bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
/
Numbers 13
Numbers 13
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
← Chapter 12
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 14 →
1
Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,
2
Udzitumire amuna, kuti azonde dziko la Kanani, limene ndirikupatsa ana a Israyeli; utumize munthu mmodzi wa pfuko liri lonse la makolo ao, yense kalonga pakati pa anzace.
3
Ndipo Mose anawatumiza kucokera ku cipululu ca Parana monga mwa mau a Yehova; amuna onsewa ndiwo akuru a ana a Israyeli.
4
Maina ao ndi awa: wa pfuko la Rubeni, Samuwa mwana wa Zakuri.
5
Wa pfuko la Simeoni, Safati mwana wa Hori.
6
Wa pfuko la Yuda, Kalebi mwana wa Yefune.
7
Wa pfuko la Isakara, Igali mwana wa Yosefe.
8
Wa pfuko la Efraimu, Hoseya mwana wa Nuni.
9
Wa pfuko la Benjamini, Paliti mwana wa Rafu.
10
Wa pfuko la Zebuloni, Gadiyeli mwana wa Sodi.
11
Wa pfuko la Yosefe, wa pfuko la Manase, Gadi mwana wa Susi.
12
Wa pfuko la Dani, Amiyeli mwana wa Gemali.
13
Wa pfuko la Aseri, Setri mwana wa Mikayeli.
14
Wa pfuko la Nafitali, Nabi mwana wa Vopisi.
15
Wa pfuko la Gadi, Geyuelimwana wa Maki.
16
Awandi maina a amunawo Mose anawatumira azonde dziko. Ndipo Mose anamucha Hoseya mwana wa Nuni Yoswa.
17
Potero Mose anawatuma azonde dziko la Kanani, nanena nao, Kwerani uko kumwela, nimukwere kumapiri;
18
mukaone dziko umo liriri; ndi anthu akukhala m'mwemo, ngati ali amphamvu kapena ofok a, ngati acepa kapena acuruka;
19
ndi umo liriri dzikoli lokhalamo iwo, ngati lokoma, kapena loipa; ndi umo iriri midziyo akhalamo iwo, ngati akhala poyera kapena m'malinga;
20
ndi umo iriri nthaka, ngati yopatsa, kapena yosuka, ngati pali mitengo, kapena palibe, Ndipo limbikani mtima, nimubwere nazo zipatso za m'dzikomo. Koma nyengoyi ndiyo nyengo yoyamba kupsa mphesa.
21
Pamenepo anakwerako, nazonda dziko kuyambira cipululu ca Zini kufikira Rehobo, polowa ku Hamati.
22
Ndipo anakwera njira ya kumwela nafika ku Hebroni; ndi apa panali Ahimani, Sesai, ndi Talmai, ana a Anaki. (Koma atamanga Hebroni zaka zisanu ndi ziwiri ndipo anamanga Zoani m'Aigupto.)
23
Ndipo anadza ku cigwa ca Esikolo, nacekako tsango limodzi la mphesa, nalisenza awiri mopika; anabwera nazonso makangaza ndi nkhuyu.
24
Malowa anawacha cigwa ca Esikolo, cifukwa ca tsangolo ana a lsrayeli analicekako.
25
Pamenepo anabwerera atazonda dziko, atatha masiku makumi anai.
26
Ndipo anamuka, nadza kwa Mose, ndi Aroni, ndi khamu lonse la ana a Israyeli, ku cipululu ca Parana ku Kadesi; ndipo anabwezera mau iwowa, ndi khamu lonse, nawaonetsa zipatso za dzikoli.
27
Ndipo anafotokozera, nati, Tinakafika ku dziko limene munatitumirako, ndilo ndithu a moyenda mkaka ndi uci ngati madzi; ndi zipatso zace siizi.
28
Komatu anthu okhala m'dzikomo ngamphamvu; ndi midziyo nja malinga, yaikuru ndithu: ndipo tinaonakonso ana a Anaki.
29
Aamaleke akhala m'dziko la kumwera; ndi Ahiti, ndi Ayebusi, ndi Aamori, akhala ku mapiri, ndi Akanani akhala kunyanja, ndi m'mphepete mwa Yordano.
30
Koma Kalebi anatontholetsa anthu pamaso pa Mose, nati, Tikwere ndithu ndi kulilandira lathu lathu; popeza tikhozadi kucita kumene.
31
Koma anthu adakwera nayewo anati, Sitikhoza kuwakwerera anthuwo; popeza atiposa mphamvu,
32
Ndipo anaipsira ana a Israyeli mbiri ya dziko adalizonda, nati, Dzikoli tapitamo kulizonda, ndilo dziko lakutheramo anthu okhalamo; ndi anthu onse tidaona pakati pace ndiwo anthu atali misinkhu.
33
Tinaonakonso Anefili, ana a Anaki, obadwa ndi Anefili; ndipo tinaoneka m'maso mwathu ngati zinsidzi; momwemonso tinaoneka m'maso mwao.
← Chapter 12
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 14 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36