bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
/
Joshua 19
Joshua 19
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
← Chapter 18
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 20 →
1
Ndipo maere aciwiri anamturukira Simeoni, pfuko la ana a Simeoni monga mwa mabanja ao; ndi colowa cao cinali pakati pa colowa ca ana a Yuda.
2
Ndipo anali naco colowa cao Beeri-seba, kapena Seba, ndi Molada;
3
ndi Hazarasuala, ndi Bala, ndi Ezemu;
4
ndi Elitoladi, ndi Betuli, ndi Horimu;
5
ndi Zikilaga, ndi Beti-malikabotu, ndi Hazari-susa:
6
ndi Beti-lebaotu, ndi Saruheni; midzi khumi ndi itatu ndi miraga yao;
7
Aini, Rimoni ndi Eteri ndi Asana; midzi inai ndi miraga yao;
8
ndi miraga yonse yozungulira midzi iyi mpaka Baalata-beeri ndiwo Rama kumwera. Ndico colowa ca pfuko la ana a Simeoni, monga mwa mabanja ao.
9
M'gawo la ana a Yuda muli colowa ca ana a Simeoni; popeza gawo la ana a Yuda linawacurukira; cifukwa cace ana a Simeoni anali naco colowa pakati pa colowa coo.
10
Ndipo maere acitatu anakwecera ana a Zebuloni monga mwa mabanja ao; ndi malire a colowa cao anafikira ku Saridi;
11
nakwera malire ao kumka kumadzulo ndi ku Marala nafikira ku Dabeseti, nafikira ku mtsinje wa patsogolo pa Yokineamu;
12
ndi kucokera ku Saridi anazungulira kumka kum'mawa kumaturukira dzuwa, mpaka malire a Kisilotu-tabori; naturuka kumka ku Daberati, nakwera ku Yafia;
13
ndi pocoka pamenepo anapitirira kumka kum'mawa ku Gati-heferi, ku Etikazini; naturuka ku Remoni umene ulembedwa mpaka ku Nea,
14
nauzungulira malire kumpoto, kumka ku Hanatoni; ndi maturukiro ace anali ku cigwa ca Ifita-eli;
15
ndi Kata, ndi Nahalala ndi Simironi, ndi Idala ndi Betelehemu: midzi khumi ndi iwiri ndi miraga yao.
16
Ici ndi colowa ca ana a Zebuloni monga mwa mabanja ao, midzi iyi ndi miraga yao.
17
Maere acinai anamturukira Isakara, kunena za ana a Isakara monga mwa mabanja ao.
18
Ndi malire ao anali ku Yezireeli, ndi Kesulotu, ndi Sunemu;
19
ndi Hafaraimu, ndi Sioni, ndi Anaharati;
20
ndi Rabiti ndi Kisioni, ndi Ebezi;
21
ndi Remeti ndi Eni-ganaimu ndi Eni-hada, ndi Beti-Pazezi;
22
ndi malire anafikira ku Tabori, ndi Sahazuma, ndi Betesemesi; ndi maturukiro a malire ao anali ku Yordano; midzi khumi ndi isanu ndi umodzi ndi miraga yao.
23
Ici ndi colowa ca pfuko la ana a Isakara, monga mwa mabanja ao, midzi ndi miraga yao.
24
Ndipo maece acisanu analiturukira pfuko la ana a Aseri monga mwa mabanja ao.
25
Ndi malire ao ndiwo Helikati, ndi Hali, ndi Beteni ndi Akisafu;
26
ndi Alameleki, ndi Amadi, ndi Misali; nafikira ku Karimeli kumadzulo ndi ku Sihorilibinati;
27
nazungulira koturukira dzuwa ku Beti-dagoni, nafikira ku Zebuloni ndi ku cigwa ca Ifita-eli, kumpoto ku Beti-emeki, ndi Nehieli; naturukira ku Kabulu kulamanzere,
28
ndi Ebroni, ndi Rehobo, ndi Hamoni, ndi Kana, mpaka ku Sidoni wamkuru;
29
nazungulira malice kumka ku Rama, ndi ku mudzi wa linga la Turo; nazungulira malire kumka ku Hosa; ndi maturukiro ace anali kunyanja, kucokera ku Hebeli mpaka ku Akizibu;
30
Uma womwe ndi Afeki, ndi Rehobo; midzi makumi awiri mphambu iwiri ndi miraga yao,
31
Ici ndi colowa ca pfuko la ana a Aseri monga mwa mabanja ao, midzi iyi ndi miragayao.
32
Maere acisanu ndi cimodzi anaturukira ana a Nafitali, ana a Nafitali monga mwa mabanja ao.
33
Ndipo malire ao anayambira ku Helefi, ku thundu wa ku Zaanani, ndi Adaminekebi, ndi Yabineeli, mpaka ku Lakumu; ndi maturukiro ace anali ku Yordano;
34
nazungulira malire kumka kumadzulo ku Azinotu-tabori, naturukira komweko kumka ku Hukoku; nafikira ku Zebuloni kumwera, nafikira ku Aseri kumadzulo, ndi ku Yuda pa Yordano kum'mawa.
35
Ndipo midzi yamalinga ndiyo Zidimu, Zeri, ndi Hamati, Rakati, ndi Kinereti;
36
ndi Adama, ndi Rama, ndi Hazori;
37
ndi Kedesi, ndi Edrei, ndi Eni-hazori;
38
ndi Ironi, ndi Migidala-eli, Horemu, ndi Betianati, ndi Beti-semesi; midzi khumi ndi isanu ndi inai, ndi miraga yao.
39
Ici ndi colowa ca pfuko la ana a Nafitali, monga mwa mabanja ao, midzi ndi miraga yao.
40
Maere acisanu ndi ciwiri anaturukira pfuko la ana a Dani, monga mwa mabanja ao.
41
Ndipo malire a colowa cao anali Zora, ndi Esitaoli ndi Iri-semesi;
42
Saalabini, ndi Aijaloni ndi ltila;
43
ndi Eloni ndi Timna ndi Ekroni;
44
ndi Eliteke, ndi Gibetoni, ndi Baalati;
45
ndi Yehudi, ndi Bene-beraki, ndi Gatirimoni;
46
ndi Me-jarikoni, ndi Rakoni, ndi malire pandunji pajapo.
47
Koma malire a ana a Dani anaturuka kupitirira iwowa; pakuti ana a Dani anakwera nathira nkhondo ku Lesemu, naulanda naukantha ndi lupanga lakuthwa, naulandira, nakhala m'mwemo, naucha Lesemu, Dani; ndilo dzina la Dani atate wao.
48
Ici ndi colowa ca pfuko la ana a Dani, monga mwa mabanja ao, midzi iyi ndi miraga yao.
49
Ndipo atatha kuligawa dziko likhale colowa cao monga mwa malire ace, ana a Israyeli anapatsa Yoswa mwana wa Nuni colowa pakati pao;
50
monga mwa lamulo la Yehova anampatsa mudzi umene anawapempha, ndiwo Timinatisera, ku mapiri a Efraimu; ndipo anamangamudziwonakhala m'mwemo.
51
Izi ndizo zolowa anazigawa Eleazare wansembe, ndi Yoswa mwana wa Nuni, ndi akulu a nyumba za atate a mapfuko a ana a Israyeli, zikhale zao zao, ndi kulota maere ku Silo pamaso pa Yehova ku khomo la cihema cokomanako. Momwemo anatha kuligawa dziko.
← Chapter 18
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 20 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24