bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
2 Thessalonians 3
2 Thessalonians 3
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 2
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
1
Potsiriza, abale, mutipempherere kuti mau a Ambuye afalikire msanga, ndipo anthu aŵalandire mauwo mwaulemu, monga momwe mudachitira inu.
2
Mupempherenso kuti Mulungu atipulumutse kwa anthu ovuta ndi oipa, pakuti si onse ali ndi chikhulupiriro.
3
Koma Ambuye ngokhulupirika, ndipo adzakulimbitsani mtima ndi kukutchinjirizani kwa Woipa uja.
4
Ambuye amatipatsa chikhulupiriro chakuti mukuchita zonse zimene timakuuzani, ndipo kuti mudzazichitabe.
5
Ambuye aongolere maganizo anu kuti muziyenda m'chikondi cha Mulungu, ndikutsata khama la Khristu.
6
Abale, tsopano tikukulamulani m'dzina la Ambuye Yesu Khristu kuti muziŵapewa abale onse a makhalidwe aulesi, osafuna kutsata mwambo umene tidaŵapatsa.
7
Paja inu nomwe mukudziŵa zimene muyenera kuchita pofuna kutitsanzira. Ife sitinali aulesi pamene tinali pakati panu.
8
Sitidalandire chakudya kwa munthu aliyense osalipira, koma tidagwira ntchito kwambiri usana ndi usiku mpaka kutopa, kuwopa kuti tingalemetse wina aliyense mwa inu.
9
Sitidachitetu zimenezi chifukwa choti tilibe mphamvu zopemphera chithandizo kwa inu, koma tinkafuna kukhala chitsanzo choti muzichitsanzira.
10
Paja nthaŵi imene tinali nanu pamodzi, tidaakulamulani kuti munthu wosafuna kugwira ntchito, kudyanso asadye.
11
Tikunena zimenezi popeza kuti tikumva kuti pali ena pakati panu amene ali ndi khalidwe laulesi. Anthu ameneŵa sagwira ntchito konse, koma amangoloŵera pa za anzao.
12
M'dzina la Ambuye Yesu Khristu tikuŵalamula ndi kuŵachenjeza anthu otere kuti azigwira ntchito mwabata, ndi kumadya chakudya chodzigwirira ntchito.
13
Koma inu abale, musatope nkuchita zabwino.
14
Ngati wina aliyense akana kumvera mau amene talemba m'kalatayi, mumuwonetsetse ameneyo, ndipo musayanjane naye, kuti choncho achite manyazi.
15
Koma musamuwone ngati mdani. Makamaka mumchenjeze ngati mbale.
16
Ambuye, eniake mtendere amene, akupatseni mtenderewo nthaŵi zonse mwa njira iliyonse. Ambuye akhale ndi inu nonse.
17
Ndi dzanja langa ndikulemba mau aŵa: “Moni. Ndine, Paulo.” Mauŵa ndi chizindikiro changa m'kalata iliyonse. Ndimalemba motero.
18
Ambuye athu Yesu Khristu akukomereni mtima nonse.
← Chapter 2
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
All chapters:
1
2
3