bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
/
1 Chronicles 13
1 Chronicles 13
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
← Chapter 12
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 14 →
1
Ndipo Davide anafunsana ndi akuru a zikwi ndi a mazana, inde atsogoleri ali onse.
2
Ndipo Davide anati kwa msonkhano wonse wa Israyeli, Cikakomera inu, ndipo cikacokera kwa Yehova Mulungu wathu, titumize konse kuti abale athu otsala m'dziko lonse la Israyeli, ndi ansembe ndi Alevi okhala nao m'midzi yao yokhala napa podyetsa, kuti asonkhane kwa ife;
3
ndipo tibwere nalo kwa ife likasa la Mulungu wathu, pakuti sitinafunako masiku a Sauli.
4
Ndipo a msonkhano onse anati kuti adzacita; pakuti cidayenera cinthuci pamaso pa anthu onse.
5
M'mwemo Davide anamemeza Aisrayeli onse kuyambira Sihori wa ku Aigupto mpaka polowera ku Hamati, kutenga likasa la Mulungu ku Kiriati-Yearimu.
6
Ndipo Davide ndi Aisrayeli onse pamodzi naye anakwera kumka ku Baala, ndiko ku Kiriati-Yearimu wa m'Yuda, kukwera nalo kucokera komweko likasa la Mulungu Yehova wakukhala pa akerubi, kumene aitanirako Dzina.
7
Ndipo anatengera likasa la Mulungu pa gareta watsopano kucokera ku nyumba ya Abinadabu; ndi Uza ndi Ahiyo anayendetsa ng'ombe za pa garetayo,
8
Ndipo Davide ndi Aisrayeli onse anasewera pamaso pa Mulungu ndi mphamvu yao yonse; ndi nyimbo, ndi azeze, ndi zisakasa, ndi malingaka, ndi nsanje, ndi malipenga,
9
Ndipo pamene anafika ku dwale la Kidoni, Uza anatambasula dzanja lace kulicirikiza likasa, pakuti ng'ombe zikadapulumuka.
10
Ndi mkwiyo wa Yehova unayakira Uza, namkantha, cifukwa anatambasulira likasa dzanja lace, nafa komweko pamaso pa Mulungu.
11
Ndipo kudaipira Davide kuti Yehova adacita cipasulo ndi Uza; motero anacha malowo Perezi Uza, mpaka lero lino.
12
Ndipo Davide anaopa Mulungu tsikulo, ndi kuti, Ndidzafika nalo bwanji likasa la Mulungu kwathu?
13
M'mwemo Davide sanafika nalo likasa kwao ku mudzi wa Davide, koma analipambutsira ku nyumba ya Obedi Edomu wa ku Giti.
14
Ndi likasa la Mulungu linakhala ndi banja la Obedi Edomu m'nyumba mwace miyezi itatu; ndipo Yehova anadalitsa nyumba ya Obedi Edomu, ndi zonse anali nazo.
← Chapter 12
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 14 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29