bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
/
Numbers 25
Numbers 25
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
← Chapter 24
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 26 →
1
Ndipo Israyeli anakhala m'Sitimu, ndipo anthu anayamba kucita cigololo ndi ana akazi a Moabu;
2
popeza anaitana anthuwo adze ku nsembe za milungu yao; ndipo anthuwo anadya, nagwadira milungu yao.
3
Pamene Israyeli anaphatikana ndi Baala Peori, Mulungu anapsa mtima pa Israyeli.
4
Ndipo Yehova anati kwa Mose, Gwira akuru onse a anthu nuwapacikire Yehova, pali dzuwa poyera, kuti mkwiyo waukali wa Yehova ucoke kwa Israyeli.
5
Ndipo Mose anati kwa oweruza a Israyeli, Iphani, yense anthu ace adapatikanawo ndi Baala-Peori.
6
Ndipo, taonani, anadza wina wa ana a Israyeli, nabwera naye mkazi Mmidyani kudza naye kwa abale ace, pamaso pa Mose, ndi pamaso pa khamu lonse la ana a Israyeli, pakulira iwo pa khomo la cihema cokomanako.
7
Pamene Pinehasi mwana wa Eleazara, mwana wa Aroni wansembe, anaciona, anauka pakati pa khamu, natenga nthungo m'dzanja lace;
8
natsata munthu M-israyeli m'hema, nawamoza onse awiri, munthu M-israyeli ndi mkaziyo m'mimba mwace. Pamenepo mliri unaletseka kwa ana a Israyeli.
9
Ndipo akufa nao mliri ndiwo zikwi makumi awiri ndi zinai.
10
Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,
11
Pinehasi mwana wa Eleazara, mwana wa Aroni wansembe, wabweza kuzaza kwanga pa ana a Israyeli, popeza anacita nsanje ndi nsanje yanga pakati pao, kotero kuti sindinawatha ana a Israyeli m'nsanje yanga.
12
Cifukwa cace nena, Taonani, ndimpatsa iye pangano langa la mtendere;
13
ndipo lidzakhala kwa iye, ndi kwa mbeu zace zakumtsata pangano la unsembe wosatha, popeza anacita nsanje cifukwa ca Mulungu wace, anawacitira ana a Israyeli cowatetezera.
14
Koma dzina la M-israyeli adamuphayo, ndiye amene adamupha pamodzi ndi mkazi Mmidyani, ndiye Zimiri mwana wa Salu, mfumu ya nyumba va makolo mwa Asimeoni.
15
Ndi dzina la mkazi Mmidyani adamuphayo ndiye Kozibi mwana wamkazi wa Zuri; ndiye mkuru wa anthu a nyumba ya makolo m'Midyani.
16
Ndipo Yehova ananena ndi Mose, ndi kuti,
17
Sautsa Amidyani ndi kuwakantha;
18
popeza akusautsani ndi manyengo ao amene anakunyengani nao; m'cija ca Peori, ndi ca Kozibi, mwana wamkazi wa kalonga wa ku Midyani, mlongo wao, amene adamupha tsiku la mliri, m'cija ca Peori.
← Chapter 24
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 26 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36