bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
/
2 Samuel 9
2 Samuel 9
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
← Chapter 8
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 10 →
1
Ndipo Davide anati, Kodi atsalako wina wa nyumba ya Sauli, kuti ndimcitire cifundo cifukwa ca Jonatani?
2
Ndipo panali mnyamata wa m'nyumba ya Sauli dzina lace Ziba; ndipo anamuitana iye afike kwa Davide; ndi mfumuyo inanena naye, Iwe ndiwe Ziba kodi? Nati iye, Ndine mnyamata wanu ame.
3
Ndipo mfumu inati, Kodi atsalanso wina wa nyumba ya Sauli kuti ndimuonetsere cifundo ca Mulungu? Ziba nanena ndi mfumu, Aliponso mwana wa Jonatani wopunduka mapazi ace.
4
Ndipo mfumu inanena naye, Ali kuti iyeyo? Ziba nanena kwa mfumu, Onani ali m'nyumba ya Makiri, mwana vya Amiyeli ku Lodebara.
5
Pamenepo Davide anatumiza anthu nakatenga iye ku nyumba ya Makiri mwana wa Amiyeli ku Lodebara.
6
Ndipo Mefiboseti mwana wa Jonatani, mwana wa Sauli, anafika kwa Davide, nagwa nkhope yace pansi, namlambira. Ndipo Davide anati, Mefiboseti! Nayankha iye, Ndine mnyamata wanu.
7
Ndipo Davide ananena naye, Usaopa, pakuti zoonadi ndidzakucitira kukoma mtima cifukwa ca Jonatani atate wako; ndi minda yonse ya Sauli ndidzakubwezera, ndipo udzadya pa gome langa cikhalire.
8
Ndipo iye anamlambira, nati, Mnyamata wanu ndani, kuti mulikupenya garu wakufa monga ine.
9
Pomwepo mfumu inaitana Ziba, mnyamata wa Sauli, ninena naye, Za Sauli zonse ndi za nyumba yace yonse ndampatsa mwana wa mbuye wako.
10
Ndipo uzimlimira munda wace, iwe ndi ana ako ndi anyamata ako; nuzibwera nazo zipatso zace kuti mwana wa mbuye wako akhale ndi zakudya; koma Mefiboseti, mwana wa mbuye wako, adzadya pa gome langa masiku onse. Ndipo Ziba anali nao ana amuna khumi ndi asanu, ndi anyamata makumi awiri.
11
Pomwepo Ziba anati kwa mfumu, Monga mwa zonse mfumu mbuye wanga mulamulira mnyamata wanu, momwemo adzacita mnyamata wanu. Tsono Mefiboseti, anadya pa gome la Davide monga wina wa ana a mfumu.
12
Ndipo Mefiboseti anali ndi mwana wamwamuna wamng'ono, dzina lace ndiye Mika. Ndipo onse akukhala m'nyumba ya Ziba anali anyamata a Mefiboseti.
13
Comweco Mefiboseti anakhala ku Yerusalemu, pakuti anadya masiku onse ku gome la mfumu, ndipo anali wopunduka mapazi ace onse awiri.
← Chapter 8
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 10 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24