bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Ruth 4
Ruth 4
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 3
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
1
Nthaŵi yomweyo Bowazi adapita ku chipata cha mzinda nakakhala pansi, pa bwalo losonkhanirana. Tsono adangoona wachibale ankanena uja akufika. Apo Bowazi adati, “Bwenzi langa, tapatukira kuno, ukhale pansi apa.” Munthu uja adapatuka nakhala pansi.
2
Adaitananso atsogoleri khumi amumzindamo naŵauza kuti, “Takhalani pansi apa.” Iwo adakhala pansi.
3
Tsono adauza munthu wachibale uja kuti, “Naomi amene wabwerera kuchokera ku dziko la Mowabu, akugulitsa munda umene udaali wa malemu Elimeleki, wachibale wathu.
4
Choncho ndinaganiza zokuuza zimenezi, kuti ugule mundawo pamaso pa anthu amene ali panoŵa, ndi pamaso pa atsogoleri a abale athu. Ngati ufuna kugula, ugule. Koma ngati sufuna, undiwuze kuti ndidziŵe, pakuti palibe wina woti augule koma iweyo, ndipo pambuyo pa iwe pali ine.” Munthuyo adati, “Ndigula munda umenewo.”
5
Tsono Bowazi adamuuza kuti, “Tsiku limene udzagule mundawo kwa Naomi, udzatenganso Rute Mmowabu, mai wamasiye uja, kuti dzina la malemu aja lisungike pa choloŵa chao.”
6
Apo wachibaleyo adati, “Sindingathe kugula mundawo kuti ukhale wanga, kuwopa kuti ndingaononge choloŵa changa. Mugule ndinu, ine sindingathe.”
7
Masiku amenewo, munthu akamachita malonda kapena kusinthana kanthu ndi mnzake, zinkayenda motere: ankavula nsapato imodzi napatsa mnzakeyo. Imeneyi ndiyo inali njira yochitira umboni m'dziko la Israele.
8
Choncho pamene wachibale uja adauza Bowazi kuti, “Gulani ndinu mundawo,” adavula nsapato yake napatsa Bowazi.
9
Tsono Bowazi adauza atsogoleri ndi anthu onse aja kuti, “Nonsenu ndinu mboni lero, kuti ine ndagula kwa Naomi zonse zimene zidaali za malemu Elimeleki, ndiponso zonse za malemu Kiliyoni ndi za malemu Maloni.
10
Ndatenganso Rute Mmowabu uja, mkazi wa malemu Maloni, kuti akhale mkazi wanga, kuti dzina la malemulo lisungike pa choloŵa chake, ndipo lisafafanizike pakati pa abale ake ndiponso m'mudzi mwake. Nonsenu ndinu mboni lero lino.”
11
Apo anthu onse amene anali pachipata paja, pamodzi ndi atsogoleri aja, adati, “Inde, ndife mboni. Mkazi amene akudzaloŵa m'nyumba mwakoyo, Chauta amsandutse wofanafana ndi Rakele ndi Leya, akazi amene adamanga banja la Israele pombalira ana ambiri. Ukhale munthu wosasoŵa kanthu mu mzinda wa Efurata, ndipo ukhale munthu wotchuka mu mzinda wa Betelehemu.
12
Ana ako amene Chauta adzakupatse mwa mai ameneyu, adzamange banja longa la Perezi, amene Tamara adabalira Yuda.”
13
Choncho Bowazi adakwatira Rute, ndipo Chauta adadalitsa Ruteyo, mwakuti adatenga pathupi nabala mwana wamwamuna.
14
Tsono akazi adauza Naomi kuti, “Ngwodala Chauta amene sadakusiyeni nokha opanda wachibale. Mwanayo dzina lake litchuke mu Israele.
15
Mwanayo adzakupatsani moyo watsopano ndipo adzakuchirikizani mu ukalamba wanu. Inde wakubalirani mwana mpongozi wanu amene amakukondani, amene wakuwonetsani kuti akupambana ana aamuna asanu ndi aŵiri.”
16
Naomi adanyamula mwanayo namfukata ndipo adakhala mlezi wake.
17
Akazi achinansi ake adalengeza kuti, “Mwana wabadwa kwa Naomi.” Ndipo adamutcha dzina loti Obedi. Iyeyu adakhala bambo wake wa Yese, bambo wa Davide.
18
Tsono zidzukulu za Perezi ndi izi: Perezi adabereka Hezironi,
19
Hezironi adabereka Ramu, Ramu adabereka Aminadabu.
20
Aminadabu adabereka Nasoni, Nasoni adabereka Salimoni.
21
Salimoni adabereka Bowazi, Bowazi adabereka Obedi.
22
Obedi adabereka Yese ndipo Yese adabereka Davide.
← Chapter 3
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
All chapters:
1
2
3
4