kwa munthu yekha, koma Mzimu Woyera adaŵalankhulitsa mau ochokera kwa Mulungu.
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 2 →
All chapters:
1
2
3
Recommended Reading
Commentary
2 Peter Commentaries
→
Devotional
2 Peter Devotional Guide
→
Get This Bible
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa) Study Bible
→