bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Haggai 2
Haggai 2
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 1
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
1
Chaka chachiŵiri cha ufumu wa Dariusi, pa tsiku la 21, mwezi wachisanu ndi chiŵiri, Chauta adapatsa mneneri Hagai uthenga.
2
Uthengawu, wopita kwa Zerubabele mwana wa Salatiyele, bwanamkubwa wa ku Yuda, kwa Yoswa mwana wa Yehozadaki, ndiponso kwa ena onse, udati,
3
“Kodi alipo ena mwa inu amene adaaona ulemerero wakale wa Nyumba iyi? Monga simukuwona kuti tsopano ulemererowo watheratu?
4
Komabe Ine Chauta Wamphamvuzonse ndikuti, usataye mtima iwe Zerubabele, usataye mtima iwe Yoswa, mwana wa Yehozadaki, mkulu wa ansembe, musataye mtima inu nonse. Yambani ntchito, pakuti Ine ndili nanu ndithu.
5
Musachite mantha, popeza kuti mzimu wanga uli pakati panu, monga momwe ndidalonjezera pamene munkatuluka ku Ejipito.
6
“Zimene ndikunena Ine Chauta Wamphamvuzonse ndi izi: Patapita nthaŵi pang'ono, ndidzagwedeza mlengalenga ndi dziko lapansi, nyanja ndi mtunda.
7
Ndidzagwedeza mitundu yonse ya anthu ndipo chuma cha anthu onse chidzabwera, motero Nyumba imeneyi ndidzaidzaza ndi ulemerero waukulu. Ndikutero Ine Chauta Wamphamvuzonse.
8
Siliva yense ndi wanga, golide yense ndi wanga.
9
Choncho ulemerero wa Nyumba yachiŵiriyi udzaposa ulemerero wa Nyumba yoyamba ija. Ndipo ndidzakhazikitsa ufulu ndi mtendere pa malo ano. Ndikutero Ine Chauta Wamphamvuzonse.”
10
Chaka chachiŵiri cha ufumu wa Dariusi pa tsiku la 24 la mwezi wachisanu ndi chinai, Chauta adapatsa mneneri Hagai uthenga uwu wakuti,
11
“Zimene ndikunena Ine Chauta Wamphamvuzonse ndi izi: Mupemphe ansembe kuti agamule nkhani iyi:
12
Ngati munthu wakulunga nyama yopatulika mu mkanjo wake, ndipo mkanjowo ukhudza buledi kapena msuzi, kapena vinyo, kapena mafuta, kapena chakudya cha mtundu wina uliwonse, kodi zimenezinso zidzasanduka zopatulika? Ansembewo adayankha kuti, ‘Iyai.’ ”
13
Apo Hagai adaŵafunsanso kuti, “Nanga ngati munthu amene adaipitsidwa pokhudza mtembo, akhudzanso zimenezi, ndiye kuti zimenezinso zidzaipitsidwa?” Ansembe adayankha kuti, “Inde, zidzaipitsidwa.”
14
Hagai adanena kuti, “Zimene akunena Chauta ndi izi: ‘Nchimodzimodzinso ndi anthu ameneŵa, nchimodzimodzinso ndi mtundu umenewu pamaso panga. Zonse zimene amachita ndi zonse zimene amapereka ku nsembe nzoipitsidwa.
15
“ ‘Tsopano muganizire zimene zinkachitika asanayambe kumanganso Nyumba ya Chauta.
16
Pamene munthu ankayembekeza kupeza miyeso ya tirigu makumi aŵiri ankangopeza khumi yokha. Akabwera kuti adzatunge miyeso makumi asanu mu mtsuko wa vinyo, ankangopeza makumi aŵiri okha.
17
Ndidaononga mbeu zanu zonse ndi chinsikwi, chinoni ndi matalala. Komabe simudaganize zolapa,’ akutero Chauta.
18
“Lero ndi tsiku la 24, mwezi wachisanu ndi chinai, tsiku limene maziko a Nyumba ya Chauta aikidwa. Muganizirepo tsono,
19
mulibe chakudya chambiri m'nkhokwe. Mpesa, mkuyu, makangaza ndiponso mtengo wa olivi zikali zosabereka. Koma kuyambira lero ndidzakudalitsani.”
20
Tsiku limenelo, tsiku la 24 la mwezi, Chauta adapatsanso Hagai kachiŵiri uthenga uwu wakuti,
21
“Umuuze Zerubabele bwanamkubwa wa ku Yuda, kuti ndidzagwedeza mlengalenga ndi dziko lapansi.
22
Ndidzagwetsa mafumu a mitundu ya anthu akunja ndi kuwononga mphamvu za maufumu ao. Ndidzagubuduza magaleta ndi okwerapo ake. Akavalo adzafa, ndipo okwerapo ao adzaphana.
23
“Ine Chauta Wamphamvuzonse mau anga ndi aŵa: Pa tsiku limenelo iwe Zerubabele mtumiki wanga, mwana wa Salatiyele, ndidzakutenga ndipo ndidzakusandutsa wolamulira m'dzina langa, pakuti ndiwe amene ndakusankhula. Ndikutero Ine Chauta Wamphamvuzonse.”
← Chapter 1
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
All chapters:
1
2