bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Ruth 3
Ruth 3
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 2
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 4 →
1
Tsiku lina Naomi adafunsa Rute kuti, “Kodi iwe mwana wanga, nanga sikwabwino kuti ndikupezere pokhala, kuti zinthu zizikuyendera bwino?
2
Bowazi amene adzakazi ake unali nawo, ndi wachibale wathu. Usiku uno iye akhala akupuntha barele ku malo ake opunthira.
3
Samba tsono, udzole mafuta ndipo uvale zovala zabwino kwambiri, upite kopunthirako. Koma munthuyo asakakuzindikire mpaka atamaliza kudya ndi kumwa.
4
Pamene akukagona, ukaonetsetse malo amene akagonewo. Tsono ukavundukule chofunda chake nukagona ku mapazi ake. Motero iyeyo akakuuza zoti uchite.”
5
Rute adayankha kuti, “Zonse mwanenazi ndichita.”
6
Choncho Rute adapita kopunthira kuja, ndipo adakachitadi monga momwe mpongozi wake uja adaamuuzira.
7
Bowazi atamaliza kudya ndi kumwa, anali wosangalala, ndipo adapita kukagona pambali pa mulu wa barele. Tsono Rute adabwera mopanda mtswatswa, adavundukula mapazi a Bowazi, nagona pomwepo.
8
Tsono pakati pa usiku Bowazi adadzidzimuka natembenuka, naona mkazi atagona ku mapazi ake. Adafunsa kuti, “Ndiwe yani?”
9
Mkaziyo adayankha kuti, “Ndine Rute mdzakazi wanu. Popeza kuti ndinu wachibale, muyenera kundiwombola pakundiloŵa chokolo.”
10
Apo Bowazi adati, “Chauta akudalitse, mwana wanga. Zabwino wachita potsirizazi zikupambana zoyamba zija zimene udachitira mpongozi wako, poti sudapite kwa anyamata osauka kapena olemera.
11
Tsopano usadandaule, mwana wanga. Ndidzakuchitira zonse zimene upemphe, pakuti anzanga am'mudzimu akudziŵa kuti ndiwe mkazi wabwino.
12
Nzoona, ine ndine wachibale, komabe alipo wachibale weniweni kupambana ine.
13
Gona konkuno usiku uno mpaka m'maŵa. Ngati iyeyo adzakuloŵe chokolo, chabwino aloŵe. Koma ngati safuna, ndidzakuloŵa ndine, ndikulumbira pamaso pa Chauta wamoyo. Gona mpaka m'maŵa.”
14
Choncho Rute adagona ku mapazi a Bowazi mpaka m'maŵa, koma adadzuka kudakali kamdimabe, chifukwa Bowaziyo sankafuna kuti anthu adziŵe kuti mkaziyo adaabwera kopunthira bareleko.
15
Tsono Bowazi adauza Rute kuti, “Bwera nacho kuno chofunda wavalacho, uchiyale pansi.” Rute adayala chofundacho, ndipo Bowazi adayesa makilogramu makumi aŵiri a barele, namsenzetsa Rute uja. Tsono Rute adachoka nakaloŵa mu mzinda.
16
Atafika kwa mpongozi wake uja, mpongoziyo adati, “Zinthu zakuyendera bwanji, mwana wanga?” Rute adamfotokozera zonse zimene munthu uja adamchitira,
17
ndipo adati, “Wandipatsa makilogramu makumi aŵiri a barele, nandiwuza kuti, ‘Usapite kwa apongozi ako chimanjamanja.’ ”
18
Apongozi akewo adayankha kuti, “Dikira mwana wanga, tiwone m'mene zikhalire zinthu, chifukwa munthuyo salekera pomwepo, koma azikonza zimenezi lero.”
← Chapter 2
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 4 →
All chapters:
1
2
3
4