bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
/
Joshua 15
Joshua 15
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
← Chapter 14
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 16 →
1
Ndipo gawo la pfuko la ana a Yuda monga mwa mabanja ao linafikira malire a Edomu, ku cipululu ca Zini kumwera, ku malekezero a kumwera.
2
Ndi malire ao a kumwera, anayambira ku malekezero a Nyanja ya Mcere, ku nyondo yoloza kumwera;
3
naturuka kumwela kwa cikweza ca Akarabi, napitirira ku Zini, nakwera kumwera kwa Kadesi-Barinea, napitirira ku Hezironi, nakwera ku Adara, nazungulira ku Karika;
4
napitirira ku Azimoni, naturuka ku mtsinje wa Aigupto; ndi malekezero a malirewa anali ku Nyanja Yaikuru; awa ndi malire anu a kumwera.
5
Ndi malire a kum'mawa ndiwo Nyanja ya Mcere, mpaka mathiriro ace a Yordano. Ndi malire a kumpoto anayambira nyondo ya nyanja ku mathiriro a Yordano;
6
nakwera malire kumka ku Beti-hogila, napitirira kumpoto kwa Beti-araba; nakwera malire kumka ku mwala wa Bohani mwana wa Rubeni;
7
nakwera malire kumka ku Dibiri, kucokera ku cigwa ca Akori, ndi kumpoto kupenyera Giligala ndiko kundunji kwa cikweza ca Adumi, ndiko kumwela kwa mtsinje; napitirira malire kumka ku madzi a Enisemesi, ndi maturukiro ace anali ku Eni-rogeli;
8
nakwera malire kumka ku cigwa ca mwana wa Hinomu, kumbali kwa Ayebusi, kumwela, ndiko Yerusalemu; nakwera malire kumka kumwamba kwa phiri lokhala patsogolo pa cigwa ca Hinomu kumadzulo, ndilo ku mathero ace a cigwa ca Refai kumpoto,
9
Ndipo analemba malire kuyambira pamwamba pa phiri mpaka citsime ca madzi ca Nefitoa, naturukira malire ku midzi ya phiri la Efroni; ndipo analemba malire kumka ku Baala, ndiwo Kiriyati-Yearimu.
10
Ndipo malire anazungulira kuyambira ku Baala kumka kumadzulo, ku phiri la Seiri, napitirira kumbali kwa phiri la Yearimu kumpoto, ndilo Kesaloni, natsikira ku Beti-semesi, napitirira ku Timina;
11
naturuka malire kumka ku mbali ya Ekroni kumpoto; ndipo analemba malire kumka ku Sikeroni, napitirira ku phiri la Baala, naturuka ku Yabindi; ndipo maturukiro a malire anali kunyanja.
12
Ndi malire a kumadzulo anali ku Nyanja Yaikuru ndiwo malire ace. Awa ndi malire a ana a Yuda pozungulira monga mwa mabanja ao.
13
Koma Yoswa anampatsa Kalebe mwana wa Yefune gawo mwa ana a Yuda, monga Yehova adamlamulira, ndiwo mudzi wa Ariba, ndiye atate wa Anaki, ndiwo Hebroni.
14
Ndipo Kalebe anaingitsako ana amuna atatu a Anaki, ndiwo Sesai, ndi Ahimani, ndi Talimai, ana a Anaki.
15
Nakwera komweko kumka kwa nzika za Dibiri; koma kale dzina la Dibiri ndilo Kiriyati-Seferi.
16
Ndipo Kalebe anati, iye amene akantha Kiriyati-Seferi, naulanda, yemweyo ndidzampatsa Akisa mwana wanga akhale mkazi wace.
17
Ndipo Otiniyeli mwana wa Kenazi, mbale wace wa Kalebe, anaulanda; ndipo anampatsa Akisa mwana wace akhale mkazi wace.
18
Ndipo kunali, m'mene anamdzera, anamkangamiza mwamuna wace kuti apemphe atate wace ampatse munda; ndipo anatsika pa buru; pamenepo Kalebe ananena naye, Ufunanji?
19
Nati iye, Mundipatse dalitso; popeza mwandipatsa dziko la kumwela, ndipatseninso zitsime za madzi. Pamenepo anampatsa zitsime za kumtunda, ndi zitsime za kunsi.
20
Ici ndi colowa ca pfuko la ana a Yuda monga mwa mabanja ao.
21
Ndipo midzi ya ku malekezero a pfuko la ana a Yuda ku malire a Edomu, kumwela ndiwo, Kabizeeli ndi Ederi, ndi Yaguri;
22
ndi Kina ndi Dimona, ndi Adada;
23
ndi Kedesi, ndi Hazori, ndi ltinani;
24
Zifi ndi Telemu ndi Bealoti;
25
ndi Hazorihadata, ndi Kerioti-hezirondi, ndiwo Hazori;
26
Amamu ndi Sema ndi Moloda;
27
ndi Hazara-gada, ndi Hesimoni, ndi Beti-peleti;
28
ndi Hazara-suala, ndi Beereseba, ndi Bizioti;
29
Baala, ndi lyimu, ndi Ezemu;
30
ndi Elitoladi, ndi Kesili ndi Horima;
31
ndi Zikilaga, ndi Madimana ndi Sanasana;
32
ndi Lebaoti, ndi Siliimu, ndi Aini ndi Rimoni; midzi yonse ndiyo makumi awiri kudza isanu ndi inai; pamodzi ndi miraga yao.
33
Ku cigwa, Esitaoli, ndi Zora ndi Asina;
34
ndi Zoona, ndi Eniganimu, Tapua, ndi Enamu;
35
Yarimutu, ndi Adulamu, Soko, ndi Azeka;
36
ndi Saaraimu, ndi Aditaimu, ndi Gedera, ndi Gederotaimu; midzi khumi ndi inai pamodzi ndi miraga yao.
37
Zenani, ndi Hadasa, ndi Migidala-gadi;
38
ndi Dilani, ndi Mizipe, ndi Yokiteeli;
39
Lakisi ndi Bozikatu ndi Egiloni;
40
ndi Kaboni, ndi Lamasi, ndi, Kitilisi;
41
ndi Gaderotu, Beti-dagoni, ndi Naama, ndi Makeda; midzi khumi ndi isanu ndi umodzi pamodzi ndi miraga yao.
42
Libina ndi Eteri ndi Asana;
43
ndi Ifita ndi Asina ndi Nezibi;
44
ndi Kehila ndi Akisibu, ndi Maresa; midzi isanu ndi inai pamodzi ndi miraga yao.
45
Ekroni pamodzi ndi midzi yace ndi miraga yao;
46
kuyambira ku Ekroni mpaka kunyanja, yonse ya ku mbali ya Asidodo, pamodzi ndi miraga yao.
47
Asidodo, midzi yace ndi miraga yace; Gaza, midzi yace ndi miraga yace; mpaka mtsinje wa Aigupto, ndi nyanja yaikuru ndi malire ace.
48
Ndi kumapiri Samiri, ndi Yatiri, om Soko;
49
ndi Dana, ndi Kiriyatisana, ndiwo Dibiri;
50
ndi Anabi, ndi Esitemo, ndi Animu;
51
ndi Goseni, ndi Holoni, ndi Gilo; midzi khumi ndi umodzi pamodzi ndi miraga yao.
52
Arabu, ndi Duma, ndi Esana;
53
ndi Yanimu, ndi Beti-tapua, ndi Apeka;
54
ndi Humita, ndi Kiriyatiariba, ndiwo Hebroni, ndi Ziori; midzi isanu ndi inai pamodzi ndi miraga yao.
55
Maoni, Karimeli, ndi Zifu, ndi Yuta;
56
ndi Yesireeli, ndi Yokideamu, ndi Zoona;
57
Kaini, Gibea ndi Timina; midzi khumi pamodzi ndi miraga yao.
58
Haluli, Beti-zuru, ndi Gedori,
59
ndi Maaratu, ndi Bete-anotu, ndi Elitekoni; midzi isanu ndi umodzi pamodzi ndi miraga yao.
60
Kiriyata-Baala, ndiwo KiriyatiYearimu ndi Raba; midzi iwiri pamodzi ndi miraga yao.
61
M'cipululu, Beti-araba, Midini, ndi Sekaka;
62
ndi Nibisani, ndi Mudzi wa Mcere, ndi En-gedi; midzi isanu ndi umodzi pamodzi ndi miraga yao.
63
Koma ana a Yuda sanakhoza kuingitsa Ayebusi, nzika za Yerusalemu: m'mwemo Ayebusi anakhala pamodzi ndi ana a Yuda, ku Yerusalemu, mpaka lero lino.
← Chapter 14
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 16 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24