bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
/
2 Samuel 22
2 Samuel 22
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
← Chapter 21
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 23 →
1
Ndipo Davide analankhula kwa Yehova mau a nyimbo iyi tsikuli Yehova anampulumutsa m'dzanja la adani ace onse, ndi m'dzanja la Sauli.
2
Ndipo anati:- Yehova ndiye thanthwe langa, ndi ngaka yanga, ndi mpulumutsi wanga, wangadi;
3
Mulungu wa thanthwe langa, Iye ndidzamkhulupirira; Cikopa canga, ndi nyanga ya cipulumutso canga, nsanja yanga yaitali, ndi populumukirapo panga; Mpulumutsi wanga, mundipulumutsa kuciwawa.
4
Ndidzaitanakwa Yehovaamene ayenera timtamande; Comweco ndidzapulumutsidwa kwa adani anga.
5
Pakuti mafunde a imfa anandizinga, Mitsinje ya zopanda pace inandiopsa ine.
6
Zingwe za kumanda zinandizingira; Misampha ya imfa inandifikira ine.
7
M'kusauka kwanga ndinaitana kwa Yehova, Inde ndinakuwira kwa Mulungu wanga; Ndipo Iye anamva mau anga ali m'kacisi wace, Ndi kulira kwanga kunafika ku makutuace.
8
Pomwepo dziko linagwedezeka ndi kunthunthumira. Maziko a dziko la kumwamba anasunthika Nagwedezeka, cifukwa iye anakwiya.
9
M'mphuno mwace munaturuka utsi, Ndi moto woturuka m'kamwa mwace unaononga; Makala anayaka nao.
10
Anaweramitsa miyambanso, natsika; Ndipo mdima wandiwe-yani unali pansi pa mapazi ace.
11
Ndipo iye anaberekeka pa Kerubi nauluka; Inde anaoneka pa mapiko a mphepo,
12
Ndipo anayesa mdimawo ngati mahema omzungulira iye, Kusonkhana kwa madzi ndi mitambo yocindikira ya mlengalenga.
13
Ceza ca pamaso pace Makala a mota anayaka,
14
Yehova anagunda kumwamba; Ndipo Wam'mwambamwamba ananena mau ace.
15
Ndipo iye anatumiza mibvi, nawawaza; Mphezi, nawaopsa,
16
Pamenepo m'munsi mwa nyanja munaoneka, Maziko a dziko anaonekera poyera, Ndi mthonzo wa Yehova, Ndi mpumo wa mweya wa m'mphuno mwace.
17
Iye anatumiza kucokera kumwamba nanditenga; Iye ananditurutsa m'madzi akuru;
18
Iye anandipulumutsa kwa mdani wanga wamphamvu, Kwa iwo akudana ndi ine; pakuti anandiposa mphamvu,
19
Anandifikira ine tsiku la tsoka langa; Koma Yehova anali mcirikizo wanga,
20
Iye ananditurutsanso ku malo akuru; Iye anandipulumutsa, cifukwa akondwera ndi ine.
21
Yehova anandibwezera monga mwa colungama canga; Monga mwa kuvera kwa manja anga anandipatsa mphotho.
22
Pakuti ndinasunga njira za Yehova, Osapambukira koipa kusiya Mulungu wanga.
23
Pakuti maweruzo ace onse anali pamaso panga; Ndipo za malemba ace, sindinawapambukira.
24
Ndinakhalanso wangwiro kwa iye, Ndipo ndinadzisunga kusacita kuipa kwanga.
25
Cifukwa cace Yehova anandibwezera monga mwa colungama canga; Monga mwa kuyera kwanga pamaso pace.
26
Ndi acifundo Inu mudzadzionetsa wacifundo, Ndi munthu wangwiro mudzadzionetsa wangwiro;
27
Ndi oyera mtima mudzadzionetsa woyera mtima; Ndi otsutsatsutsa mudzadzionetsa wopotoza.
28
Ndipo mudzapulumutsa anthu osautsidwa; Koma maso anu ali pa odzikuza kuti muwacepetse.
29
Pakuti Inu ndinu nyali yanga, Yehova; Ndipo Yehova adzaunika mumdima mwanga.
30
Pakuti ndi Inu ndithamangira gulu; Ndi Mulungu wanga ndilumphira linga.
31
Kunena za Mulungu, njira yace iri yangwiro; Mau a Yehova anayesedwa; iye ndiye cikopa kwa onse akukhulupirira iye.
32
Pakuti Mulungu ndani, koma Yehova? Ndipo thanthwe ndani, koma Mulungu wathu?
33
Mulungu ndiye Gnga langa lamphamvu; Ndipo iye ayendetsa angwiro mu njira yace.
34
Iye asandutsa mapazi ace akunga mapazi a mbawala; Nandiika pa misanje yanga.
35
Iye aphunzitsa manja anga nkhondo; Kotero kuti manja anga alifula uta wamkuwa.
36
Ndiponso munandipatsa cikopa ca cipulumutso canu; Ndi kufatsa kwanu kunandikulitsa.
37
Munakulitsa kulunza kwanga pansi panga, Ndi mapazi anga sanaterereka.
38
Ndinapitikitsa adani anga, ndi kuwaononga; Ndiponso sindinabwerera mpaka nditawatha.
39
Ndinawatha ndi kuwapyoza, kuti sakhoza kuuka, Inde anagwa pansi pa mapazi anga.
40
Pakuti Inu munandimanga m'cuuno ndi mphamvu ya kunkhondo; Munandigonjetsera akundiukira.
41
Munatembenuzitsanso adani anga andipatse mbuyo, Kuti ndiwalikhe akudana ndi ine.
42
Anayang'ana iwo, koma panalibe wopulumutsa; Ngakhale kwa Yehova, koma iye sanawayankha.
43
Pomwepo ndinawasansantha asalale ngati pfumbi la padziko, Ndinawapondereza ngati dothi la m'makwalala.
44
Inunso munandipulumutsa ine pa kulimbana kwa anthu anga; Munandisunga ndikhale mutu wa amitundu; Anthu amene sindinawadziwa adzanditsumikira ine.
45
Alendo adzandigonjera ine, Pakumva za ine, adzandimbera pomwepo.
46
Alendo adzafota, Nadzabwera ndi kunthunthumira oturuka mokwiririka mwao.
47
Yehova ali ndi moyo; ndipo lidalitsike thanthwe langa; Ndipo akulitsidwe Mulungu wa thanthwe la cipulumutso canga;
48
Inde Mulungu wakundibwezera cilango ine, Ndi kundigonjetsera anthu a mitundu.
49
Amene anditurutsa kwa adani anga; Inde mundikweza ine pamwamba pa iwo akundiukira; Mundipulumutsa kwa munthu waciwawa.
50
Cifukwa cace ndidzakuongani Yehova, pakati pa amitundu, Ndipo ndidzayimba zolemekeza dzina lanu.
51
Iye apatsa mfumu yace cipulumutso cacikuru; Naonetsera cifundo wodzozedwa wace, Kwa Davide ndi mbeu yace ku nthawi zonse.
← Chapter 21
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 23 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24