bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
2 Peter 3
2 Peter 3
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 2
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
1
Inu okondedwa, kalata ndikukulemberaniyi ndi yachiŵiri. M'makalata aŵiri onseŵa ndafuna kuutsa mitima yanu kuti mukhale ndi maganizo oona.
2
Kumbukirani mau amene aneneri oyera adanena kale, ndiponso lamulo la Ambuye ndi Mpulumutsi wathu limene atumwi adakupatsani.
3
Choyamba mumvetse izi: pa masiku otsiriza kudzafika anthu olalata, otsata zilakolako zao zoipa.
4
Azidzalalata nkumanena kuti, “Kodi suja Ambuye adalonjeza kuti adzabweranso? Nanga ali kuti? Lija nkale adamwalira makolo athu, koma zonse zili monga momwe Mulungu adazilengera poyamba paja.”
5
Apa akuiŵala dala kuti kalelo Mulungu atanena mau, zakuthambo zidalengedwa, ndipo dziko lapansi lidapangidwa ndi madzi kufumira m'madzi.
6
Ndipo ndi madzi okhaokhawo dziko lapansi la masiku amenewo lidamizidwa ndi kuwonongedwa.
7
Koma Mulungu ndi mau omwe aja adasunga zakuthambo ndi dziko lapansi la masiku ano kuti adzazitenthe ndi moto. Akuzisunga kufikira tsiku limene adzaweruza ndi kuwononga anthu onse osasamala za Iye.
8
Koma inu okondedwa, chinthu chimodzi musaiŵale, kuti pamaso pa Ambuye tsiku limodzi lili ngati zaka chikwi chimodzi, ndipo zaka chikwi chimodzi zili ngati tsiku limodzi.
9
Sikuti akuzengereza kuchita zimene adalonjeza, monga m'mene ena amaganizira, koma akukulezerani mtima. Safuna kuti ena aonongedwe, koma afuna kuti onse atembenuke mtima.
10
Koma tsiku la Ambuye lidzafika ngati mbala. Pa tsikulo zakumwamba zidzatha ndi phokoso loopsa. Zinthu zonse zidzayaka moto nkusungunuka, ndipo dziko lapansi ndi zonse zili m'menemo zidzapseratu.
11
Popeza kuti zonsezi zidzasungunuka motero, nanga simuyenera kukhala anthu angwiro m'makhalidwe anu ndiponso osamala za Mulungu?
12
Muziyembekeza tsiku la Ambuye ndi kugwira ntchito zofulumizitsa kudza kwake. Pa tsikulo zakumwamba zidzayaka moto ndi kusungunuka, ndipo zinthu zonse nazonso zidzasungunukira m'motomo.
13
Koma potsata lonjezo la Mulungu, tikudikira kumwamba kwatsopano ndi dziko lapansi latsopano, m'mene chilungamo chizidzakhalamo.
14
Choncho inu okondedwa, popeza kuti mukudikira zimenezi, muzichita changu kuti Ambuye adzakupezeni muli opanda banga kapena chilema ndiponso muli pa mtendere ndi Ambuyewo.
15
Zindikirani kuti Ambuye athu akukulezerani mtima kuti mupulumuke. Paulo, mbale wathu wokondedwa uja, nayenso adakulemberani za zimenezi ndi nzeru zimene Mulungu adampatsa.
16
Paja amanena chimodzimodzi m'makalata ake onse polemba za zimenezi. M'makalatamo muli zina zapatali kuzimvetsa, ndipo anthu osaphunzira ndi a nzeru zosakhazikika amazipotoza, monga amapotozeranso Malembo ena. Pakutero akungodziwononga okha.
17
Tsono inu okondedwa, popeza kuti mwazidziŵiratu zimenezi, chenjerani kuti zolakwa za anthu ochimwa zingakusokeretseni ndipo mungagwedezeke kenaka nkugwa.
18
Koma mukule m'chifundo ndi m'nzeru za Yesu Khristu, Ambuye athu ndi Mpulumutsi wathu. Iye akhale ndi ulemerero tsopano ndi mpaka muyaya. Amen.
← Chapter 2
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
All chapters:
1
2
3