bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
/
2 Samuel 8
2 Samuel 8
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
← Chapter 7
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 9 →
1
Ndipo m'tsogolo mwace Davide anakantha Afilisti, nawagonjetsa; Davide nalanda mudzi wa Metege Ama m'manja mwa Afilisti.
2
Ndipo anakantha Amoabu nawayesa ndi cingwe, nawagonetsa pansi; ndipo anawayesera zingwe ziwiri kupha, ndi cingwe cimodzi cathunthu kusunga ndi moyo. Ndipo Amoabu anakhala anthu a Davide, nabwera: nayo mitulo.
3
Davide anakanthanso Hadadezeri, mwana wa Rehobu, mfumu ya ku Zoba, pomuka iye kukadzitengeranso ufumu wace ku cimtsinje ca Firate.
4
Ndipo Davide anatenga apakavalo ace cikwi cimodzi mphambu mazana asanu ndi awiri, ndi oyenda pansi zikwi maku mi awiri; ndipo Davide anadula mitsita akavalo onse a magareta, koma anasunga a iwo akufikira magareta zana limodzi.
5
Ndipo pakufika Aaramu a ku Damasiko kudzathandiza Hadadezeri mfumu ya ku Zoba, Davide anakanthako Aaramu zikwi makumi awiri mphambu ziwiri.
6
Pamenepo Davide anaika maboma m'Aramu wa Damasiko, Ndipo Aaramu anasanduka anthu a Davide, nabwera nayo mitulo. Ndipo Yehova anamsunga Davide kuli konse anamukako.
7
Ndipo Davide anatenga zikopa zagolidi zinali ndi anyamata a Hadadezeri, nabwera nazo ku Yerusalemu.
8
Ndipo ku Beta ndi ku Berotai midzi ya Hadadezeri, mfumu Davide anatenga mikuwa yambiri ndithu.
9
Ndipo pamene Toi mfumu ya ku Hamati anamva kuti Davide adakantha khamu lonse la Hadadezeri,
10
Toi anatumiza mwana wace Joramu kwa mfumu Davide, kuti akamlankhule iye, ndi kumdalitsa, popeza anamenyana ndi Hadadezeri ndi kumkantha; pakuti pakati pa Hadadezeri ndi Toi panali nkhondo. Ndipo Joramu anabwera ndi zotengera zasiliva, ndi zotengera zagolidi, ndi zotengera zamkuwa.
11
Izi zomwe mfumu Davide anazipatula zikhale za Yehova, pamodzi ndi siliva ndi golidi anapatulako za amitundu onse adawagonjetsa;
12
za Aaramu, za Amoabu, za ana a Amoni, za Afilisti, za Amaleki, ndi zofunkha za Hadadezeri, mwana wa Rehobu mfumu ya ku Zoba.
13
Ndipo Davide anamveketsa dzina lace pamene anabwera uko adakantha Aaramu m'cigwa ca mcere, ndiwo anthu zikwi khumi mphambu zisanu ndi zitatu.
14
Ndipo anaika maboma m'Edomu; m'dziko lonse la Edomu anaika maboma, ndipo Aedomu onse anasanduka anthu a Davide. Ndipo Yehova anasunga Davide kuli konse anamukako.
15
Ndipo Davide anakhala mfumu ya Aisrayeli onse, Davide naweruza ndi cilungamo mirandu ya anthu onse.
16
Ndipo Yoabu mwana wa Zeruya anayang'anira ankhondo, ndi Josafati mwana wa Ahiludi anali wolemba mbiri,
17
ndi Zadoki mwana wa Ahitubi, ndi Ahimeleki mwana wa Abyatara anali ansembe, ndi Seraya anali mlembi.
18
Ndipo Benaya mwana wa Jehoyada anayang'anira Akereti ndi Apeleti. Ndipo ana a Davide anali nduna zace.
← Chapter 7
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 9 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24