bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
/
Numbers 17
Numbers 17
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
← Chapter 16
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 18 →
1
Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,
2
Nena ndi ana a Israyeli, nulandire kwa yense ndodo, banja liri onse la makolo ndodo imodzi, mafuko ao onse monga mwa mabanja a makolo ao azipereka ndodo, zikhale khumi ndi ziwiri; nulembe dzina la yense pa ndodo yace.
3
Ndipo ulembe dzina la Aroni pa ndodo ya Levi; pakuti pakhale ndodo imodzi pa mkuru yense wa nyumba za makolo ao.
4
Ndipo uziike m'cihema cokomanako, cakuno ca mboni, kumene ndikomana ndi inu.
5
Ndipo kudzali, kuti ndodo ya munthu ndimsankheyo, idzaphuka; ndipo ndidzadziletsera madandaulo a ana a Israyeli amene adandaula nao pa inu.
6
Ndipo Mose ananena ndi ana a Israyeli, ndipo akalonga ao onse anapereka, yense ndodo imodzi, monga mwa mabanja a makolo ao, ndodo khumi ndi ziwiri; ndi ndodo ya Aroni inakhala pakati pa ndodo zao.
7
Ndipo Mose anaika ndodozo pamaso pa Yehova m'cihema ca mboni.
8
Ndipo kunali m'mawa mwace, kuti Mose analowa m'cihema ca mboni; ndipo taonani, ndodo ya Aroni, ya pa banja la Levi, inaphuka, nionetsa timaani, nicita maluwa, nipatsa akatungurume.
9
Ndipo Mose anaturutsa ndodo zonse kuzicotsa pamaso pa Yehova, azione ana onse a Israyeli; ndipo anapenya, natenga yense ndodo yace.
10
Ndipo Yehova anati kwa Mose, Bweza ndodo ya Aroni kulika cakuno ca mboni, isungike ikhale cizindikilo ca pa ana opikisana; kuti unelitsirizire madandaulo ao, kuti ungafe.
11
Ndipo Mose anacita monga Yehova adamuuza, momwemo anacita.
12
Pamenepo ana a Israyeli ananena ndi Mose, nati, Taonani, tikufa, tionongeka, tionongeka tonse.
13
Yense wakuyandikiza kacisi wa Yehova amwalira; kodi tidzatha nkufa?
← Chapter 16
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 18 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36