bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
James 2
James 2
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 1
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 3 →
1
Abale anga, popeza kuti mumakhulupirira Ambuye athu Yesu Khristu, Ambuye aulemerero, musamakondera.
2
Mwachitsanzo: munthu wina aloŵa mumsonkhano mwanu atavala mphete zagolide m'manja, alinso ndi zovala zokongola. Winanso nkuloŵa, koma ali mmphaŵi, nsanza zili wirawira.
3
Tsono inu pofuna kusamala kwambiri wovala zokongolayo, mumuuza kuti, “Khalani apa pabwinopa”, mmphaŵi uja nkumuuza kuti, “Iwe, kaimirire apo, kapena dzakhale pansi kumapazi kwangaku.”
4
Limenelotu ndi tsankho pakati pa inu nokhanokha, ndipo inuyo mwasanduka oweruza a maganizo oipa.
5
Mverani, abale anga okondedwa, kodi suja Mulungu adasankha ooneka amphaŵi m'maso mwa anthu, kuti akhale olemera pa chikhulupiriro, ndi kuti alandire madalitso amene Iye adalonjeza anthu omukonda?
6
Koma inuyo mwakhala mukumnyoza mmphaŵiyo. Kodi si anthu olemera amene amakupsinjani? Si anthu olemera kodi amene amakukokerani ku mabwalo amilandu?
7
Kodi si omwewo amene amalichita chipongwe dzina lolemekezekali la Khristu, limene inu mumatchulidwa?
8
Tsono mumachita bwino ngati mumatsatadi lamulo lachifumu lija limene limapezeka m'Malembo, lonena kuti, “Uzikonda mnzako monga momwe umadzikondera iwe wemwe.”
9
Koma mukamaonetsa kukondera, mukuchimwa, ndipo Malamulo a Mulungu akukutsutsani kuti ndinu opalamula.
10
Pajatu munthu wotsata Malamulo onse, akangophonyapo ngakhale pa mfundo imodzi yokha, ndiye kuti wachimwira Malamulo onsewo.
11
Pakuti Mulungu amene adanena kuti, “Usachite chigololo”, adanenanso kuti, “Usaphe”. Ngati inu chigololo simuchita, koma kupha mumapha, ndiye kutitu mwachimwira Malamulo onse.
12
Tsono muzilankhula ndi kuchita zinthu monga anthu oti Mulungu adzaŵaweruza potsata lamulo loŵapatsa ufulu.
13
Paja munthu woweruza mopanda chifundo, nayenso Mulungu adzamuweruza mopanda chifundo. Koma wochita chifundo alibe chifukwa choopera chiweruzo cha Mulungu.
14
Abale anga, pali phindu lanji, ngati munthu anena kuti, “Ndili ndi chikhulupiriro,” koma popanda chimene akuchitapo? Kodi chikhulupiriro chotere chingampulumutse?
15
Mwachitsanzo: mbale wina kapena mlongo ali ndi usiŵa, ndipo masiku onse alibe chakudya chokwanira.
16
Tsono wina mwa inu angoŵauza kuti. “Pitani ndi mtendere, mukafundidwe ndipo mukakhute”, koma osaŵapatsa zimene akusoŵazo, pamenepo phindu lake nchiyani?
17
Choncho, chikhulupiriro pachokha, chopanda ntchito zake, nchakufa basi.
18
Koma kapena wina anganene kuti, “Inuyo muli ndi chikhulupiriro, ineyo ndili ndi ntchito zabwino.” Pamenepo ine nkumuyankha kuti, “Uyesetse kundiwonetsa chikhulupiriro chako chopanda ntchito zakecho, ine ndi ntchito zanga ndikuwonetsa chikhulupiriro changa.”
19
Inu mumakhulupirira kuti Mulungu ndi mmodzi yekha. Ai chabwino, mumakhoza, komatu ndi mizimu yoipa yomwe imakhulupirira zimenezi, imachitanso kunjenjemera.
20
Wopusawe, kodi ukufuna umboni wotsimikiza kuti chikhulupiriro chopanda ntchito zake nchachabe?
21
Nanga Abrahamu, kholo lathu, suja adakhala wolungama pamaso pa Mulungu chifukwa cha ntchito yomwe adachita, muja adaapereka mwana wake Isaki pa guwa lansembe?
22
Waona tsono kuti chikhulupiriro chake ndi zochita zake zidachitikira pamodzi. Zochita zake zidasandutsa chikhulupiriro chake kuti chifike pake penipeni.
23
Motero zidachitikadi zimene Malembo adaanena, kuti, “Abrahamu adakhulupirira Mulungu, nchifukwa chake Mulungu adamuwona kuti ngwolungama;” mwakuti ankatchedwa bwenzi la Mulungu.
24
Mukuwonatu kuti zochita zake za munthu ndizo zimamsandutsa wolungama pamaso pa Mulungu, osati chikhulupiriro chokha.
25
Kodi suja zidaateronso ndi Rahabu, mkazi wadama uja? Iye adaalandira azondi aja, nkuŵabweza kwao poŵadzeretsa njira ina, ndipo adapezeka kuti ngwolungama pamaso pa Mulungu chifukwa cha zimene adaachitazo.
26
Paja monga momwe thupi lopanda mzimu limakhala lakufa, moteronso chikhulupiriro chopanda ntchito zake nchakufa.
← Chapter 1
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 3 →
All chapters:
1
2
3
4
5