bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
2 Thessalonians 1
2 Thessalonians 1
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 2 →
1
Ndife, Paulo, Silivano ndi Timoteo. Tikulembera mpingo wa ku Tesalonika, umene uli wake wa Mulungu Atate, ndiponso wa Ambuye Yesu Khristu.
2
Mulungu Atate ndi Ambuye Yesu Khristu akukomereni mtima ndi kukupatsani mtendere.
3
Tiyenera kuthokoza Mulungu nthaŵi zonse chifukwa cha inu, abale. Nkoyeneradi kutero, chifukwa chikhulupiriro chanu chikunka chikukulirakulira kwambiri pamodzi ndi kukondana kwanu pakati pa inu nonse.
4
Nchifukwa chake ife timakunyadirani, m'mipingo yonse ya Mulungu, chifukwa cha kulimbika kwanu ndi chikhulupiriro chanu pakati pa masautso ndi mazunzo onse amene adakugwerani.
5
Zonsezi zikutsimikiza kuti Mulungu amaweruza molungama. Cholinga chake nchakuti inu mupezeke oyenera kuloŵa mu Ufumu wa Mulungu umene mukuusaukira tsopano.
6
Paja Mulungu mwa chilungamo chake, adzaŵalanga ndi masautso anthu amene amakusautsani inu.
7
Koma inu amene mukusauka tsopano, adzakupatsani mpumulo pamodzi ndi ife tomwe. Adzachita zimenezi, Ambuye Yesu akadzabwera kuchokera Kumwamba pamodzi ndi angelo ake amphamvu.
8
Adzabwera ndi moto woyaka, nadzalanga anthu amene sadziŵa Mulungu, ndi amene sadamvere Uthenga Wabwino wa Ambuye athu Yesu.
9
Chilango chao nchakuti adzaonongedwa kwamuyaya, sadzaona konse nkhope ya Ambuye kapena ulemerero wa mphamvu zake,
10
pa tsiku limene Iye adzabwera kuti alemekezedwe mwa oyera, ndipo alandire ulemu mwa onse omkhulupirira. Ndipotu inunso mudzakhala nawo, chifukwa mudakhulupirira umboni wathu.
11
Nchifukwa chake timakupemphererani nthaŵi zonse, kuti Mulungu wathu akusandutseni oyenera moyo umene Iye adakuitanirani. Timapemphanso kuti ndi mphamvu zake akulimbikitseni kuchita zabwino zonse zimene mumalakalaka kuzichita, ndiponso ntchito zotsimikizira chikhulupiriro chanu.
12
Motero dzina la Ambuye athu Yesu lidzalemekezedwa mwa inu, ndipo inu mudzalemekezedwa mwa Iye. Zonsezi zidzachitika chifukwa cha kukoma mtima kwa Mulungu wathu ndi kwa Ambuye Yesu Khristu.
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 2 →
All chapters:
1
2
3