bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Philippians 1
Philippians 1
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 2 →
1
Ndife, Paulo ndi Timoteo, atumiki a Khristu Yesu. Tikulembera onse a mu mzinda wa Filipi, amene ali anthu ake a Mulungu mwa Khristu Yesu. Tikulemberanso oyang'anira Mpingo ndi atumiki ao.
2
Mulungu Atate athu ndi Ambuye Yesu Khristu akukomereni mtima ndi kukupatsani mtendere.
3
Ndimayamika Mulungu wanga nthaŵi zonse ndikamakukumbukirani.
4
Nthaŵi zonse pamene ndikukupemphererani nonsenu, ndimapemphera mokondwa.
5
Ndiyeneradi kuthokoza chifukwa mwakhala mukugwirizana nane ndi kundithandiza kufalitsa Uthenga Wabwino, kuchokera tsiku limene mudayamba kukhulupirira mpaka tsopano.
6
Sindikayika konse kuti Mulungu, amene adayamba kuchita ntchito yabwinoyi mwa inu, adzaipitiriza mpaka itatsirizika pa Tsiku la Kubweranso kwa Khristu Yesu.
7
Ndikuyeneradi kuganiza zotere za nonsenu, popeza kuti ndimakukondani kwambiri. Pakuti nonsenu ndinu ogwirizana nane ndithu, pamene ndili m'ndende ndiponso pamene ndikugwira ntchito iyi imene Mulungu adandipatsa mwa kukoma mtima kwake, ntchito ya kuteteza ndi kukhazikitsa Uthenga Wabwino.
8
Mulungu akundichitira umboni kuti ndimakulakalakani kwambiri, pakuti ndimakukondani ndi mtima wonse, motsanzira chikondi cha Khristu Yesu mwini.
9
Pemphero langa ndi lakuti chikondi chanu chinke chikukulirakulira pamodzi ndi nzeru ndi kumvetsetsa zinthu mozama.
10
Pamenepo mudzadziŵa kusankha zimene zili zabwino kotheratu. Apo pa Tsiku la Kubweranso kwa Khristu mudzapezeka oyera mtima, ndi opanda cholakwa chilichonse.
11
Ndipo moyo wanu udzakhala wodzaza ndi zipatso za chilungamo zimene mudzaonetsa mothandizidwa ndi Yesu Khristu, kuti anthu onse alemekeze ndi kutamanda Mulungu.
12
Abale, ndikufuna kuti mudziŵe kuti zimene zandigwera, zathandiza ndithu kufalitsa Uthenga Wabwino.
13
Mwakuti asilikali onse olonda nyumba ya mfumu, ndi ena onse kuno, adziŵa kuti ndili m'ndende chifukwa cha Khristu.
14
Tsono chifukwa choti ndili m'ndende, abale ochuluka akulimba mtima mwa Ambuye, ndipo akulalika mau a Mulungu mopanda mantha.
15
Alipodi ena amene amalalika Khristu chifukwa cha kaduka ndi kukonda mikangano. Koma aliponso ena amene amamlalika ndi mtima woona.
16
Otsirizaŵa amamlalika chifukwa cha chikondi, popeza kuti amadziŵa kuti Mulungu adandikhazika muno kuti ndigwire ntchito yoteteza Uthenga Wabwino.
17
Koma oyamba aja salalika Khristu moona. Amangodzikonda okha, ndipo amafuna kundiwonjezera zoŵaŵa pamene ndili m'ndende muno.
18
Zili nkanthu ngati! Kaya amalalika mwachiphamaso, kaya moona, malinga nkuti Khristu akulalikidwa, pamenepo ine ndikukondwa.
19
Ndipo sindidzaleka kukondwa podziŵa kuti chifukwa cha mapemphero anu ndiponso chithandizo cha Mzimu wopatsidwa ndi Yesu Khristu ndidzamasulidwa.
20
Motero ndikuyembekeza ndi kukhulupirira ndi mtima wonse kuti sipadzakhala konse manyazi. Koma ndikuyembekeza kuti ndidzalimba mtima kulankhula poyera, kuti tsopanonso, monga nthaŵi zonse, Khristu alemekezedwe mwa ine, ngakhale ndikhale moyo, kapena ndimwalire.
21
Kwa inetu moyo ndi Khristu amene, ndipo nayonso imfa ili ndi phindu.
22
Koma ngati kukhalabe moyo kungandipatse mwai woti ndigwire ntchito yoonetsa zipatso, sindidziŵa kaya ndingasankhe chiti.
23
Ndagwira njakata. Kwinaku ndikulakalaka kuti ndisiye moyo uno ndikakhale pamodzi ndi Khristu, pakuti chimenechi ndiye chondikomera koposa.
24
Koma kwinakunso nkofunika kwambiri kuti ndikhale moyo chifukwa cha inuyo.
25
Mosakayika konse ndikudziŵa kuti ndidzakhalapobe. Ndidzapitiriza kukhala nanu nonsenu, kuthandiza kuti chikhulupiriro chanu chizikula, ndipo chikupatseni chimwemwe koposa kale.
26
Motero pamene ndidzafikanso kwanuko, mudzakhala ndi zifukwa zochuluka zonyadira Khristu Yesu chifukwa cha ine.
27
Chachikulu nchakuti mayendedwe anu akhale oyenerana ndi Uthenga Wabwino wonena za Khristu. Ngakhale ndibwere kudzakuwonani, kapena ndikhale kutali, ndikufuna kumva kuti mukulimbika ndi mtima umodzi. Ndikufunanso kumva kuti momvana ndi mothandizana mukumenya nkhondo chifukwa chokhulupirira Uthenga Wabwino,
28
osalola kuti adani anu azikuwopsezani pa kanthu kalikonse. Zimenezi zidzaŵatsimikizira kuti iwowo adzaonongeka, koma inu mudzapulumuka. Mulungu ndiye amene adzakuchitirani zimenezi.
29
Paja Iye adakupatsani mwai, osati wakungokhulupirira Khristu ai, komanso wakumva zoŵaŵa chifukwa cha Iye.
30
Inunso mukumenya nkhondo yomwe ija imene mudandiwona ine ndikuimenya, yomwenso ndikumenyabe tsopano, monga mukumveramu.
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 2 →
All chapters:
1
2
3
4