bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
/
Joshua 20
Joshua 20
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
← Chapter 19
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 21 →
1
Ndipo Yehova anati kwa Yoswa,
2
Nena ndi ana a Israyeli ndi kuti, Mudziikire midzi yopulumukirako, monga ndinanena kwa inu mwa dzanja la Mose,
3
kuti athawireko wakupha munthu osamupha dala, osadziwa; ndipo idzakhalira inu yopulumukirako, kumpulumuka wolipsa mwazi.
4
Munthu akathawira umodzi wa midzi iyi, aziima polowera pa cipata ca mudziwo, nafotokozere mlandu wace m'makutu a akuru a mudziwo; pamenepo azimlandira kumudzi kwao, ndi kumpatsa malo, kuti akhale pakati pao.
5
Ndipo akamlondola wolipsa mwazi, asampereke m'dzanja lace wakupha mnzaceyo; pakuti anakantha mnansi wace mosadziwa, osamuda kale.
6
Ndipo azikhala m'mudzimo mpaka adzaima pamaso pa msonkhano anene mlandu wace, mpaka atafa mkulu wansembe wa m'masiku omwewo; pamenepo wakupha mnzace azibwerera ndi kufika kumudzi kwace, ndi nyumba yace, kumudzi kumene adathawako.
7
Ndipo anapatula Kedesi m'Galileya ku mapiri a Nafitali, ndi Sekemu ku mapiri a Efraimu, ndi mudzi wa Ariba ndiwo Hebroni ku mapiri a Yuda.
8
Ndipo tsidya lija la Yordano kum'mawa kwa Yeriko, anaika Bezeri m'cipululu, kucidikha, wa pfuko la Rubeni, ndi Ramoti m'Gileadi wa ofuko la Gadi, ndi Golani m'Basana wa pfuko la Manase.
9
Iyi ndi midzi yoikidwira ana onse a Israyeli, ndi mlendo wakukhala pakati pao, kuti athawireko ali yense wakupha munthu, ndi kuti asafe ndi dzanja la wolipsa mwazi, asanaime pamaso pa msonkhano.
← Chapter 19
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 21 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24