bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Haggai 1
Haggai 1
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 2 →
1
Chaka chachiŵiri cha ufumu wa Dariusi, tsiku loyamba la mwezi wachisanu ndi chimodzi, Chauta adapatsa mneneri Hagai uthenga. Uthengawu, wopita kwa Zerubabele mwana wa Salatiyele, bwanamkubwa wa ku Yuda, ndiponso kwa Yoswa mwana wa Yehozadaki, mkulu wa ansembe, udati,
2
“Zimene ndikunena Ine Chauta Wamphamvuzonse ndi izi: Anthu aŵa amanena kuti, ‘Nthaŵi siinafike yoti nkumanganso Nyumba ya Chauta.’ ”
3
Tsono Chauta adapatsa mneneri Hagai uthenga uwu wakuti:
4
“Kodi nzabwino zimenezi kuti inuyo muzikhala m'nyumba zomanga bwino, pamene Nyumba yangayi ili bwinja?
5
“Nchifukwa chake tsono Ine Chauta Wamphamvuzonse ndikunena kuti muganizepo bwinotu pamenepa.
6
Mwafesa zambiri, koma mwakolola pang'ono. Mumadya, koma osakhuta. Mumamwa, koma ludzu osatha. Mumavala, koma osamva kufunda. Malipiro a anthu antchito ndi osakwanira mpang'ono pomwe,
7
“Nchifukwa chake Ine Chauta Wamphamvuzonse ndikunena kuti muganizeponso bwinotu pamenepa.
8
Kwerani ku mapiri, mukadule nsichi, mudzandimangire Nyumba yoyenera, kuti ndikondwere nayo ndi kulandiriramo ulemerero.
9
“Mwakhala mukuyembekeza zokolola zambiri, koma mwangopeza pang'ono. Pamene munkatuta zokolola zanu, Ine ndidangozimwazamwaza. Tsono Ine Chauta Wamphamvuzonse ndikuti, Ndidachitiranji zimenezi? Chifukwa chake nchakuti Nyumba yanga ndi bwinja, pamene aliyense akutanganidwa nkumanga nyumba yake.
10
Nkuwonatu mvula yati zii, nthaka yati gwa.
11
Nkuwonanso ndagwetsa chilala pa dziko lonse, pa minda ya tirigu, ya mphesa ndi ya mitengo ya olivi, pa zonse zomera pa nthaka, ndi pa zonse zimene anthu amalima, ndiponso pa anthu ndi nyama zomwe.”
12
Pamenepo Zerubabele mwana wa Salatiyele, Yoswa mwana wa Yehozadaki mkulu wa ansembe, ndi anthu ena onse obwerako ku ukapolo, adachita zimene Chauta Mulungu wao adanena. Adamva mau a mneneri Hagai amene Chauta adamtuma, ndipo adachita mantha kwambiri.
13
Motero Hagai, wamthenga uja, adaŵauza mau a Chauta akuti, “Ine Chauta ndikukuuzani kuti ndili nanu ndithu.”
14
Tsono Chauta adalimbitsa mtima Zerubabele mwana wa Salatiyele, bwanamkubwa wa ku Yuda, ndi Yoswa mwana wa Yehozadaki, mkulu wa ansembe, ndiponso anthu ena onse. Adabwera, nayamba kugwira ntchito yomanga Nyumba ya Chauta Wamphamvuzonse, Mulungu wao,
15
pa tsiku la 24 la mwezi wachisanu ndi chimodzi, wa chaka chachiŵiri pamene Dariusi anali mfumu.
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 2 →
All chapters:
1
2