bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
/
1 Chronicles 18
1 Chronicles 18
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
← Chapter 17
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 19 →
1
Ndipo zitatha izi, Davide anakantha Afilisti, nawagonjetsa, nalanda Gati ndi midzi yace m'manja a Afilisti.
2
Anakanthanso Moabu; ndi Amoabu anakhala anthu a Davide, nabwera nazo mphatso,
3
Ndipo Davide anakantha Hadarezeri mfumu ya Zoba ku Hamati, pomuka iye kukhazikitsa ulamuliro wace ku mtsinje wa Firate.
4
Ndipo Davide analanda magareta ace cikwi cimodzi, ndi apakavalo zikwi zisanu ndi ziwiri, ndi oyenda pansi zikwi makumi awiri; Davide anadula mitsita akavalo onse okoka magareta, koma anasungako ofikira magareta zana limodzi.
5
Ndipo Aaramu a ku Damasiko anadza kudzathandiza Hadarezeri mfumu ya Zoba; koma Davide anakantha Aaramu amuna zikwi makumi awiri mphambu ziwiri.
6
Ndipo Davide anaika asilikari a boma m'Aramu wa Damasiko; ndi Aaramu anasanduka anthu a Davide, nabwera nazo mphatso, Ndipo Yehova anasunga Davide kuli konse anamukako.
7
Natenga Davide zikopa zagolidi zinali pa anyamata a Hadarezeri, nabwera nazo ku Yerusalemu.
8
Ndi ku Tibati, ndi ku Kuni, midzi ya Hadarezeri, Davide anatenga mkuwa wambiri, ndiwo umene Solomo anayenga nao thawale lamkuwa, ndi nsanamira, ndi zipangizo zamkuwa.
9
Ndipo pakumva Tou, mfumu ya ku Hamati, kuti Davide adakantha khamu lonse la Hadarezeri mfumu ya ku Zoba,
10
anatumiza Hadoramu mwana wace kwa Davide, kumlankhula ndi kumdalitsa, popeza adayambana ndi Hadarezeri, namkantha; pakuti Hadarezeri adacita nkhondo ndi Tou; ndipo anali nazo zipangizo za mitundu mitundu za golidi ndi siliva ndi mkuwa.
11
Izi zomwe mfumu Davide anazipatulira Yehova, pamodzi ndi siliva ndi golidi adazitenga kwa amitundu onse, kwa Edomu, ndi kwa Moabu, ndi kwa ana a Amoni, ndi kwa Afilisti, ndi kwa Amaleki.
12
Ndipo Abisai mwana wa Zeruya anakantha Aedomu m'Cigwa ca Mcere zikwi khumi mphambu zisanu ndi zitatu.
13
Ndipo anaika asilikari a boma m'Edomu; ndi Aedomu onse anasanduka anthu a Davide. Ndipo Yehova anasunga Davide kuli konse anamukako.
14
Ndipo Davide anakhala mfumu ya Aisrayeli onse, naweruza anthu ace onse, nawacitira cilungamo.
15
Ndipo Yoabu mwana wa Zeruya anayang'anira khamu la nkhondo, ndi Yehosafati mwana wa Ahiludi anali wolemba mbiri.
16
Ndi Zadoki mwana wa Ahitubu, ndi Abimeleki mwana wa Abyatara, anali ansembe, ndi Savisa anali mlembi,
17
ndi Benaya mwana wa Yehoyada anayang'anira Akereti ndi Apeleti; koma ana a Davide ndiwo oyamba ku dzanja la mfumu.
← Chapter 17
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 19 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29