bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Philippians 4
Philippians 4
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 3
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
1
Tsono abale anga, ndimakukondani ndipo ndikukulakalakani. Mumandisangalatsa ndipo ndinu mphotho yanga imene ndimainyadira. Okondedwa anga, limbikani choncho mogwirizana ndi Ambuye.
2
Yuwodiyayo ndi Sintikeyo ndaŵapemba, chonde akhale omvana, popeza kuti ndi abale mwa Ambuye.
3
Ndiponso iwe, mnzanga weniweni pa ntchito yathuyi, bwanji uŵathandize azimaiŵa. Paja ameneŵa pofalitsa Uthenga Wabwino akhala akugwira ntchito kolimba pamodzi ndi ine ndi Klemensi ndi antchito anzanga ena onse, amene maina ao ngolembedwa m'buku la amoyo.
4
Muzikondwa mwa Ambuye nthaŵi zonse. Ndikubwerezanso kuti, “Muzikondwa.”
5
Kufatsa kwanu kuziwoneka pamaso pa anthu onse. Ambuyetu ali pafupi.
6
Musade nkhaŵa ndi kanthu kalikonse, koma m'mapemphero anu onse muzipempha Mulungu zimene zikusoŵani, ndipo nthaŵi zonse muzipemphe ndi mtima woyamika.
7
Pamenepo mtendere wochokera kwa Mulungu, umene uli wopitirira nzeru zonse za anthu, udzasunga bwino mitima yanu ndi maganizo anu mwa Khristu Yesu.
8
Potsiriza, abale, muziika mtima pa zilizonse zabwino kwambiri ndi zotamandika, monga izi: zinthu zoona ndi zolemekezeka, zinthu zolungama, zoyera, zokongola, ndi zaulemu.
9
Muzichita zimene mudaphunzira ndi kulandira kwa ine, ndiponso zimene mudamva kwa ine ndi kuwonera kwa ine. Pamenepo Mulungu amene amapatsa mtendere adzakhala nanu.
10
Ndakondwa kwambiri mwa Ambuye kuti tsopano, patapita nthaŵi yaitali, mwayambanso kuwonetsa kuti mumandikumbukira. Kukumbukira munkandikumbukiradi, koma munkangosoŵa mpata woti muwonetsere.
11
Sindikunena zimenezi modandaula kuti ndikusoŵa kanthu, pakuti ine ndaphunzira kukhutira ndi zimene ndili nazo.
12
Kukhala wosauka ndimakudziŵa, kukhala wolemera ndimakudziŵanso. Pa zonse ndidaphunzira chinsinsi chake cha kukhala wokhutitsidwa, pamene ndapeza chakudya kapena ndili ndi njala, pamene ndili ndi zambiri kapena ndili wosoŵeratu.
13
Ndingathe kuchita zonse chifukwa Khristu amandipatsa mphamvu.
14
Komabe mudaachita bwino kundithandiza pa zovuta zanga.
15
Inu Afilipi, mukudziŵa inu nomwe kuti pamene ndidachoka ku Masedoniya, masiku oyamba aja akulalika Uthenga Wabwino, panalibe mpingo wina wogwirizana nane pa zoyenera kulipira kapena kulandira, koma inu nokha.
16
Pamene ndinali ku Tesalonika, mudatumiza kangapo zondithandiza pa zosoŵa zanga.
17
Sikuti ndikuika mtima pa mphatso zanu ai, koma chimene ndikukhumba nchakuti pa zimene muli nazo, pawonjezedwe phindu.
18
Ndalandiradi zonse, ndipo ndili nazo zochuluka. Ndili ndi zonse zofunika tsopano, popeza kuti ndalandira kwa Epafrodito zimene mudanditumizira. Zili ngati chopereka cha fungo lokoma, ngati nsembe imene Mulungu ailandira ndi kukondwera nayo.
19
Mulungu wanga ali ndi chuma chochuluka, ndipo mwa Khristu Yesu adzakupatsani zonse zimene mukusoŵa.
20
Mulungu Atate athu alemekezedwe mpaka muyaya. Amen.
21
M'dzina la Khristu Yesu mundiperekereko moni kwa aliyense wamumpingo. Akukupatsani moni abale amene ndili nawo pamodzi kuno.
22
Akukupatsani moni anthu onse a Mulungu amene ali kuno, makamakanso ogwira ntchito ku nyumba ya Mfumu ya ku Roma.
23
Ambuye Yesu Khristu akudalitseni.
← Chapter 3
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
All chapters:
1
2
3
4
Recommended Reading
Commentary
Philippians Commentaries
→
Devotional
Philippians Devotional Guide
→
Get This Bible
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa) Study Bible
→