bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
James 3
James 3
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 2
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 4 →
1
Abale anga, musachuluke ofuna kukhala aphunzitsi, chifukwa monga mudziŵa, aphunzitsife tidzaweruzidwa mouma koposa anthu ena onse.
2
Paja tonsefe timalakwa pa zinthu zambiri. Ngati alipo amene salakwa pakulankhula, ndiye kuti ndi wangwirodi ameneyo, mwakuti angathe kulamuliranso thupi lake lonse.
3
Timaika kachitsulo m'kamwa mwa kavalo kuti atimvere, ndipo tingathe kumaongolera thupi lake lonse.
4
Onaninso zombo. Ngakhale nzazikulu kwambiri, ndipo zimakankhidwa ndi mphepo yamphamvu, komabe tsigiro laling'onong'ono ndi limene limaziwongolera kulikonse kumene woyendetsa akufuna.
5
Chimodzimodzinso lilime: ndi kachiwalo kakang'ono, komabe limadzitama kuti nkuchita zazikulu. Tangoganizani kukula kwake kwa nkhalango imene ingayatsidwe ndi kalilaŵi kakang'ono ka moto.
6
Tsonotu lilime limatentha ngati moto. Chifukwa chokhala pakati pa ziwalo zathu limawanditsa zoipa m'thupi monse. Limaipitsa khalidwe lonse la munthu. Limayatsa moto moyo wathu wonse kuyambira pobadwa mpaka imfa; ndipo moto wake ngwochokera ku Gehena.
7
Munthu angathe kuŵeta mtundu uliwonse wa nyama, wa mbalame, wa zokwaŵa, ndi wazam'nyanja, ndipo adaziŵetapodi.
8
Koma lilime palibe munthu amene angathe kuliŵeta. Ndi loipa, silidziŵa kupumula, ndipo ndi lodzaza ndi ululu wakupha.
9
Ndi lilime lomwelo timayamika Ambuye, amenenso ndi Atate, komanso ndi lilime lomwelo timatemberera anthu anzathu amene Mulungu adaŵalenga ofanafana naye.
10
Pakamwa pomwe pamatuluka mayamiko pomweponso pamatuluka matemberero. Abale anga, zoterezi siziyenera kumachitika.
11
Kodi kasupe amatulutsa madzi omweka ndi oŵaŵa pa dzenje limodzimodzi?
12
Abale anga, kodi mkuyu ungathe kubala zipatso za olivi, kapena mpesa kubala nkhuyu? Momwemonso kasupe wa madzi amchere sangathe kupereka madzi omweka.
13
Ndani mwa inu ali wanzeru ndi womvetsa zinthu? Aonetse ndi makhalidwe ake abwino kuti nzeru zimaongoleradi zochita zake zofatsa.
14
Koma ngati muli ndi mtima wakaduka ndi wodzikonda, musamanyada ndi kutsutsana ndi choona pakunena mabodza.
15
Nzeru zotere si zochokera Kumwamba, koma ndi nzapansipano, ndi za anthu chabe, ndiponso nzochokera ku mizimu yoipa.
16
Pajatu pamene pali kaduka ndi kudzikonda, pomweponso pali chisokonezo ndi ntchito yoipa ya mtundu uliwonse.
17
Koma nzeru zochokera Kumwamba, poyamba nzangwiro, kuwonjeza apo nzamtendere, zofatsa ndi zomvera bwino. Ndi za chifundo chambiri, ndipo zipatso zake zabwino nzochuluka. Nzeruzo sizikondera kapena kuchita chiphamaso.
18
Ndipo chilungamo ndiye chipatso cha mbeu zimene anthu odzetsa mtendere amafesa mu mtendere.
← Chapter 2
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 4 →
All chapters:
1
2
3
4
5